Gawo 126
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, mu nyumba ya Brigham Young, ku Nauvoo, Illinois, Julayi 9, 1841. Brigham Young adali atangobwelera ku banja lake ku Nauvoo kuchokera ku mishoni ya zaka ziwiri kupita ku England.
1–3, Brigham Young ayamikiridwa chifukwa cha ntchito zake ndipo amasuka paulendo wamtsogolo wakunja kwa dziko.
1 M’bale wokondedwa, Brigham Young, indetu akutero Ambuye kwa iwe: Mtumiki wanga Brigham, sikukufunikanso m’dzanja lako kusiya banja lako monga kale, pakuti nsembe yako ndiyovomelezeka kwa ine.
2Â Ndaona ntchito yako ndi kuvutikira kwako paulendo chifukwa cha dzina langa.
3Â Kotero ndikukulamula kuti utumize mawu anga kunja kwa dziko, ndikusamalira makamaka banja lako kuyambira pano mpaka muyaya. Ameni.