Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 104


Gawo 104

Vumbulutso loperekedwa kwa Mneneri Joseph Smith, ku Kirtland, Ohio, Epulo 23, 1834, zokhudzana ndi United Firm (onani mitu ya magawo 78 ndi 82). Mwachidziwikire chochitikacho chidali cha msonkhano wa bungwe la mamembala a United Firm, umene udakambirana za zosoweka zaku thupi za Mpingo. Msonkhano woyamba wa kampaniyo pa Epulo 10 udatsimikiza kuti bungweli lithe. Vumbulutso ili likutsogoza kuti kampaniyo m’malomwake ikonzedwenso; katundu wake adayenera kugawidwa pakati pa mamembala a kampani monga adindo awo Motsogozedwa ndi Joseph Smith, mawu akuti “United Firm” adasinthidwa ndi “gulu logwirizana” mu vumbulutso.

1–10, Oyera mtima amene alakwira bungwe lamgwirizano adzatembeleredwa; 11–16, Ambuye amasamalira Oyera mtima Ake mu njira Yake; 17–18, Lamulo la Uthenga Wabwino limalamula chisamaliro cha osauka; 19–46, Maudindo ndi madalitso a abale osiyanasiyana aikidwiratu; 47–53, Bungwe lamgwirizano mu Kirtland ndi order mu Ziyoni zikuyenera kugwira ntchito mosiyana; 54–66, thumba la chuma chopatulika cha Ambuye likhazikitsidwa kuti chitsindikizire malembo opatulika; 67–77, Chuma chonse cha bungwe lamgwirizano chikuyenera kugwiritsidwa ntchito pamaziko a kuvomereza kwa onse; 78–86, Iwo ali mu gulu logwirizana akuyenera kulipira ngongole zawo zonse, ndipo Ambuye adzawawombola iwo ku ukapolo wa chuma.

Indetu ndikunena kwa inu, abwenzi anga, ndikupereka kwa inu uphungu, ndi lamulo, zokhudzana ndi katundu yense wa mgwirizano limene ndidalamula kuti likonzedwe ndi kukhazikitsidwa, kuti likhale gulu logwirizana, ndi gulu lamuyaya la phindu la mpingo wanga, ndi la chipulumutso cha anthu kufikira ine ndidzabwere—

Ndi kulonjeza lokhazikika ndi losasinthika, kuti monga momwe iwo amene ndidawalamula adali okhulupirika iwo akuyenera kudalitsidwa ndi madalitso ochuluka;

Koma popeza iwo sadali okhulupirika adali pafupi kutembeleredwa.

Kotero, popeza kuti ena a atumiki anga sadasunge lamulo, koma aphwanya pangano mwa kusilira kwa nsanje, ndi mawu onyenga, ine ndawatembelera iwo ndi thembelero lowawa ndi lopweteka kwambiri.

Pakuti ine, Ambuye ndalamula mu mtima mwanga, kuti pamene munthu ali yense wa order adzapezedwa wolakwa, kapena, m’mawu ena, adzaphwanya pangano limene mwamangidwa nalo, iye adzatembeleredwa m’moyo wake, ndipo adzaponderezedwa ndi amene ndifuna;

Pakuti ine, Ambuye, sindikuyenera kunyozedwa mu zinthu izi—

Ndipo zonsezi kuti osalakwa asalangidwe pakati panu pamodzi ndi osalungama; ndipo kuti asapulumuke ochimwa pakati panu; chifukwa ine, Ambuye, ndalonjeza kwa inu korona wa ulemelero pa dzanja langa lamanja.

Kotero, popeza mwapezeka olakwa, simungathe kuthawa mkwiyo wanga m’miyoyo yanu.

Pamene inu mwadulidwa chifukwa cha kulakwa, simungathawe madyelero a Satana kufikira tsiku la chiwombolo.

10 Ndipo tsopano ndikupereka kwa inu mphamvu kuyambira ola lomwelino, kuti ngati munthu aliyense wa inu, wa mu order, adzapezedwa wolakwa ndipo sadzalapa pa choipacho, kuti mudzampereke iye ku madyelero a Satana; ndipo sadzakhala ndi mphamvu yakubweretsa pa inu choipa.

11 Ndi nzeru mwa ine; kotero, lamulo ndikupereka kwa inu, kuti mudzadzilinganiza nokha ndi kusankha munthu aliyense udindo wake;

12 kuti munthu aliyense adzathe kupereka tsatanetsatane kwa ine wa udindo umene udaikidwa kwa iye.

13 Pakuti ndi koyenera kuti ine, Ambuye, ndipange munthu aliyense kuyankha, monga mdindo pa madalitso a dziko lapansi, amene ndawapanga ndi kukonzera zolengedwa zanga.

14 Ine Ambuye, ndidatambasula kumwamba, ndipo ndidamanga dziko lapansi, ntchito ya manja anga; ndipo zinthu zonse zili m’menemo ndi zanga.

15 Ndipo ndicholinga changa kupezera oyera mtima anga, pakuti zinthu zonse ndi zanga.

16 Koma zikuyenera zichitike mu njira yanga; ndipo taonani, iyi ndi njira yomwe ine, Ambuye, ndalamula kuti ndiwapezere oyera mtima anga, kuti aumphawi adzakwezedwa, mokuti olemera atsitsidwe.

17 Pakuti dziko lapansi ndi lodzaza, ndipo pali zokwanira ndi zosungidwa; inde, ndidakonza zinthu zonse, ndipo ndapereka kwa ana a anthu kuti akhale othandizira kwa iwoeni.

18 Kotero, ngati munthu aliyense atenge za zochuluka zimene ndapanga, ndi kusapereka gawo lake, molingana ndi lamulo la uthenga wanga wabwino, kwa osauka ndi osowa, iye, pamodzi ndi oipa, adzakweza maso ake mu gahena, ali m’mazunzo.

19 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu, zokhudzana ndi katundu wa order—

20 Lolani mtumiki wanga Sidney Rigdon asankhe kwa iye malo kumene iye tsopano akhala, ndi malo ofufutira zikopa chifukwa cha udindo wake, kaamba ka chisamaliro chake pamene iye akugwira ntchito m’munda wanga wa mpesa, ngakhale monga momwe ine ndidzamulamulire iye.

21 Ndipo lolani zinthu zonse zichitike molingana ndi uphungu wa bungwe, ndi chilolezo chogwirizana kapena mawu a dongosolo, omwe akukhala m’dziko la Kirtland.

22 Ndipo udindowu ndi madalitso awa, ine, Ambuye, ndapereka pa mtumiki wanga Sidney Rigdon kuti am’dalitse iye, ndi mbewu yake pambuyo pake;

23 Ndipo ndidzachulukitsa madalitso pa iye, monga momwe adzadzichepetsere pamaso panga.

24 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Martin Harris asankhe kwa iye, chifukwa cha udindo wake, gawo la malo limene mtumiki wanga John Johnson adalandira mosinthanitsa ndi cholowa chake chakale, kwa iye ndi mbewu yake pambuyo pake;

25 Ndipo pamene ali wokhulupirika, ndidzachulukitsa madalitso pa iye ndi mbewu yake pambuyo pake.

26 Ndipo lolani mtumiki wanga Martin Harris apereke ndalama zake kuti zilengezere mawu anga, molingana ndi momwe mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., adzatsogolere.

27 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Frederick G. Williams akhale pa malo amene tsopano lino akukhala.

28 Ndipo lolani mtumiki wanga Oliver Cowdery akhale ndi malo amene ayambika kulumikiza nyumba, amene adzakhala a ofesi yotsindikiza, omwe ali malo oyamba, ndiponso malo amene atate ake amakhala.

29 Ndipo lolani atumiki anga Frederick G. Williams ndi Oliver Cowdery akhale ndi ofesi yotsindikizira ndi zinthu zonse zokhudzana nayo.

30 Ndipo uwu udzakhala udindo wawo umene udzaikidwa kwa iwo.

31 Ndipo pamene iwo ali okhulupirika, taonani, ndidzawadalitsa, ndi kuchulukitsa madalitso pa iwo.

32 Ndipo ichi ndi chiyambi cha udindo umene ndawaikira iwo, ndi kwa mbewu yawo pambuyo pawo.

33 Ndipo, pamene iwo ali okhulupirika, ine ndidzachulukitsa madalitso pa iwo ndi mbewu yawo pambuyo pawo, ngakhale kuchuluka kwa madalitso.

34 Ndiponso, lolani mtumiki wanga John Johnson akhale ndi nyumba imene iye akukhala, ndi cholowa, zonse kusiyapo malo amene asungidwa kaamba ka kumanga nyumba zanga, zimene zili za cholowa chimenecho, ndi malo aja amene atchulidwa a mtumiki wanga Oliver Cowdery.

35 Ndipo pamene ali wokhulupirika, ndidzachulukitsa madalitso pa iye.

36 Ndipo ndi chifuniro changa kuti agulitse malo amene aikidwa kuti amange mzinda wa oyera mtima anga, kotero kuti adzadziwika kwa iye ndi liwu la Mzimu, ndi molingana ndi uphungu wa dongosolo, ndi mawu a dongosolo.

37 Ndipo ichi ndi chiyambi cha udindo umene ndauika kwa iye, kuti ukhale mdalitso kwa iye ndi mbewu yake pambuyo pake.

38 Ndipo monga momwe iye ali wokhulupirika, ine ndidzachulukitsa kuchulukitsa kwa madalitso pa iye.

39 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Newel K. Whitney amuikire kwa iye nyumba ndi malo kumene akukhala tsopano, ndi malo ndi nyumba yomwe mercantile establishment yaima, komanso malo omwe ali pamphambano kumwera kwa mercantile establishment, komanso malo omwe asheri ili.

40 Ndipo zonsezi ndaziika kwa mtumiki wanga Newel K. Whitney pa udindo wake, pa dalitso pa iye ndi mbewu yake pambuyo pake, mu ubwino wa mercantile establishment kwa bungwe langa limene ndalikhazikitsa ku Siteki yanga m’dziko la Kirtland.

41 Inde, ndithudi, uwu ndi udindo umene ndauika kwa mtumiki wanga N. K. Whitney, ngakhale mercantile establishment yonseyi, iye ndi wothandizira wake, ndi mbewu yake pambuyo pake.

42 Ndipo pamene ali wokhulupirika pakusunga malamulo anga, amene ndapereka kwa iye, ndidzachulukitsa madalitso pa iye ndi mbewu yake pambuyo pake, ngakhale madalitso ochuluka.

43 Ndiponso, lolani mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., amupangire iye malo amene aikidwa omangira nyumba yanga, amene ndi mizati makumi anayi m’litali mwake, ndi kupingasa kwake khumi ndi ziwiri, ndiponso cholowa chimene atate ake akukhalapo tsopano;

44 Ndipo ichi ndi chiyambi cha udindo umene ine ndidawuika kwa iye, kwa mdalitso pa iye, ndi pa atate ake.

45 Pakuti, taonani, ndasungira atate ake cholowa, pa chithandizo chawo, kotero adzawerengedwa m’nyumba ya mtumiki wanga Joseph Smith, Jun.

46 Ndipo ndidzachulukitsa madalitso pa nyumba ya mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., pamene ali wokhulupirika, ngakhale madalitso ochuluka.

47 Ndipo tsopano, lamulo ndipereka kwa inu lokhudzana ndi Ziyoni, kuti simudzakhalanso monga gulu logwirizana kwa abale anu a Ziyoni, mwa njira iyi yokha—

48 Pambuyo pa kukonzedwa kwanu, mudzatchedwa Bungwe Logwirizana la siteki ya ziyoni Mzinda wa Kirtland. Ndipo abale anu, pambuyo pakukonzedwa kwawo, adzatchedwa gulu ligwirizana la pa Siteki ya Ziyoni.

49 Ndipo iwo adzakonzedwa mu maina awo, ndi mudzina lawo; ndipo adzachita malonda awo mu dzina lawo, ndi mu maina awo;

50 Ndipo mudzichita malonda anu m’dzina lanu, ndi mu maina a anu.

51 Ndipo izi ndalamula kuti zichitike pa chipulumutso chanu, ndiponso pa chipulumutso chawo, chifukwa cha kuthamangitsidwa kwawo ndi chimene chili nkudza.

52 Mapangano akuphwanyidwa kudzera mu cholakwa, mwa kusilira ndi mawu onyenga—

53 Kotero, inu mukuthetsedwa monga gulu logwirizana ndi abale anu, kuti simuli womangidwa kokha mpaka ola lino kwa iwo, mwa njira iyi yokha, monga ine ndidati, ndi ngongole monga adzagwirizana ndi order iyi mu bungwe, monga nyengo zanu zidzavomereza ndi mawu a bungwe kutsogolera.

54 Ndiponso, lamulo ine ndikupereka kwa inu lokhudzana ndi udindo wanu umene ine ndauika kwa inu.

55 Taonani, akatundu onse awa ndi anga, kapena chikhulupiliro chanu chili chabe, ndipo mudzapezedwa onyenga, ndi mapangano amene mwapanga kwa ine aphwanyidwa;

56 Ndipo ngati katundu ali wanga, ndiye kuti ndinu adindo; apo ayi simuli adindo.

57 Koma, indetu, ndikunena kwa inu, ndakuikani inu kukhala adindo a pa nyumba yanga, ngakhale adindo ndithu.

58 Ndipo chifukwa cha cholinga ichi ndakulamulani kuti mudzikonze nokha, ngakhale kutsindikiza mawu anga, chidzalo cha malemba anga, mavumbulutso omwe ndidapereka kwa inu, ndipo omwe ndidzapereka, kuyambira nthawi ino, ndi ku nthawi ndi nthawi ndidzakhala ndikukupatsani—

59 Ndi cholinga chomanga mpingo wanga ndi ufumu wanga padziko lapansi, ndi kukonzekeretsa anthu anga ku nthawi yomwe ndidzakhala nawo, yomwe ili pafupi.

60 Ndipo mudzadzikonzekere malo osungira chuma, ndipo mudzamupatulira mu dzina langa.

61 Ndipo mudzaika m’modzi pakati panu kuti asunge thumba la chuma, ndipo iye adzadzodzedwa ndi mdalitsowo.

62 Ndipo padzakhale chidindo pa thumba lachumalo, ndipo zinthu zonse zopatulika zidzaperekedwe ku thumba lachumalo; ndipo pasadzapezeke munthu pakati panu wolitcha kuti ndi lake, kapena gawo lake lililonse, chifukwa lidzakhala la nonse mogwirizana.

63 Ndipo ndapereka kwa inu kuyambira nthawi ino; ndipo tsopano onetsetsani, kuti mupite kukagwiritsa ntchito udindowo umene ndauika kwa inu, wa zinthu zopatulikazo, pa cholinga chosindikizira zinthu zopatulikazo monga ndanenera.

64 Ndipo phindu la zinthu zopatulikazo lidzaikidwa ku thumba la chumalo, ndipo chidindo chidzakhalapo; ndipo sichidzagwiritsidwa ntchito kapena kuchotsedwa kuthumbalo ndi aliyense, kapena chidindocho sichidzamatulidwa chimene chitadzaikidwe pamenepo, ndi mawu okha a dongosolo, kapena ndi lamulo.

65 Ndipo kotero inu mudzasunga phindu la zinthu zopatulikazo mu thumba la chuma, pa zolinga zopatulika ndi zoyera.

66 Ndipo ichi chidzatchedwa chuma chopatulika cha Ambuye; ndipo chidindo chidzaikidwa pa icho kuti chikathe kukhala choyera ndi chopatulidwira kwa Ambuye.

67 Ndiponso, padzakhala thumba lina lokonzedwa, ndipo msungichuma adzasankhidwa kuti asunge chumacho, ndipo chidindo chidzaikidwa pamenepo;

68 Ndipo ndalama zonse zomwe mumalandira mu maudindo anu, pokonzanso katundu yemwe ndakupatsani, mu nyumba, kapena mu minda, kapena ng’ombe, kapena mu zinthu zonse kupatula zolemba zoyera ndi zopatulika, zomwe ndadzisungira ndekha ku zolinga zoyera ndi zopatulika, zidzaponyedwa ku thumba la chumalo mwamsanga pamene mukulandira ndalamazo, mwa mazana, kapena mwa makumi asanu, kapena mwa makumi awiri, kapena mwa khumi, kapena mwa zisanu.

69 Kapena m’mawu ena, ngati munthu aliyense pakati panu apeza madola asanu mloleni awaponye ku thumba la chuma; kapena akalandira khumi, kapena makumi awiri, kapena makumi asanu, kapena zana, achite momwemo;

70 Ndipo musalore aliyense mwa inu anene kuti ndi zake zokha; pakuti sizidzatchedwa zake, ngakhale gawo lililonse la izo.

71 Ndipo sipadzakhala gawo lililonse la izo logwiritsidwa ntchito, kapena kuchotsedwa kuthumba lachuma, koma mwa mawu okha ndi kuvomereza kwa onse kwa dongosolo.

72 Ndipo awa adzakhala mawu ndi kuvomereza kwa onse kwa dongosolo—kuti wina wa inu adzanena kwa msungichuma: ndikusowa ichi kuti chindithandize mu udindo wanga—

73 Ngati ndi madola asanu, kapena ngati ndi madola khumi, kapena makumi awiri, kapena makumi asanu, kapena zana limodzi, msungichuma adzampatse ndalama zimene akufunazo kuti zimuthandize pa udindo wake—

74 Kufikira atapezeka kuti ndi wolakwa, ndipo kudzaonekera pamaso pa akuluakulu a bungwe la order poyera kuti iye ndi mdindo wosakhulupirika ndi wopanda nzeru.

75 Koma ngati iye ali mu chiyanjano chathunthu, ndipo ali wokhulupirika ndi wanzeru mu udindo wake, ichi chidzakhala chizindikiro chake kwa msungichuma kuti msungichuma sadzamukaniza.

76 Koma pakakhala kulakwa, msungichuma adzamvera bungwe ndi liwu la dongosolo.

77 Ndipo ngati msungichuma apezedwa kuti ndi mdindo wosakhulupirika ndi wopanda nzeru, akuyenera kumvera bungwe ndi mawu a dongosolo, ndipo adzachotsedwa m’malo mwake, ndipo wina adzaikidwa m’malo mwake.

78 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, zokhudzana ndi ngongole zanu—taonani ndi chifuniro changa kuti mudzalipira ngongole zanu zonse.

79 Ndipo ndi chifuniro changa kuti mudzichepetse pamaso panga, ndi kulandira dalitso ili mwa kulimbikira kwanu ndi kudzichepetsa kwanu ndi pemphero la chikhulupiliro.

80 Ndipo pamene muli olimbikira ndi odzichepetsa, ndi kupemphera pemphero la chikhulupiliro, taonani, ndidzafewetsa mitima ya iwo amene muli nawo ngongole, mpaka ndidzatumiza njira kwa inu ya chipulumutso chanu.

81 Kotero lembelani mofulumira ku New York ndipo lembani molingana ndi icho chimene chidzanenedwa ndi Mzimu wanga; ndipo ndidzafewetsa mitima ya iwo amene muli nawo ngongole, kuti idzachotsedwa m’maganizo mwawo ku kubweretsa masautso pa inu.

82 Ndipo pamene muli odzichepetsa ndi okhulupirika ndi kuitanira pa dzina langa, taonani, ndikupatsani chigonjetso.

83 Ine ndikupereka kwa inu lonjezo, kuti inu mudzawomboledwa kamodzi kokhaka kuchokera mu ukapolo wanu.

84 Pamenemwapeza mwayi wobwereketsa ndalama mazana, kapena mazanamazana, ngakhale mpaka mutabwereketsa kuti mudzipulumutse kuukapolo, ndimwayi wanu.

85 Ndipo lonjezani katundu amene ndaika m’manja mwanu, kamodzi kokhaka, pa kupereka mayina anu mwa kuvomerezana kwa onse kapena mwanjira ina, monga zidzakhala zabwino kwa inu.

86 Ine ndikupatsani inu mwayi uwu, kamodzi kokhaka; ndipo taonani, ngati mupitilira kuchita zinthu zimene ndaziika patsogolo panu, molingana ndi malamulo anga, zinthu zonsezi ndi zanga, ndipo inu ndinu adindo anga, ndipo mbuye sadzalola kuti nyumba yake ithyoledwe. Ngakhale choncho. Ameni.