Gawo 96
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, Juni 4, 1833. Chochitikacho chidali msonkhano wa akulu ansembe, ndipo mutu wankhani woganiziridwa udali kutaya minda ina, yodziwika kuti munda wa Falansa, ogulidwa ndi Mpingo pafupi ndi Kirtland. Popeza msonkhanowu sudagwirizane amene angatenge ulamuliro wa mundawu, onse adagwirizana kuti afunse Ambuye zokhudzana ndi nkhaniyi.
1, Siteki ya Kirtland ya Ziyoni ikuyenera kukhala yolimba; 2–5, Bishopu akuyenera kugawa zolowa za Oyera mtima; 6–9, John Johnson akuyenera kukhala membala wa bungwe logwirizana.
1Â Taonani, ndinena kwa inu, nayi nzeru, imene mungathe kudziwira kuchitidwe kokhudzana ndi nkhani iyi, pakuti ndizoyenera mwa ine kuti siteki iyi imene ine ndaikhazikitsa pa kulimbikitsa Ziyoni ipangidwe kukhala yolimba.
2 Kotero, lolani mtumiki wanga Newel K. Whitney atenge utsogoleri wa malo amene atchulidwa pakati panu, pamene ine ndakonza kuti nyumba yanga yoyera imadwepo.
3 Ndiponso, iloleni igawidwe m’magawo, molingana ndi nzeru, pa phindu la iwo amene akufuna zolowa, monga zidzatsimikiziridwe mu msonkhano pakati panu.
4Â Kotero, onetsetsani kuti mukonze nkhani imeneyi, ndi gawo limene liri lofunikira kupindulira dongosolo langa, pa cholinga chobweretsa mawu anga kwa ana a anthu.
5Â Pakuti taonani, ndikunena kwa inu, ichi ndi chofunikira kwambiri kwa ine, kuti mawu anga apite kwa ana a anthu, pa cholinga chogonjetsa mitima ya ana a anthu pa ubwino wanu. Ngakhale choncho. Ameni.
6 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, ndi chanzeru ndi chofunikira mwa ine, kuti mtumiki wanga John Johnson amene chopereka chake ndachivomeleza, ndipo amene mapemphero ake ndawamva, kwa amene ndapereka lonjezo la moyo wosatha pamene iye asunga malamulo anga kuchokera pano—
7 Pakuti iye ndi mbadwa ya Yosefe ndi olandira madalitso a lonjezo lopangidwa kwa makolo ake—
8Â Taonani, ndikunena kwa inu, ndi zoyenera mwa ine kuti iye akhale membala wa dongosolo, kuti iye akathe kuthandizira mu kubweretsa mawu anga kwa ana a anthu.
9Â Kotero mudzamudzodza iye ku dalitso limeneli, ndipo iye adzafunafuna mwa khama kuchotsa zotchinga zomwe zili pa nyumba yomwe yanenedwa pakati panu, kuti iye akakhalemo. Ngakhale choncho. Ameni.