Gawo 97
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Ogasiti 2, 1833. Vumbulutso ili limakamba makamaka za zochitika za Oyera Mtima mu Ziyoni, Jackson County, Missouri, poyankha ku funso la Mneneri kwa Ambuye pa zambiri zokhudza sukulu ya aneneri ku Missouri. Mamembala a Mpingo ku Missouri adali pa nthawiyi akukumana ndi chizunzo choopsya ndipo, pa Julaye 23, 1833 adakakamizidwa kusayinira mgwirizano wochoka ku Dera la Jackson.
1–2, Oyera mtima ambiri mu Ziyoni (Jackson County, Missouri) adalitsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwawo; 3–5, Parley P. Pratt ayamikiridwa pa ntchito yake mu sukulu ya Ziyoni; 6–9, Iwo amene amasunga mapangano awo ndi ovomelezeka ndi Ambuye; 10–17, Nyumba ikuyenera kumangidwa mu Ziyoni mumene oyera mu mtima adzaona Mulungu; 18–21, Ziyoni ndi oyera mu mtima; 22–28, Ziyoni adzathawa chilango cha Ambuye ngati akhala okhulupirika.
1Â Indetu ndikunena kwa inu abwenzi anga, ndikuyankhula kwa inu ndi mawu anga, ngakhale mawu a Mzimu wanga, kuti ndikaonetsere kwa inu chifuniro changa chokhudza abale anu mu dziko la Ziyoni, ambiri mwa iwo ali odzichepetsadi ndipo akufuna mwakhama kuphunzira nzeru ndi kupeza choonadi.
2Â Indetu, indetu, ndinena kwa inu, odala ndi otero, pakuti iwo adzapeza; pakuti ine, Ambuye, ndimaonetsa chisomo kwa onse ofatsa, ndi pa onse amene ndingafune, kuti ndikalungamitsidwe pamene ndidzawabweretsa iwo ku chiweruzo.
3 Taonani, ndikunena kwa inu, zokhudzana ndi sukulu ya Ziyoni, ine, Ambuye, ndili okondwera kuti kukhale sukulu mu Ziyoni, komanso ndi mtumiki wanga Parley P. Pratt, pakuti iye ali mwa ine.
4Â Ndipo pamene iye apitiriza kukhala mwa ine iye adzapitiriza kutsogolera pa sukuluyi mu dziko la Ziyoni kufikira nditapereka kwa iye malamulo ena.
5Â Ndipo ndidzamudalitsa iye ndi madalitso ochuluka, mu kufotokozera malembo onse ndi zinsinsi ku kumangiriza sukulu, ndi mpingo mu Ziyoni.
6Â Ndi kwa masukulu otsalira, ine, Ambuye, ndikufuna kuonetsa chifundo; komabe, alipo iwo amene akufunikira kulangidwa, ndipo ntchito zawo zidzadziwika.
7Â Nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; ndipo mtengo uliwonse umene siubeleka zopatso zabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pamoto. Ine, Ambuye, ndanena ichi.
8 Indetu ndinena kwa inu, onse mwa iwo amene akudziwa mitima yawo ndi yachilungamo, ndipo ndiyosweka, ndipo mizimu yawo yolapa, ndipo akufuna kusunga mapangano awo mwa nsembe—inde, nsembe iliyonse imene ine, Ambuye, ndidzalamula—ali ovomelezedwa ndi ine.
9Â Pakuti ine, Ambuye, ndidzachititsa iwo kuti abale zipatso monga zipatso zobzalidwa mu nthaka yabwino, mphepete mwa mtsinje woyera, umene udzabeleka zipatso zamtengo wapatali.
10Â Indetu ndikunena kwa inu, kuti ndi chifuniro changa kuti nyumba imangidwe kwa ine mu dziko la Ziyoni, yofanana ndi maonekedwe amene ine ndakupatsani.
11Â Inde, lolani iyo imangidwe mwachangu, ndi chakhumi cha anthu anga.
12 Taonani, ichi ndi chakhumi ndi nsembe imene ine, Ambuye, ndikuifuna pa manja awo, kuti kumeneko kukathe kukhala nyumba yomangidwa kwa ine ku chipulumutso cha Ziyoni—
13Â Pa malo akuthokozera a oyera mtima onse, ndi pa malo a malangizo kwa onse amene aitanidwa ku ntchito ya utumiki mu maitanidwe awo osiyanasiyana ndi maudindo;
14Â Kuti iwo akalungamitsidwe mu kumvetsa kwa utumiki wawo, mu nzeru, mu mfundo yofunika, ndi mu chiphunzitso, mu zonse zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi, mafungulo ake a ufumuwo apatsidwa kwa inu.
15 Ndipo pamene anthu anga amanga nyumba kwa ine mu dzina la Ambuye, ndipo sakulola chodetsedwa chinachilichonse kulowa m’menemo, kuti isadetsedwe, ulemelero wanga udzakhala pamenepo;
16 Inde, ndipo kupezeka kwanga kudzakhalamo, pakuti ndidzabwera m’menemo, ndipo onse oyera mu mtima amene adzabweramo adzaona Mulungu.
17Â Koma ngati idetsedwa sindidzabweramo, ndipo ulemelero wanga sudzakhalamo; pakuti sindidzabwera mu kachisi wosayera.
18Â Ndipo, tsopano, taonani, ngati Ziyoni achita zinthu izi iye adzachitabwino, ndikudzifalitsa yekha, ndi kukhala wa ulemelero waukulu, ndi wamphamvu kwambiri, ndi owopsya kwambiri.
19 Ndipo maiko a dziko lapansi adzamulemekeza, ndipo adzati: Zoonadi Ziyoni ndi mzinda wa Mulungu wathu, ndipo zoonadi Ziyoni sangagwe, kapena kuchotsedwa m’malo ake, pakuti Mulungu ali m’menemo, ndipo dzanja la Ambuye lili kumeneko;
20Â Ndipo iye walumbira ndi mphamvu ya mphamvu yake kukhala chipulumutso chake ndi nsanja yake yapamwamba.
21 Kotero, indetu, akutero Ambuye, lolani Ziyoni akondwere, pakuti uyu ndi Ziyoni—oyera mu mtima; kotero, lolani Ziyoni akondwere, pamene oipa onse adzalira.
22Â Pakuti taonani, ndipo onani, kubwenzera kubwera mwachangu pa wosapembedza monga kamvulumvulu; ndi ndani angamuthawe?
23Â Mliri wa Ambuye udzadutsa mu usiku ndi usana, ndipo mbiri yake idzazunza anthu onse; inde, siidzaimikidwa kufikira Ambuye atabwera;
24Â Pakuti mkwiyo wa Ambuye wayaka motsutsana ndi zonyansa zawo ndi ntchito zawo zoipa zonse.
25Â Komabe, Ziyoni adzathawa ngati iye asunga kuchita zinthu zonse zimene ine ndamulamula iye.
26Â Koma ngati iye sasunga kuchita zimene ine ndamulamula iye, ndidzamuyendera iye molingana ndi ntchito zake zonse, ndi masautso oopsya, ndi chigumula, ndi mliri, ndi lupanga, ndi kubwezera, ndi moto wonyeketsa.
27Â Komabe, lolani ziwerengedwe kamodzi kokhaka ku makutu ake, kuti ine, Ambuye, ndavomeleza nsembe yake; ndipo ngati iye sachimwanso zinthu zonsezi sizidzabwera pa iye;
28Â Ndipo ndidzamudalitsa iye ndi madalitso, ndi kuchulukitsa madalitso ochuluka pa iye, ndi pa mibadwo yake ku nthawi za nthawi, atero Ambuye Mulungu wanu. Ameni.