Mutu 30
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa David Whitmer, Peter Whitmer Jr., ndi John Whitmer, ku Fayette, New York, Seputembara 1830, potsatira msonkhano wa masiku atatu mu Fayette, koma asadasiyane akulu a Mpingo. Poyambilira zinthu izi zidasindikizidwa ngati mavumbulutso atatu; zidaphatikizidwa mu gawo limodzi ndi Mneneri mu kope la 1835 la Chiphunzitso ndi Mapangano.
1–4, David Whitmer alangidwa chifukwa cholephera kutumikira mwakhama; 5–8, Peter Whitmer Jr. adzaperekezana ndi Oliver Cowdery ku mishoni kwa Alamani;9–11, John Whitmer akuitanidwa kukalalikira uthenga wabwino.
1 Taona, ndinena kwa iwe, David, kuti iwe waopa munthu, ndipo sudandidalire ine kuti ndikupatse mphamvu monga ukuyenera.
2 Koma malingaliro ako akhala pa zinthu za dziko lapansi koposa pa zinthu za ine, Mlengi wako, ndi utumiki umene iwe waitanidwako; ndipo sudamvetsere kwa Mzimu wanga, ndi kwa iwo amene adakhazikidwa pa iwe, koma wakopeka ndi iwo amene sindidawalamule.
3 Kotero, iwe wasiyidwa kuti udzifunse wekha pa dzanja langa, ndi kulingalira pa zinthu zimene iwe udalandira.
4 Ndipo kwanu kudzakhala ku nyumba ya atate ako, mpaka ine ndidzakupatse iwe malamulo ena. Ndipo udzasamalira utumiki mu mpingo, ndi pamaso pa dziko, ndi madera ozungulira. Ameni.
5 Taona, ndinena kwa iwe, Peter, kuti udzatenga ulendo wako ndi m’bale wako Oliver; pakuti nthawi yafika kuti ndi kofunika mwa ine kuti udzatsegule pakamwa pako kuti ulalikile uthenga wanga wabwino; kotero, usaope, koma mvetsera ku mawu ndi uphungu wa m’bale wako, umene iye adzakupatsa iwe.
6 Ndipo khala iwe osautsidwa m’masautso ake onse, ukukwezera mtima wako nthawi zonse kwa ine mupemphero ndi chikhulupiliro, pa chiwombolo cha iye ndi chako; pakuti ndapereka kwa iye mphamvu kuti amange mpingo wanga pakati pa Alamani;
7 Ndipo palibe amene ndamuika kukhala mlangizi wake pa iye mu mpingo, zokhudza nkhani za mpingo, kupatula m’bale wake, Joseph Smith, Jun.
8 Kotero, mvetsera ku zinthu izi ndi kukhala wolimbikira mu kusunga malamulo anga, ndipo udzadalitsidwa ku moyo wosatha. Ameni.
9 Taona, ndikunena kwa iwe, mtumiki wanga John, kuti udzayamba kuchokera nthawi ino kupita patsogolo kulalikira uthenga wanga wabwino, monga ndi mawu a lipenga.
10 Ndipo ntchito yako idzakhala kwa m’bale wako Philip Burroughs’, ndi muchigawo chimenecho mozungulira, inde, kulikonse kumene ungakhonze kumvedwa, mpaka ine nditakulamula iwe kuchoka kuno.
11 Ndipo ntchito yako yonse idzakhala mu Ziyoni, ndi moyo wako wonse, kuyambira tsopano; inde, udzatsegula pakamwa pako nthawi zonse pa cholinga changa, osaopa chimene munthu angachite, pakuti ine ndili ndi iwe. Ameni.