Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 46


Gawo 46

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Mpingo, ku Kirtland, Ohio, Malichi 8, 1831. Mu nthawi yoyambilira ya Mpingo imeneyi, dongosolo logwirizana la kayendetsedwe ka misonkhano ya Mpingo lidali lisadakhazikike. Komabe, mwambo ovomereza mamembala okha ndi ofufuza moona mtima ku misonkhano ya m’gonero ndi misonkhano ina ya Mpingowu idakhala yodziwika. Vumbulutso ili likufotokoza chifuniro cha Ambuye chokhudzana ndi kulamulira ndi kuchititsa misonkhano ndi malangizo Ake pa kufunafuna ndi kuzindikira mphatso za Mzimu.

1–2, Akulu akuyenera kuchita misonkhano motsogozedwa ndi Mzimu Woyera; 3–6, Ofunafuna choonadi sakuyenera kuchotsedwa ku misonkhano ya m’gonero; 7–12, Pemphani kwa Mulungu ndi kufunafuna mphatso za Mzimu; 13–26, Kuwerengera zina za mphatso izi kwaperekedwa; 27–33, Atsogoleri a Mpingo amapatsidwa mphamvu ya kuzindikira mphatso za Mzimu.

1 Mvetserani, O inu anthu a mpingo wanga; pakuti indetu ndinena kwa inu kuti zinthu izi zidayankhulidwa kwa inukuti mupindule ndi kuphunzira.

2 Koma mosatengera za zinthu zimenezo zimene zalembedwa, nthawi zonse zikhale zikuperekedwa kwa akulu a mpingo wanga kuyambira pachiyambi, ndipo zidzachitikabe, kuti azichititsa misonkhano yonse pamene iwo akuyendetsedwa ndi kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

3 Komabe inu mukulamulidwa kuti musamatulutse aliyense pamisonkhano yanu yapagulu, yomwe imachitika pamaso pa dziko lapansi.

4 Inunso mwalamulidwa kuti musatulutse aliyense amene ali wa mpingo kunja kwa misonkhano yanu ya m’gonero; koma ngati wina walakwa, musamulole iye kudya kufikira iye atachita chiyanjanitso.

5 Ndiponso ndinena kwa inu, kuti musadzatulutse aliyense m’misonkhano yanu ya m’gonero amene akufunafuna ufumu moona mtima—ndikuyankhula izi zokhudzana ndi iwo amene sali a mpingo.

6 Ndiponso ndinena kwa inu, zokhudzana ndi misonkhano yanu ya chitsimikiziro, kuti ngati pali ena amene sali a mpingo, amene moona mtima akufunafuna Ufumu, inu musadzawatulutse iwo.

7 Koma mwalamulidwa mu zonse kupempha kwa Mulungu, amene amapatsa molowa manja; ndi icho chimene Mzimu umachitira umboni kwa inu ngakhale kotero ine ndikadafuna kuti muchite mu chiyero chonse cha mtima, kuyenda mowongoka pamaso panga, kulingalira mapeto a chipulumutso chanu, kuchita zinthu zonse ndi pemphero ndi chiyamiko, kuti inu musathe kunyengeka ndi mizimu yoipa, kapena ziphunzitso za ziwanda, kapena malamulo a anthu; pakuti ena ali a anthu, ndi ena a ziwanda.

8 Kotero, chenjerani kuti munganyengedwe; ndipo kuti musanyengedwe funani moona mtima mphatso zopambana, kukumbukila nthawi zonse pa zimene zimapatsidwa;

9 Pakuti indetu ndinena kwa inu, zimaperekedwa kwa phindu la iwo amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga onse, ndipo iye amene akufuna kutero; kuti onse akapindule amene akufuna kapena akupempha kwa ine, amene apempha ndipo osati chizindikiro, kuti akathe kuchiwononga pa zilakolako zawo.

10 Ndiponso, indetu ine ndinena kwa inu, ine ndikufuna kuti nthawi zonse muzikumbukira, ndipo nthawi zonse kusunga mu malingaliro anu chimene mphatso izo zili, zimene zaperekedwa kwa mpingo.

11 Pakuti si onse ali nazo mphatso zonse zopatsidwa kwa iwo; pakuti mphatso zilipo zambiri, ndipo kwa munthu aliyense wapatsidwa mphatso mwa Mzimu wa Mulungu.

12 Kwa ena yaperekedwa ina, ndi kwa ena ina, kuti onse apindule nazo.

13 Kwa ena kumapatsidwa mwa Mzimu Woyera kuti adziwe kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu, ndi kuti adapachikidwa chifukwa cha machimo adziko lapansi.

14 Kwa ena kumapatsidwa kuti akhulupilire mawu awo, kuti iwonso akakhale nawo moyo wosatha ngati apitiriza kukhala okhulupirika.

15 Ndiponso kwa ena kwapatsidwa mwa Mzimu Woyera kudziwa kusiyana kwa kayendetsedwe ka ntchito, monga kudzakhala kokondweretsa kwa Ambuye yemweyo, molingana ndi momwe Ambuye akufunira, koyenera zifundo zake molingana ndi makhalidwe a ana a anthu.

16 Ndiponso, kwapatsidwa ndi Mzimu Woyera kwa ena kudziwa mitundu yosiyanasiyana ya machitidwe, ngati iwo ali a Mulungu, kuti maonetseredwe a Mzimu apatsidwe kwa munthu aliyense kuti apindule nawo.

17 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, kwa ena kwapatsidwa, mwa Mzimu wa Mulungu, mawu a nzeru.

18 Kwa wina amapatsidwa mawu achidziwitso, kuti onse akathe kuphunzira kukhala anzeru ndi chidziwitso.

19 Ndiponso, kwa ena amapatsidwa kukhala ndi chikhulupiliro kuti achiritsidwe;

20 Ndipo kwa ena amapatsidwa kukhala ndi chikhulupiliro chochiritsa.

21 Ndiponso, kwa ena kwapatsidwa kuchita zodabwitsa;

22 Ndipo kwa ena kwapatsidwa kunenera;

23 Ndi kwa ena kuzindikira mizimu.

24 Ndiponso, kwapatsidwa kwa ena kuyankhula ndi malilime;

25 Ndipo kwa wina kwapatsidwa kumasulira kwa malilime.

26 Ndipo mphatso zonsezi zimachokera kwa Mulungu, chifukwa cha phindu la ana a Mulungu.

27 Ndipo kwa bishopu wa mpingo, ndi kwa iwo amene Mulungu adzawasankha ndi kuwadzodza kuti ayang’anire mpingo ndi kukhala akulu a mpingo, akuyenera kupatsidwa kwa iwo kuzindikira mphatso zonse izo kuopa kuti pangakhale wina wa inu wodzinenera koma osati wa Mulungu.

28 Ndipo kudzachitika kuti iye amene apempha mu Mzimu adzalandira mu Mzimu;

29 Kuti kwa ena kutha kupatsidwa kukhala nazo mphatso zonsezo, kuti pakathe kukhala mutu, ndi cholinga kuti membala aliyense apindule nazo.

30 Iye amene amapempha mu Mzimu amapempha molingana ndi chifuniro cha Mulungu; kotero zimachitidwa ngakhale monga adapempha.

31 Ndiponso, ndinena kwa inu, zinthu zonse zikuyenera kuchitidwa mu dzina la Khristu, zilizonse mudzichita mu Mzimu;

32 Ndipo inu mukuyenera kuyamika Mulungu mu Mzimu pa dalitso lina lililonse limene munadalitsidwa nalo.

33 Ndipo inu muzichita ukoma ndi chiyero pamaso panga nthawi zonse. Ngakhale zili choncho. Ameni.