Gawo 18
Vumbulutso kwa Joseph Smith Mneneri, Oliver Cowdery, ndi David Whitmer, loperekedwa ku Fayette, New York, Juni 1829. Molingana ndi Mneneri, vumbulutso limeneli lidazindikiritsa “kuitanidwa kwa atumwi khumi ndi awiri m’masiku otsiriza ano, ndiponso malangizo okhudza kumanga Mpingo.”
1–5, Malemba amaonetsa m’mene angamangire Mpingo; 6–8, Dziko lapansi likucha mu kusaweruzika; 9–16, Mtengo wa miyoyo ndi waukulu; 17–25, Kuti alandire chipulumutso, anthu akuyenera kudzitengera pa iwo eni dzina la Khristu; 26–36, Maitanidwe ndi ntchito ya Khumi ndi Awiri zavumbulutsidwa; 37–39, Oliver Cowdery ndi David Whitmer akuyenera kufunafuna Khumi ndi Awiri; 40–47, Kuti alandire chipulumutso, anthu akuyenera kulapa, kubatizidwa, ndi kusunga malamulo.
1 Tsopano, taona, chifukwa cha chinthu chimene iwe, mtumiki wanga Oliver Cowdery, wakhumba kudziwa kwa ine, ndikupereka kwa iwe mawu awa:
2 Taona, ndaonetsa kwa iwe, mwa Mzimu wanga mu zochitika zambiri, kuti zinthu zimene iwe udalemba ndi zoona; kotero ukudziwa kuti ndi zoona.
3 Ndipo ngati iwe ukudziwa kuti ndi zoona, taona, ndikupatsa iwe lamulo, kuti udzidalira pa zinthu zimene zalembedwa;
4 Pakuti m’menemo mudalembedwa zinthu zonse zokhudza maziko a mpingo wanga, uthenga wanga wabwino, ndi thanthwe langa.
5 Kotero, ngati udzamanga mpingo wanga, pa maziko a uthenga wanga wabwino ndi thanthwe langa, zipata za gahena sizidzapambana motsutsana nawe.
6 Taona, dziko lapansi likucha mu kusaweruzika; ndipo zikuyenera kukhala kuti ana a anthu autsidwa m’kulapa, onse Amitundu ndiponso nyumba ya Israeli.
7 Kotero, monga momwe udabatizidwira ndi manja a mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., molingana ndi izo zimene ndamulamula iye, iye wakwanitsa kuchita chinthu chimene ine ndidamulamula.
8 Ndipo tsopano, usadabwe kuti ndamuitana iye ku cholinga changa, chimene cholingacho chikudziwika mwa ine; kotero, ngati iye adzakhala wolimbikira mu kusunga malamulo anga iye adzadalitsidwa ku moyo wosatha; ndipo dzina lake ndi Joseph.
9 Ndipo tsopano, Oliver Cowdery, ndikuyankhula kwa iwe, ndiponso kwa David Whitmer, mwa njira ya lamulo; pakuti, taonani, ine ndikulamula anthu onse kulikonse kuti alape, ndipo ine ndikuyankhula kwa inu, ngakhale monga kwa Paulo mtumwi wanga, pakuti inu mwaitanidwa ngakhale ndi maitanidwe omwewo amene iye adaitanidwa nawo.
10 Kumbukirani kuti mtengo wa miyoyo ndi waukulu pamaso pa Mulungu;
11 Pakuti, taonani, Ambuye Muwomboli wanu adazunzika imfa mu thupi; kotero adamva zowawa za anthu onse, kuti anthu onse akathe kulapa ndi kubwera kwa Iye.
12 Ndipo Iye adaukanso kwa akufa, kuti akathe kubweretsa anthu onse kwa iye, pa zikhalidwe za kulapa.
13 Ndipo chimwemwe chake ndi chachikulu bwanji mwa munthu amene walapa!
14 Kotero, inu mwaitanidwa kuti mufuule kulapa kwa anthu awa.
15 Ndipo ngati zitakhala kuti inu mugwire ntchito masiku anu onse mu kufuula kulapa kwa anthu awa, ndi kubweretsa, olo utakhale moyo umodzi kwa ine, chimwemwe chanu chidzakhala chachikulu bwanji pamodzi ndi iye mu ufumu wa Atate anga!
16 Ndipo tsopano, ngati chimwemwe chanu chidzakhala chachikulu ndi moyo umodzi umene mwandibweretsela kwa ine mu ufumu wa Atate anga, chimwemwe chanu chidzakhala chachikulu bwanji ngati mudzabweretsa miyoyo yambiri kwa ine!
17 Taonani, muli nawo uthenga wanga pamaso panu, ndi thanthwe langa, ndi chipulumutso changa.
18 Pemphani Atate mu dzina langa mu chikhulupiliro, kukhulupilira kuti mudzalandira, ndipo mudzakhala ndi Mzimu Woyera, umene umaonetsa zinthu zonse zimene zili zoyenera kwa ana a anthu.
19 Ndipo ngati mulibe chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi, simungathe kuchita kanthu.
20 Musalimbane ndikutsutsana ndi mpingo uliwonse, kupatula iwo utakhala mpingo wa mdyerekezi.
21 Tengani pa inu dzina la Khristu, ndipo yankhulani choonadi modziletsa.
22 Ndipo pamene ambiri alapa ndi kubatizidwa m’dzina langa, limene ndi Yesu Khristu, ndi kupilira mpaka kumapeto, yemweyo adzapulumutsidwa.
23 Taonani, Yesu Khristu ndi dzina limene laperekedwa ndi Atate, ndipo palibe dzina lina loperekedwa limene munthu angapulumutsidwe nalo;
24 Kotero, anthu onse akuyenera kutenga pa iwo dzina limene lapatsidwa ndi Atate, pakuti mu dzina limenelo iwo adzatchedwa pa tsiku lomaliza;
25 Kotero, ngati iwo sakudziwa dzina lomwe akutchedwa nalo, iwo sangakhale ndi malo mu ufumu wa Atate anga.
26 Ndipo tsopano, taonani, pali ena amene aitanidwa kuti alengeze uthenga wanga, kwa onse Amitundu ndi kwa Ayuda;
27 Inde, ngakhale khumi ndi awiri; ndipo Khumi ndi Awiriwo adzakhala ophunzira anga, ndipo iwo adzatenga pa iwo dzina langa; ndipo khumi ndi awiriwo ndi iwo amene adzakhumba kutenga pa iwo dzina langa ndi cholinga chonse cha mtima.
28 Ndipo ngati iwo akhumba kutenga pa iwo dzina langa ndi cholinga chonse cha mtima, iwo aitanidwa kupita ku dziko lapansi lonse kukalalikira uthenga wanga kwa cholengedwa chilichonse.
29 Ndipo iwo ali iwo amene adzodzedwa ndi ine kukabatiza mu dzina langa, molingana ndi izo zimene zalembedwa;
30 Ndipo inu muli nazo zimene zalembedwa patsogolo panu; kotero, mukuyenera kuchita ichi molingana ndi mawu amene alembedwawo.
31 Ndipo tsopano ndikuyankhula kwa inu, khumi ndi Awiri—Taonani, chisomo changa chili chokwanira kwa inu; mukuyenera kuyenda moongoka pamaso panga, ndipo musachimwe.
32 Ndipo taonani, inu ndinu amene mudadzodzedwa ndi ine kukadzodza ansembe ndi aphunzitsi; kukalengeza uthenga wanga wabwino, molingana ndi mphamvu ya Mzimu Woyera umene uli mwa inu, ndi molingana ndi maitanidwe ndi mphatso za Mulungu kwa anthu;
33 Ndipo ine, Yesu Khristu, Ambuye wanu ndi Mulungu wanu, ndayankhula izi.
34 Mawu awa sali a anthu kapena a munthu, koma a ine; kotero, mudzachitira umboni iwo ndi a ine ndipo osati a munthu;
35 Pakuti ndi liwu langa limene likuyankhula iwo kwa inu; pakuti apatsidwa ndi Mzimu wanga kwa inu, ndipo mwa mphamvu yanga inu mukhonza kuwerenga iwo wina ndi mzake; ndipo kupatula kuti zidali mwamphamvu yanga inu simukadatha kukhala nawo;
36 Kotero, mutha kuchitira umboni kuti mudamva mawu anga, ndipo mukudziwa mawu anga.
37 Ndipo tsopano, taonani, ndikupereka kwa iwe, Oliver Cowdery, komanso kwa David Whitmer, kuti mudzafufuza Khumi ndi Awiri, amene adzakhala ndi zikhumbo zomwe ndayankhula;
38 Ndipo ndi zokhumba zawo ndi ntchito zawo inu mudzawadziwa.
39 Ndipo pamene mwawapeza iwo inu mudzawaonetse zinthu izi kwa iwo.
40 Ndipo mudzagwa pansi ndi kulambira Atate mu dzina langa.
41 Ndipo inu mukuyenera kulalikira kwa dziko lapansi, kunena: Inu mukuyenera kulapa ndi kubatizidwa, mu dzina la Yesu Khristu;
42 Pakuti anthu onse akuyenera kulapa ndi kubatizidwa, osati amuna okha, koma akazi, ndi ana amene afika pa zaka za kuyankha mlandu.
43 Ndipo tsopano, mutatha kulandira izi, mukuyenera kusunga malamulo anga mu zinthu zonse;
44 Ndipo ndi manja anu ndidzagwira ntchito yodabwitsa pakati pa ana a anthu, kwa kutsimikizira ambiri ku machimo awo, kuti athe kubwera m’kulapa, ndi kuti iwo athe kukafika ku ufumu wa Atate anga.
45 Kotero, madalitso amene ine ndipereka kwa inu ali pamwamba pa zinthu zonse.
46 Ndipo mutatha kulandira izi, ngati simusunga malamulo anga simungathe kupulumutsidwa mu ufumu wa Atate anga.
47 Taonani, ine, Yesu Khristu, Ambuye wanu ndi Mulungu wanu, ndi Muwomboli wanu, mwa mphamvu ya Mzimu wanga ndayankhula izi. Ameni.