Gawo 120
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Far West, Missouri, Julaye 8, 1838, kudziwitsa kagawidwe ka katundu wachakhumi monga zatchulidwira mu vumbulutso lapambuyo, gawo 119.
1Â Indetu, akutero ambuye, nthawi yafika tsopano, kuti zidzagawidwa ndi bungwe, lopangidwa ndi Atsogoleri Oyamba a Mpingo wanga, ndi bishopu ndi bungwe lake, ndi bungwe lalikulu langa; ndi mawu anga omwe kwa iwo, atero Ambuye. Ngakhale choncho. Ameni.