Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 35


Gawo 35

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Fayette, New York, Disembara 7, 1830. Pa nthawiyi, Mneneriyu ankagwira ntchito yomasulira Baibulo pafupifupi tsiku lililonse. Kumasulilako kudayambika kumayambiliro kwa Juni 1830, ndipo onse Oliver Cowdery ndi John Whitmer adatumikira monga alembi. Popeza tsopano adali ataitanidwa ku ntchito zina, Sidney Rigdon adaitanidwa ndi kusankhidwa kwaumulungu kuti akhale mlembi wa Mneneri pa ntchitoyi (onani ndime 29). Monga mawu oyamba ku zolembedwa za vumbulutsoli, mbiri ya Joseph Smith ikunena: “Mu Disembala Sidney Rigdon adabwera [kuchokera ku Ohio] kudzafunsa kwa Ambuye, ndipo ndi iye adabwera Edward Partridge. … Abale awiriwa atangofika kumene, Ambuye adayankhula motere.”

1–2, Momwe anthu angakhalile ana a Mulungu; 3–7, Sidney Rigdon aitanidwa kuti akabatize ndi kuti akapereke Mzimu Woyera; 8–12, Zizindikiro ndi zozizwitsa zimachitidwa mwa chikhulupiliro; 13–16, Atumiki a Ambuye adzapuntha mafuko ndi mphamvu ya Mzimu; 17–19, Joseph Smith ali ndi mafungulo a zinsinsi; 20–21, Osankhidwa adzadikila tsiku la kudza kwa Ambuye; 22–27, Israeli adzapulumutsidwa.

1 Mvetserani ku mawu a Ambuye Mulungu wanu, ngakhale Alefa ndi Omega, oyamba ndi otsiriza, amene njira yake ndi kuzungulira kwamuyaya, yemweyo lero monga dzulo, ndi kunthawi zonse.

2 Ine ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene adapachikidwa chifukwa cha machimo adziko lapansi, ngakhale onse amene adzakhulupilira dzina langa, kuti akathe kukhala ana a Mulungu, ngakhale m’modzi mwa ine monga ine ndili m’modzi mwa Atate, monga Atate ali m’modzi mwa ine, kuti tikathe kukhala amodzi.

3 Taona, indetu, indetu, ndinena kwa mtumiki wanga Sidney, ndayang’ana pa iwe ndi ntchito zako. Ndamva mapemphero ako, ndipo ndakukonzeketsa iwe ku ntchito yokulirapo.

4 Ndiwe wodala, pakuti iwe udzachita zinthu zazikulu. Taona iwe udatumidwa, inde monga Yohane, kukakonza njira patsogolo panga, ndi patsogolo pa Eliya amene akuyenera kubwera, ndipo iwe sudazidziwe izi.

5 Iwe udabatiza ndi madzi ku kulapa, koma iwo sadalandire Mzimu Woyera;

6 Koma tsopano ine ndikupatsa iwe lamulo, kuti iwe udzabatiza ndi madzi, ndipo iwo adzalandira Mzimu Woyera mwa kusanjika kwa manja, ngakhale monga atumwi akale.

7 Ndipo zidzachitika kuti kudzakhala ntchito yaikulu m’dzikolo, ngakhale pakati pa Amitundu, pakuti kupusa kwawo ndi zonyansa zawo zidzaonetsedwa m’maso mwa anthu onse.

8 Pakuti ine ndine Mulungu, ndipo dzanja langa silifupika; ndipo ndidzasonyeza zozizwitsa, zizindikiro, ndi zodabwitsa, kwa onse amene amakhulupilira m’dzina langa.

9 Ndipo amene adzapempha m’dzina langa ndi chikhulupiliro, iwo adzatulutsa ziwanda; iwo adzachilitsa odwala; iwo adzachititsa akhungu kuona, ndi ogontha kumva, osayankhula kuyankhula, ndi olumala kuyenda.

10 Ndipo nthawi ikudza mofulumira imene zinthu zazikulu zikuyenera kuonetsedwa kwa ana a anthu;

11 Koma popanda chikhulupiliro palibe chimene chidzaonetsedwe kupatula zipululu pa Babulo, yemweyo amene wapangitsa mitundu yonse kumwa vinyo wa mkwiyo wa dama lake.

12 Ndipo palibe amene amachita zabwino kupatula iwo amene ali okonzeka kulandira chidzalo cha uthenga wabwino wanga, umene ndidatumiza kwa m’badwo uno.

13 Kotero, ndikuitanira pa zinthu zofowoka za dziko lapansi, iwo amene ali osaphunzira ndi onyozedwa, kuti aphwanye mitundu ya anthu ndi mphamvu ya Mzimu wanga;

14 Ndipo mkono wawo udzakhala mkono wanga, ndipo ine ndidzakhala chishango chawo ndi chishango cham’mikono chawo; ndipo ine ndidzamanga m’chuuno mwawo, ndipo iwo adzandimenyera nkhondo mwamphamvu; ndipo adani awo adzakhala pansi pa mapazi awo; ndipo ndidzalora kuwagwetsera lupanga m’malo mwawo, ndipo ndi moto wa ukali wanga ndidzawapulumutsa iwo.

15 Ndipo osauka ndi ofatsa adzalalikidwa uthenga wabwino kwa iwo, ndipo adzakhala akuyang’anira nthawi ya kudza kwanga, pakuti ili pafupi—

16 Ndipo iwo adzaphunzira fanizo la mtengo wa mkuyu, pakuti ngakhale tsopano chirimwe chili pafupi.

17 Ndipo ndatumiza chidzalo cha uthenga wanga wabwino kudzera mu dzanja la mtumiki wanga Joseph; ndipo mu kufooka ndamudalitsa iye;

18 Ndipo ndapereka kwa iye mafungulo a chinsinsi cha zinthu zomwe zidasindikizidwa, ngakhale zinthu zomwe zidali kuchokera ku maziko a dziko, ndi zinthu zomwe zidzabwera kuchokera nthawi ino mpaka nthawi ya kubwera kwanga, ngati akhala mwa ine, ndipo ngati satero, ndidzadzala wina m’malo mwake.

19 Kotero, mumuyang’anile iye kuti chikhulupiliro chake chisalephele, ndipo chidzaperekedwa ndi Mtonthozi, Mzimu Woyera, amene amadziwa zinthu zonse.

20 Ndipo lamulo ine ndikupereka kwa iwe—kuti iwe udzamulembera iye; ndipo malembo adzaperekedwa, inde monga ali m’chifuwa changa chomwe, kwa chipulumutso cha osankhidwa anga;

21 Pakuti iwo adzamva mawu anga, ndipo adzandiona ine, ndipo sadzagona, ndipo adzadikira tsiku la kudza kwanga; pakuti adzayeretsedwa, monga ine ndili woyera.

22 Ndipo tsopano ndinena kwa iwe, khala naye, ndipo adzayenda pamodzi ndi iwe; usamusiye iye, ndipo ndithudi zinthu izi zidzakwaniritsidwa.

23 Ndipo pamene iwe sulemba; taona, kudzapatsidwa kwa iye kuti anenere; ndipo iwe udzalalikira uthenga wanga ndi kuitana pa aneneri oyera kuti atsimikizire mawu ake, monga iwo adzapatsidwa kwa iye.

24 Sunga malamulo onse ndi mapangano omwe iwe wamangidwa nawo; ndipo ndidzapangitsa kumwamba kugwedezeka chifukwa cha ubwino wako, ndipo Satana adzanjenjemera, ndipo Ziyoni adzasangalala pamapiri ndi kuphukila;

25 Ndipo Israeli adzapulumutsidwa pa mu nthawi yanga; ndipo ndi mafungulo amene ndapereka iwo adzatsogoledwa, ndipo sadzasokonezedwa konse.

26 Kwezani mitima yanu ndi kusangalala, chiwombolo chanu chayandikira.

27 Musaope, kagulu kankhosa inu, ufumu ndi wanu kufikira ine ndidzabwera. Taonani, ndidza msanga. Ngakhale zili choncho. Ameni.