Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 31


Gawo 31

Vumbulutso loperekedwa kudzera kwa Joseph Smith Mneneri kwa Thomas B. Marsh, Seputembera 1830. Mwambowu udangotsatira msonkhano wa Mpingo (onani mutu wa gawo 30). Thomas B. Marsh adali atabatizidwa kumayambiliro kwa mweziwo ndipo adadzodzedwa kukhala mkulu mu Mpingo vumbulutso ili lisadaperekedwe.

1–6Thomas B. Marsh aitanidwa kukalalikira uthenga wabwino ndipo atsimikiziridwa za chisamaliro cha banja lake; 7–13, Iye alangizidwa kukhala wopilira, kupemphera nthawi zonse, ndi kutsatira Mtonthozi.

1 Thomas, mwana wanga, wodala ndiwe chifukwa cha chikhulupiliro chako mu ntchito yanga.

2 Taona, udali nazo zowawa zambiri chifukwa cha banja lako; komabe, ndidzakudalitsa iwe ndi banja lako, inde, ana ako aang’ono; ndipo tsiku likudza loti adzakhulupilira ndi kudziwa choonadi ndi kukhala limodzi ndi iwe mu mpingo wanga.

3 Kweza mtima wako ndipo sangalala, pakuti ola la utumiki wako lafika; ndipo lilime lako lidzamasulidwa, ndipo udzalalikira uthenga wabwino wa chisangalalo chachikulu kwa m’badwo uno.

4 Iwe udzalengeza zinthu zimene zaululidwa kwa mtumiki wanga, Joseph Smith, Jun. Udzayamba kulalikira kuyambira nthawi ino kupita m’tsogolo, inde, kukolola m’munda umene mwacha kale kuti muwotchedwe.

5 Kotero, ponya chikwakwa chako ndi moyo wako wonse, ndipo machimo ako akhululukidwa, ndipo udzasenza mitolo pamsana pako, pakuti wantchito akuyenera kulandira malipiro ake. Kotero, banja lako lidzakhala ndi moyo.

6 Taona, indetu, ndinena kwa iwe, choka kwa iwo kwa kanthawi kochepa, ndipo lalikira mawu anga, ndipo ine ndidzawakonzera iwo malo.

7 Inde, ndidzatsegula mitima ya anthu, ndipo adzakulandira iwe. Ndipo ndidzakhazikitsa mpingo ndi dzanja lako;

8 Ndipo iwe udzawalimbikitsa ndi kuwakonzekeretsa iwo pa nthawi imene adzasonkhanitsidwa.

9 Pilira m’masautso, usanyoze amene akukunyoza; Lamulira nyumba yako mofatsa, ndipo khala okhazikika.

10 Taona, ndinena kwa iwe kuti udzakhala dotolo kwa mpingo, koma osati kwa dziko, pakuti iwo sadzakulandira iwe.

11 Pita kulikonse kumene ndikufuna, ndipo Mtonthozi adzakupatsa iwe zimene ukuyenera kuchita ndi kumene utadzapite.

12 Pemphera nthawi zonse, kuopa kuti ungalowe m’mayesero ndi kutaya mphotho yako.

13 Khala wokhulupirika kufikira chimaliziro, ndipo taona, ine ndili ndi iwe. Mawu awa si a munthu kapena a anthu, koma a ine, ngakhale Yesu Khristu, Muwomboli wako, mwa chifuniro cha Atate. Ameni.