Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 19


Gawo 19

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith, ku Manchester, New York, n’kutheka cha mu chirimwe cha 1829. Mu mbiri yake, Mneneriyu amalitchula kuti “lamulo la Mulungu osati la munthu, kwa Martin Harris, loperekedwa ndi iye amene ali Wamuyaya.”

1–3, Khristu ali ndi mphamvu zonse; 4–5, Anthu onse akuyenera kulapa kapena kuzunzika; 6–12, Chilango chamuyaya ndi chilango cha Mulungu; 13–20, Khristu adavutikira onse, kuti asazunzike ngati angalape; 21–28, Lalikani uthenga wabwino wa kulapa; 29–41, Lengezani uthenga wabwino.

1 Ine ndine Alefa ndi Omega, Khristu Ambuye; inde, ngakhale ine ndine iye, oyamba ndi otsiriza, Muwomboli wa dziko lapansi.

2 Ine, nditakwaniritsa ndi kutsiriza chifuniro cha iye amene ine ndili wake ngakhale Atate, zokhudzana ndi ine—nditachita ichi kuti ndikagonjetse zinthu zonse kwa ine ndekha—

3 Kusunga mphamvu zonse, mpaka kuwononga Satana ndi ntchito zake pa mapeto a dziko lapansi, ndi tsiku lalikulu lomaliza la chiweruzo, limene ndidzapereka kwa anthu okhalamo, kuweruza munthu aliyense molingana ndi ntchito zake ndi ntchito zake zimene adazichita.

4 Ndipo ndithudi munthu aliyense akuyenera kulapa kapena kusautsika, pakuti ine, Mulungu, ndilibe mapeto.

5 Kotero, sindidzabweza ziweruzo zimene ndidzapereka, koma tsoka lidzapita, kulira, kubuula ndi kukukuta kwa mano, inde, kwa iwo amene adzapezedwa ku dzanja langa lamanzere.

6 Komabe, sikudalembedwa kuti kuzunzika kumeneku sikudzatha, koma kwalembedwa chizunzo chosatha.

7 Komanso, kwalembedwa chiwonongeko chamuyaya; kotero ndi kufotokoza kwambiri kuposa malemba ena, kuti zikathe kugwira ntchito pa mitima ya ana a anthu, palimodzi chifukwa cha ulemerero wa dzina langa.

8 Kotero, ndikufotokozerani chinsinsi ichi, chifukwa ndi koyenera kwa inu kudziwa ngati atumwi anga.

9 Ndiyankhula kwa inu osankhidwa mu chinthu ichi, ngakhale monga m’modzi, kuti mukathe kulowa mu mpumulo wanga.

10 Pakuti, taonani, chinsinsi cha umulungu, ndi chachikulu bwanji! Pakuti, taona, ine ndilibe mapeto, ndipo chilango chimene chaperekedwa kuchokera m’dzanja langa ndi chilango chosatha, pakuti Wamuyaya ndilo dzina langa. Kotero—

11 Chilango chamuyaya ndi chilango cha Mulungu.

12 Chilango chosatha ndi chilango cha Mulungu.

13 Kotero, ndikulamula iwe kuti ulape, ndi kusunga malamulo amene walandira ndi dzanja la mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., m’dzina langa;

14 Ndipo ndi mwa mphamvu yanga yayikulu kuti udawalandira iwo;

15 Kotero ndikukulamula kuti ulape—ulape, kuwopa kuti ndingakukanthe ndi ndodo ya m’kamwa mwanga, ndi ukali wanga, ndi mkwiyo wanga, ndi kuzunzika kwako kukhala kowawa—kuwawa bwanji iwe sudziwa, kwambiri bwanji iwe sudziwa, inde, kuvuta kupilira kwake iwe sudziwa.

16 Pakuti, taona, ine, Mulungu, ndamva zowawa izi kwa onse, kuti iwo asathe kuzunzika ngati iwo angalape;

17 Koma ngati sanalape akuyenera kuzunzika monga ine;

18 Kuvutika kumene kudandipangitsa inemwini, ngakhale Mulungu, wamkulu koposa zonse, kunjenjemera chifukwa cha ululu, ndi kukhetsa mwazi pamabowo onse, ndi kuvutika zonse thupi ndi mzimu—ndipo ndikadafuna kuti ndisamwe chikho chowawa, ndi kufota—

19 Komabe, ulemerero ukhale kwa Atate, ndipo ndidatenga ndi kutsiriza kukonzekera kwanga kwa ana a anthu.

20 Kotero, ndikukulamulanso kuti ulape, kuwopa kuti ndingakuchepetse ndi mphamvu yanga yayikulu; ndi kuti uvomereze machimo ako, kuwopa kuti ungazunzike zilango izi zomwe ndanena, izo zimene mu kuchepetsa, inde, ngakhale mu mlingo wochepa womwe udalawa pa nthawi yomwe ndidachotsa Mzimu wanga.

21 Ndipo ine ndikukulamula iwe kuti usalalikire china koma kulapa, ndipo usaonetse zinthu izi kwa dziko kufikira itakhala nzeru mwa ine.

22 Pakuti sangathe kulandira nyama tsopano, koma akuyenera kulandira mkaka; kotero iwo asadziwe zinthu izi, kuwopa kuti angawonongeke.

23 Phunzira kwa ine, ndipo mvera mawu anga; yenda m’kufatsa kwa Mzimu wanga, ndipo udzakhala ndi mtendere mwa ine.

24 Ine ndine Yesu Khristu; Ndidadza mwa chifuniro cha Atate, ndipo ndimachita chifuniro chawo.

25 Ndiponso, ndikukulamula iwe kuti usasilire mkazi wa mnansi wako; kapena kufuna moyo wa mnansi wako.

26 Ndiponso, ndikukulamula iwe kuti usasilire chuma chako chomwe, koma upereke momasuka ku kusindikiza kwa Buku la Mormoni, limene lili ndi choonadi ndi mawu a Mulungu—

27 Limene lili liwu langa kwa Amitundu, kuti posachedwapa likhonza kupita kwa Myuda, amene Alamani ali otsalira ake, kuti akathe kukhulupilira uthenga wabwino, ndipo asayang’ane kwa Mesiya kuti adzabwere amene adabwera kale.

28 Ndiponso, ndikukulamula iwe kuti udzipemphera momveka komanso mumtima mwako; inde, pamaso pa dziko komanso mu chinsinsi, pamaso pa anthu komanso mseri.

29 Ndipo iwe ulalikire uthenga wabwino, inde, kuulengeza pa mapiri, ndi pa malo aatali onse, ndi mwa anthu onse amene udzaloledwa kuwaona.

30 Ndipo udzichita ndi kudzichepetsa konse, kukhulupilira mwa ine, osachitira chipongwe achipongwewo.

31 Ndipo usayankhule za mfundo zina; koma udzalengeza kulapa ndi chikhulupiliro pa Mpulumutsi, ndi chikhululukiro cha machimo ndi ubatizo, ndi moto, inde, ngakhale Mzimu Woyera.

32 Taona, ili ndi lamulo lalikulu ndi lotsiriza limene ndidzapereka kwa iwe zokhudza nkhani iyi; pakuti izi zidzakhala zokwanira pa ulendo wako wa tsiku ndi tsiku, ngakhale mpaka mapeto a moyo wako.

33 Ndipo chisoni udzalandira ngati upeputsa uphungu uwu, inde, ngakhale kudziwononga kwa iwe mwini ndi chuma.

34 Pereka gawo la chuma chako, inde, ngakhale gawo la minda yako, ndi zonse kupatula thandizo la banja lako.

35 Lipira ngongole yomwe wapangana ndi osindikiza. Dzimasule wekha ku ukapolo.

36 Siya nyumba yako ndi kwanu, kupatula pamene iwe udzakhumba kuona banja lako;

37 Ndipo yankhula momasuka kwa onse; inde, lalikira, chenjeza, lengeza choonadi; ngakhale ndi mawu aakulu, ndi mawu achimwemwe, kufuula—Hosana, Hosana, lidalitsike dzina la Ambuye Mulungu!

38 Pemphera nthawi zonse, ndipo ndidzatsanulira pa iwe Mzimu wanga; ndipo aakulu adzakhala madalitso ako—inde, kuposa ngati utapeza chuma cha padziko lapansi ndi chivundi kuchuluka kwake.

39 Taona, kodi ungawerenge izi popanda kusangalala ndi kukweza mtima wako chifukwa cha chisangalalo?

40 Kapena utha kuthamanga motalika ngati wotsogolera wakhungu?

41 Kapena ungakhale wodzichepetsa ndi wofatsa, ndi kuchita mwanzeru pamaso panga? Inde, bwera kwa ine Mpulumutsi wako. Ameni.