Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 122


Mutu 122

Mawu a Ambuye kwa Joseph Smith Mneneri, pamene adali mkaidi mu ndende ya Liberty, Missouri. Gawo ili ndi lotengedwa kuchokera ku kalata yakumpingo yolembedwa cha M’malitchi 22, 1839.

1–4, Malekezero a dziko lapansi adzafunsa za dzina la Joseph Smith; 5–7, Masautso ake onse ndi mazunzo zidzampatsa iye mangolomera ndikukhala za ubwino wake; 8–9, Mwana wa Munthu wadutsa pansi pa zonse.

1 Malekezero a dziko lapansi adzafunsa za dzina langa, ndipo opusa adzakunyozani inu, ndipo gahena udzalusa motsutsana nanu;

2 Pamene oyera mtima, ndi anzeru, ndi wolemekezeka, ndi aukoma, adzafuna uphungu, ndi ulamuliro, ndi madalitso kosalekeza kuchokera pansi pa dzanja lako.

3 Ndipo anthu ako sadzatembenuzidwa motsutsana nawe ndi umboni wa achiwembu.

4 Ndipo ngakhale mphamvu zawo zidzakuponya iwe m’mavuto, ndi mzitsulo ndi makoma, udzachotsedwa ulemu; ndipo koma kwa kanthawi kochepa ndipo mawu ako adzakhala owopsya pakati pa adani ako kuposa mkango wobuma, chifukwa cha chilungamo chako; ndipo Mulungu wako adzaima nawe ku nthawi za nthawi.

5 Ngati iwe waitanidwa kudutsa muzowawitsa; ngati iwe uli muzoopsya pakati pa abale onama; ngati iwe uli muzoopsya pakati pa ambanda; ngati iwe uli mu zoopsya ndi nthaka kapena nyanja;

6 Ngati iwe ukuzengedwa ndi milandu yosiyanasiyana yabodza; ngati adani ako agwera pa iwe; ngati iwo akuchotsa iwe mu ubale wa atate ako ndi amayi ako ndi achimwene ako ndi alongo ako, ndi ana ako, ndi mwana wako mamwamuna wamkulu, ngakhale koma wadzaka zisanu ndi chimodzi chakubadwa adzakangamira ku chovala chako, ndipo adzanena, Atate anga, atate anga, bwanji simungakhale nafe? O atate anga, kodi anthuwa achita nanu chiyani? ndipo ngati kenako iye adzasompholedwa kwa iwe ndi lupanga, ndipo iwe kuponyedwa mundende, ndipo adani ako kukukhamukira iwe ngati mimbulu ku mwazi wa mwana wa nkhosa;

7 Ndipo ngati ungaponyedwe mudzenje, kapena mu manja a okupha, ndi chilango cha imfa chidzaperekedwa pa iwe; ngati iwe ungaponyedwa mkuya; ngati utsi ungakufungatire iwe; ndipo mphepo zowopsya zikhala mdani wako; ngati mitambo ikungana mdima; ndi zinthu ziphatikana kutchinga njira yako, ndipo pamwamba pa zonse; ngati nsagwada za gahena zidzatsegula kamwa lake kuti zikumeze, dziwa iwe, mwana wanga, kuti zinthu zonsezi zidzakupatsa iwe mangolemera, ndipo zidzakhala za ubwino wako.

8 Mwana wa Munthu adadutsa pansi pa zonsezi. Kodi ndiwe wamkulu kuposa iye?

9 Kotero, khalabe mu njira yako, ndipo unsembe udzakhalabe ndi iwe; pakuti malire awo aikidwa, iwo sangadutsepo. Masiku akudziwika, ndipo zaka zako sizadzawerengedwa zochepa; kotero, usaope chimene munthu angachite, pakuti Mulungu adzakhala nawe ku nthawi ndi nthawi zosatha.