Gawo 47
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Malichi 8, 1831. John Whitmer, yemwe adali atatumikira kale ngati kalaliki kwa Mneneri, poyambilira adazengereza pamene adapemphedwa kuti agwire ntchito ngati wolemba mbiri ya Mpingo ndi mlembi, kulowa m’malo mwa Oliver Cowdery. Iye adalemba kuti: “Ndikadakonda kusachichita koma kuona kuti chifuniro cha Ambuye chichitike, ndipo ngati akufuna, ndimafuna kuti achionetse kudzera mwa Joseph wamasomphenyayo.” Joseph Smith atatha kulandira vumbulutsoli, John Whitmer adavomera ndipo adatumikira mu udindo wake wosankhidwa.
1–4, John Whitmer adasankhidwa kusunga mbiri ya Mpingo ndi kulembera Mneneri.
1 Taona, ndi koyenera mwa ine kuti mtumiki wanga John alembe ndi kusunga mbiri yakale yokhazikika, ndi kuthandiza iwe, mtumiki wanga Joseph, mu kulemba zinthu zonse zimene zidzapatsidwa kwa iwe, kufikira iye ataitanidwa ku ntchito zina.
2 Ndiponso, indetu ndinena kwa iwe kuti iye akhozanso kukweza mawu ake m’misonkhano, pamene kudzakhala koyenera.
3 Ndiponso, ndinena kwa inu kuti kudzasankhidwa kwa iye kusunga zolemba za mpingo ndi mbiri yakale mosalekeza; pakuti Oliver Cowdery ndamusankhira ku udindo wina.
4 Kotero, chidzapatsidwa kwa iye, pamene ali wokhulupirika, kudzera mwa Mtonthozi, kulemba zinthu izi. Ngakhale zili choncho. Ameni.