Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 118


Gawo 118

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Far West, Missouri, Julaye 8, 1838, poyankha ku pembedzero, “Tionetseni chifuniro chanu, O Ambuye, chokhudza Khumi ndi Awiriwo”.

1–3, Ambuye adzasamalira mabanja a Khumi ndi Awiri; 4–6, Mipata mu anthu Khumi ndi Awiri yadzazidwa.

Indetu, akutero Ambuye: lolani msonkhano uchitike mwachangu; lolani Khumi ndi Awiri akhazikitsidwe; ndipo lolani amuna asankhidwe kukwaniritsa m’malo mwa iwo amene agwa.

Lolani mtumiki wanga Thomas akhale kwa kanthawi mu dziko la Ziyoni, kuti asindikize mawu anga.

Lolani otsalawo apitilize kulalika kuchokera ku ola limelo, ndipo ngati iwo adzachita izi mu kudzichepetsa konse kwa mtima, mu chifatso ndi kudzichepetsa, ndi kupilira, ine, Ambuye, ndipereka kwa iwo lonjezo kuti ndidzasamalira mabanja awo; ndipo khomo lathandizo lidzatsegulidwa kwa iwo, kuyambira tsopano.

Ndipo masika akudzawa aloleni iwo achoke kupita ku madzi aakulu, ndipo kumeneko akalengeze uthenga wanga wabwino, chidzalo chake, ndi kuchitira umboni wa dzina langa.

Aloleni iwo awasiye oyera mtima anga mu mzinda wa Far West, patsiku la makumi awiri ndi zisanu kudza limodzi la Epulo winayo, pa malo omangira nyumba yanga, atero Ambuye.

Lolani mtumiki wanga John Taylor, ndiponso mtumiki wanga John E. Page, ndiponso mtumiki wanga Wilford Woodruff, ndiponso mtumiki wanga Willard Richards, asankhidwe kudzadzitsa malo a iwo amene agwa, ndipo adzadziwitsidwe mwandondomeko za kusankhidwa kwawo.