Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 20


Gawo 20

Vumbulutso la kakhazikitsidwe ndi kayendetsedwe ka Mpingo, loperekedwa kudzera kwa Joseph Smith Mneneri, ku kapena pafupi ndi Fayette, New York. Magawo a vumbulutsoli atha kukhala kuti adaperekedwa cha m’chirimwe cha 1829. Vumbulutso lathunthu, lodziwika pa nthawiyo ngati Mfundo ndi Mapangano, n’kutheka kuti lidalembedwa patangotha Epulo 6, 1830 (tsiku limene Mpingo udakhazikitsidwa). Mneneri adalemba, “Tidalandira kwa Iye [Yesu Khristu] zotsatirazi, mwa mzimu wa uneneri ndi vumbulutso; zimene sizidangotipatsa ife chidziwitso chochuluka, komanso zidasonyeza kwa ife tsiku lenileni limene, molingana ndi chifuniro Chake ndi lamulo, tikuyenera kupitiriza kukhazikitsanso Mpingo Wake pano pa dziko lapansi,”

1–16, Buku la Mormoni limatsimikizira umulungu wa ntchito ya m’masiku otsiriza; 17–28, Ziphunzitso za chilengedwe, kugwa, chitetezero, ndi ubatizo zatsimikizidwa; 29–37, Malamulo olamulira zakulapa, zakulungamitsa, zakuyeretsedwa, ndi zaubatizo akhazikitsidwa; 38–67, Ntchito za akulu, ansembe, aphunzitsi, ndi madikoni zifotokozedwa mwachidule; 68–74, Ntchito ya mamembala, kudalitsa ana, ndi njira ya ubatizo ziwululidwa; 75–84, Mapemphero a mgonero ndi malamulo olamulira umembala wa Mpingo aparekedwa,

1 Kuphukira kwa Mpingo wa Yesu Khristu mu masiku ano otsiriza, pokhala chaka cha chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi atatu ndi makumi atatu chibwelereni Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu muthupi, iwo wokhala ukukonzedwa ndi kukhazikitsidwa mogwirizana ndi malamulo a dziko lathu, mwa chifuniro ndi malamulo a Mulungu, mu mwezi wachinayi, ndi pa tsiku la chisani ndi limodzi la mwaziwo umene umatchedwa Epulo—

2 Amene malamulo ake adaperekedwa kwa Joseph Smith, Jun., amene adaitanidwa ndi Mulungu, ndi kudzodzedwa Mtumwi wa Yesu Khristu, kukhala mkulu woyamba wa mpingo uno;

3 Ndi kwa Oliver Cowdery, amene adaitanidwanso ndi Mulungu, Mtumwi wa Yesu Khristu, kukhala mkulu wachiwiri wa mpingo uno, ndi kudzodzedwa pansi pa dzanja lake;

4 Ndipo izi molingana ndi chisomo cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, kwa iye kukhale ulemelero wonse, pano ndi kunthawi zosatha. Ameni.

5 Pambuyo pa kuonetseredwa moonadi kwa mkulu woyambayu kuti iye adalandira chikhululukiro cha machimo ake, iye adakodwanso mu zachabechabe za dziko lapansi;

6 Koma atatha kulapa, ndi kudzichepetsa yekha moona mtima, kudzera mwa chikhulupiliro, Mulungu adatumikira kwa iye kudzera mwa mngelo woyera, amene maonekedwe ake adali ngati mphezi, ndipo amene chovala chake chidali chowala ndi choyera kuposa kuyera kwina konse.

7 Ndipo adapereka kwa iye malamulo amene adauzira iye;

8 Ndipo adampatsa mphamvu kuchokera kumwamba, mu njira imene idakonzedwa kale, kuti amasulire Buku la Mormoni;

9 Limene lili ndi zolemba za anthu amene adafa, ndi chidzalo cha uthenga wabwino wa Yesu Khristu kwa Amitundu ndiponso kwa Ayuda;

10 Limene lidaperekedwa mwa kuuziridwa, ndipo ndilotsimikiziridwa ndi ena mwa utumiki wa angelo, ndipo likulengezedwa ku dziko lapansi ndi iwo—

11 Kutsimikizira ku dziko kuti malembo oyera ndi oona, ndipo kuti Mulungu amauzira anthu ndi kuwaitanira iwo ku ntchito yake yoyera mu nyengo ndi m’badwo uno, chimodzimodzi mu mibadwo yakale.

12 Potero kuonetsa kuti iye ndi Mulungu yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zosatha. Ameni.

13 Kotero, pokhala ndi mboni zochuluka chonchi, ndi izo dziko lidzaweruzidwa, ngakhale onse amene pambuyo pake adzabwera kuchidziwitso cha ntchito imeneyi.

14 Ndipo iwo amene ailandira mu chikhulupiliro, ndi kuchita chilungamo, adzalandira kolona wa moyo wamuyaya;

15 Koma iwo amene adzaumitsa mitima yawo mu kusakhulupilira, ndi kuikana, idzatembenukira ku chiweruzo chawo chomwe—

16 Pakuti Ambuye Mulungu wayankhula ichi; ndipo ife, akulu a mpingo, tamva ndi kuchitira umboni ku mawu a Mfumu yaulemelero ya kumwamba, kwa iye kukhale ulemelero kunthawi ndi nthawi zosatha. Ameni.

17 Mwa zinthu izi ife tikudziwa kuti kuli Mulungu kumwamba, amene ali wamphamvu ndi wamuyaya, kuyambira kunthawi zosatha ndi kunthawi zosatha Mulungu yemweyo wosasintha, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zinthu zonse zimene zili m’menemo;

18 Ndipo kuti iye adalenga munthu, mwamuna ndi mkazi, potsatira chifaniziro chake, ndi maonekedwe ake, iye adawalenga iwo;

19 Ndi kupereka kwa iwo malamulo kuti adzikonda ndi kumutumikira iye, Mulungu yekhayo wamoyo ndi oona, ndipo kuti akhale munthu yenkhayo amene iwo adzipembedza.

20 Koma mwa kulakwira kwa malamulo oyera amenewa munthu adakhala wachithupithupi ndi waudyelekezi, ndi kukhala munthu wakugwa.

21 Kotero, Mulungu wamphamvu zonse adapereka Mwana wake Wobadwa yekha, monga kudalembedwera mu malembo oyerawo amene adaperekedwa a iye.

22 Iye adazunzika mayesero koma sadamvere kwa iwo.

23 Iye adapachikidwa, adafa, ndipo adaukanso tsiku lachitatu.

24 Ndipo adakwera kumwamba, kukakhala pansi ku dzanja lamanja la Atate, kukalamulira ndi mphamvu zonse molingana ndi chifuniro cha Atate;

25 Kuti pamene ambiri adzakhulupilira ndi kubatizidwa mu dzina lake loyera, ndi kupilira mu chikhulupiliro mpaka kumapeto, adzapulumutsidwa—

26 Osati okhawo amene adakhulupilira atabwera mu nthawi ya meridiyani, mu thupi, koma onse amene kuyambira pachiyambi, ngakhale ambiri amene adabadwa iye asadabwere, amene adakhulupilira mu mawu a aneneri oyera, amene adayankhula pamene adauzira ndi mphatso ya Mzimu Woyera, amene adachitira umboni moona za iye mu zinthu zonse, adzakhala ndi moyo wamuyaya,

27 Limodzinso ndi iwo amene adzabwera pambuyo pake, amene adzakhulupilira mu mphatso ndi maitanidwe a Mulungu mwa Mzimu Woyera, umene umachitira umboni wa Atate ndi wa Mwana;

28 Amene Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera ndi Mulungu m’modzi, wamphamvu ndi wamuyaya, opanda malire. Ameni.

29 Ndipo tikudziwa kuti anthu onse akuyenera kulapa ndi kukhulupilira mu dzina la Yesu Khristu, ndi kulambira Atate mu dzina lake, ndi kupilira mu chikhulupiliro pa dzina lake mpaka mapeto, kapena iwo sangathe kupulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu.

30 Ndipo tikudziwa kuti kulungamitsa kudzera mwa chisomo cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu ndi kolungama ndi koona;

31 Ndipo tikudziwanso, kuti kuyeretsedwa kudzera mwa chisomo cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu ndi kolungama ndi koona, kwa iwo onse amene amakonda ndi kutumikira Mulungu ndi mphamvu, malingaliro, ndi nyonga zawo zonse.

32 Koma pali kuthekera kuti munthu akhonza kugwa ku chisomo ndi kuchoka kwa Mulungu wamoyo;

33 Kotero lolani mpingo ukhale watcheru ndi kupemphera nthawi zonse kuopa angagwe m’mayesero;

34 Inde, ndipo ngakhale lolani iwo amene ayeretsedwa kukhale atcherunso.

35 Ndipo tikudziwa kuti zinthu izi ndi zoona ndipo molingana ndi mavumbulutso a Yohane, posawonjezera, kapena kuchotsera ku uneneri wa mubuku lake, malembo oyera, kapena mavumbulutso a Mulungu amene adzabwera kuchokera pano mwa mphatso ndi mphamvu ya Mzimu Woyera, mawu a Mulungu, kapena utumiki wa angelo.

36 Ndipo Ambuye Mulungu wayankhula izi; ndipo ulemu, mphamvu ndi ulemelero zipite ku dzina lake loyera, tsopano ndi kunthawi zosatha. Ameni.

37 Ndiponso, mwa njira ya lamulo ku mpingo lokhudzana ndi kachitidwe ka ubatizo—Onse amene adzichepetsa wokha pamaso pa Mulungu, ndi kukhumba kuti abatizidwe, ndi kubwera ndi mitima yosweka ndi mizimu yolapa, ndi kuchitira umboni pamaso pa mpingo kuti iwo alapa kwathunthu machimo awo onse, ndipo akufuna kutenga pa iwo dzina la Yesu Khristu, pokhala wotsimikizika kumutumikira iye mpaka kumapeto, ndi kuonetsa moona ndi ntchito zawo kuti iwo alandira kwa Mzimu wa Khristu chikhululukiro cha machimo awo, adzalandiridwa mwa ubatizo mu mpingo wake.

38 Ntchito ya akulu, ansembe, aphunzitsi, madikoni, ndi mamembala a mpingo wa Khristu—Mtumwi ndi Mkulu, ndipo ndi ntchito yake kubatiza;

39 Ndi kudzodza akulu ena, ansembe, aphunzitsi ndi madikoni;

40 Ndi kuperekera mkate ndi vinyo—zizindikiro za thupi ndi mwazi wa Khristu—

41 Ndi kutsimikizira iwo amene abatizidwa mu mpingo, posanjikiza manja pa ubatizi wa moto ndi Mzimu Woyera, molingana ndi malembo;

42 Ndi kuphunzitsa, kufotokozera, kulimbikitsa, kubatiza ndi kuyang’anira mpingo;

43 Ndi kutsimikizira mpingo posanjikiza manja, ndi kupereka Mzimu Woyera;

44 Ndi kutsogolera misonkhano yonse.

45 Akulu akuyenera kutsogolera misonkhano pamene akutsogoleredwa ndi Mzimu Woyera, molingana ndi malamulo ndi mavumbulutso a Mulungu.

46 Ntchito ya ansembe ndi kulalika, kuphunzitsa, kufotokozera, kulimbikitsa, ndi kubatiza, ndi kuperekera mgonero.

47 Ndi kuyendera khomo la membala wina aliyense, ndi kuwalimbikitsa iwo kupemphera mokweza ndi mwa chinsinsi ndi kuchita ntchito zonse zapabanja.

48 Ndipo iye akhonzanso kudzodza ansembe, aphunzitsi ndi madikoni.

49 Ndipo iye akuyenera kutsogolera misonkhano pamene palibe mkulu;

50 Koma pamene mkulu alipo, iye akuyenera kungolalika, kuphunzitsa, kufotokozera, kulimbikitsa ndi kubatiza basi,

51 Ndi kuyendera khomo la membala wina aliyense, kuwalimbikitsa iwo kuti adzipemphera mokweza ndi mwa chinsinsi ndi kuchita ntchito zonse zapabanja

52 Mu ntchito zonsezi wansembe akuyenera kuthandiza mkulu ngati pakufunika kutero.

53 Ntchito za mphunzitsi ndi kuyang’anira mpingo nthawi zonse, ndi kukhala nawo ndi kuwalimbikitso iwo;

54 Ndi kuona kuti palibe kusaweruzika mu mpingo, ngakhale kulimbana wina ndi mzake, ngakhale mabodza, miseche, kape na kuyankhula zoipa.

55 Ndi kuona kuti mpingo ukukumana pamodzi kawirikawiri, ndiponso kuona kuti mamembala onse akuchita ntchito yawo.

56 Ndipo iye akuyenera kutsogolera misonkhano pomwe palibe mkulu kapena wansembe—

57 Ndipo akuyenera kuthandizidwa nthawi zonse, mu ntchito zake zonse mu mpingo, ndi madikoni, ngati pakufunika kutero.

58 Koma onsewa aphunzitsi kapena madikoni alibe ulamuliro wobatiza, kuperekera mgonero, kapena kusanjikiza manja;

59 Iwowa, komabe, akuyenera kuchenjeza, kufotokozera, kulimbikitsa, ndi kuphunzitsa, ndi kuitana onse kuti abwere kwa Khristu.

60 Mkulu aliyense, wansembe, mphunzitsi, kapena dikoni akuyenera kudzodzedwa molingana ndi mphatso ndi mayitanidwe a Mulungu kwa iye; ndipo akuyenera kudzodzedwa ndi mphamvu ya Mzimu Woyera, imene ili mwa iye amene akumudzodzayo.

61 Akulu angapo opanga mpingo uno akuyenera kukumana mu msonkhano waukulu kamodzi mu miyezi itatu, kapena kwa nthawi ndi nthawi pamene msokhano wanenedwawo udzatsogolera kapena kusankha;

62 Ndipo misonkhano yanenedwayo idzachita chilichonse chokhudza mpingo chofunikira kuti chichitike pa nthawiyo.

63 Akulu akuyenera kulandira chilolezo chawo kuchokera kwa akulu ena, pa chisankho cha mpingo umene iwo ali, kapena kuchokera ku msonkhano waukulu.

64 Wansembe aliyense, mphunzitsi, kapena dikoni, amene wadzodzedwa ndi wansembe, angathe kutenga chiphaso kuchokera kwa iyeyo pa nthawiyo, chiphasocho, chikaonetsedwa kwa mkulu, chidzamuyenereza iye ku chilolezo, chimene chidzamuloleza iye kugwira ntchito za maitanidwe ake, kapena akhonza kuchilandira kuchokera ku msonkhano waukulu.

65 Palibe munthu akuyenera kudzodzedwa ku udindo uliwonse mu mpingo uwu, pamene pali kale nthambi yokhazikitsidwa yofafana, opanda chisankho cha mpingowo;

66 Koma akulu otsogolera, mabishopu oyendera, alangizi akuluakulu, ansembe aakulu, ndi akulu, akhonza kukhala ndi mwayi wodzodza, pamene palibe nthambi ya mpingo kuti chisankho chitha kuitanitsidwa.

67 Mtsogoleri aliyense wa unsembe aakulu (kapena mkulu otsogolera), bishopu, mlangizi wamkulu, ndi wansembe wamkulu, akuyenera kudzodzedwa ndi utsogoleri wa bungwe lalikulu kapena msonkhano waukulu.

68 Ntchito ya mamembala atatha kulandiridwa kudzera mu ubatizo—Akulu kapena ansembe akuyenera kukhala ndi nthawi yokwanira kufotokozera zinthu zonse zokhudza mpingo wa Khristu mwa kumvetsa kwawo, asadayambe kulandira mgonero wawo ndi kutsimikiziridwa mwa kusanjikidwa ndi manja a akuluakulu, kuti zinthu zonse zikathe kuchitika mu ndondomeko.

69 Ndipo mamembala adzaonetsa pamaso pa mpingo, ndiponso pamaso pa akulu, mwa mayendedwe aumulungu ndi kukambirana, kuti iwo ali woyenerera, kuti pakathe kukhala ntchito ndi chikhulupiliro chovomelezedwa ku malembo woyera—kuyenda mu chiyelo pamaso pa Ambuye.

70 Membala aliyense wa mpingo wa Khristu wokhala ndi ana akuyenera kuwabweretsa iwo kwa akulu pamaso pa mpingo, amene akuyenera kusanjika manja awo pa iwo mu dzina la Yesu Khristu, ndi kuwadalitsa mudzina lake.

71 Palibe amene angalandiridwe mu mpingo wa Khristu pokhapokha iye atafika dzaka zokutha kuyankha mulandu pamaso pa Mulungu, ndipo ndiwothekera kulapa.

72 Ubatizo ukuyenera kuperekedwa mu njira yotsatirayi kwa onse amene alapa—

73 Munthu amene waitanidwa ndi Mulungu ndipo ali ndi ulamuliro kuchokera kwa Yesu Khristu kuti abatize, adzalowa m’madzi ndi munthu amene wadzionetsera yekha ku ubatizo, ndipo adzati, kumuitana iye ndi dzina: Pokhala wotumidwa ndi Yesu Khristu, ndikukubatiza iwe mu dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera. Ameni.

74 Kenako iye adzamumiza iye m’madzi, ndi kumutulutsanso m’madzi.

75 Ndi kofunikira kwambiri kuti mpingo udzikumana pamodzi kawiri kawiri kulandira mkate ndi vinyo pokumbukira Ambuye Yesu.

76 Ndipo mkulu kapena wansembe adzaupereka; ndipo potsatira machitidwe awa iye adzaupereka—iye adzagwada limodzi ndi mpingo ndi kuitana dzina la Atate mu pemphero la ulemu kunena:

77 O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa mkate uwu kwa miyoyo ya onse amene adye mkatewu; kuti adye pokumbukira thupi la Mwana wanu, ndi kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti iwo ndiwofunitsitsa kutenga pa iwo dzina la Mwana wanu, ndi kumukumbukira iye nthawi zonse, ndikusunga malamulo ake amene iye wapereka kwa iwo, kuti akathe kukhala nawo Mzimu wake nthawi zonse. Ameni.

78 Mchitidwe operekera vinyo—iye adzatenganso chikho, nati:

79 O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani, m’dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa vinyo uyu ku miyoyo ya onse amene amwamo, kuti athe kuchita ichi pokumbukira mwazi wa Mwana wanu, umene udakhetsedwa chifukwa cha iwo; kuti akathe kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu; Atate Wamuyaya, kuti amukumbukire iye nthawi zonse, kuti akathe kukhala ndi Mzimu wake nthawi zonse kukhala nawo. Ameni.

80 Membala wina aliyense wa mpingo wa Khristu wolakwira, kapena amene wapezaka wolakwa, adzachitiridwa monga malembo amatsogolera.

81 Idzakhala ntchito ya mipingo ingapo, yopanga mpingo wa Khristu, kutumiza m’modzi kapena angapo mwa aphunzitsi awo kukakhala nawo pa misonkhano yaikulu yopangidwa ndi akulu a mpingo.

82 Ndi mndandanda wa maina a mamembala ambiri kugwirizana okha ndi mpingo kuchokera ku msonkhano waukulu wam’mbuyo; kapena kutumiza pa dzanja la ansembe ena; kuti mndandanda wa maina onse a mpingo wonse akathe kusungidwa mu buku ndi m’modzi mwa akulu, aliyense amene akulu enawo adzamusankhe ku nthawi ndi nthawi.

83 Ndiponso, ngati ena achotsedwa mu mpingo, kotero maina awo akhonza kuchotsedwa mu kalembera wa maina a mpingo.

84 Mamembala onse ochokera ku mpingo komwe iwo amakhala, ngati akupita ku mpingo komwe sakudziwidwa, akhonza kutenga kalata yovomeleza kuti iwo ndi mamembala ndipo ali mu ubwezi wabwino, imene kalata yake ikhonza kusainidwa ndi Mkulu kapena wansembe ngati membala akuilandira kalatayo ndi odziwika kwa mkuluyo kapena wansembeyo, kapena ikhonza kusainidwa ndi mphunzitsi kapena dikoni wa mpingowo.