Masomphenya operekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Hiram, Ohio, Febuluwale 16, 1832. Poyamba zolemba za masomphenya awa, mbiri ya Joseph Smith ikunena: “Pa kubwelera kwanga kuchokera ku msonkhano wa Amherst, ndidayambiranso kumasulira Malemba. Kuchokera ku mavumbulutso akale omwe adalandiridwa, zidali zoonekeratu kuti mfundo zambiri zofunika zokhudza chipulumutso cha munthu zidachotsedwa mu Baibulo, kapena zidatayika lisadasonkhanitsidwe. Zidaoneka zodziwikiratu kuchokera ku choonadi chimene chidatsala, kuti ngati Mulungu adapereka mphotho kwa aliyense mogwirizana ndi ntchito zochitidwa m’thupi, liwu lakuti ‘Kumwamba,’ monga kudakonzedwa kukhala nyumba yamuyaya ya Oyera mtima, kukuyenera kuphatikizapo maufumu ambiri kuposa umodzi. Motero, … pamene tinkamasulira Uthenga Wabwino wa Yohane Woyera, ineyo ndi Mkulu Rigdon tidaona masomphenya otsatirawa.” Pa nthawi imene masomphenyawa ankaperekedwa, Mneneriyu ankamasulira Yohane 5:29.