Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 81


Gawo 81

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Malitchi 15, 1832. Frederick G. Williams aitanidwa kukhala wansembe wamkulu ndi mlangizi wa Atsogoleri a Unsembe Waukulu. Zolemba zakale zikuonetsa kuti pamene vumbulutso ili lidalandiridwa mu Malitchi 1832, lidaitana Jesse Gause ku udindo wa mlangizi kwa Joseph Smith mu Utsogoleri. Komabe, pamene iye adalephera kupitiliza mu njira yogwirizana ndi kusankhidwaku, kuitanidwaku kenako kudasamutsidwira kwa Frederick G. Williams. Vumbulutsolo (tsiku lake Malitchi1832) likuyenera kutengedwa ngati njira yopitira ku kakhazikitsidwe ka Atsogoleri Oyamba kovomelezeka, makamaka kuitana kwa udindo wa mlangizi mu bungwelo ndi kufotokozera ulemu wa kusankhidwako. M’bale Gause adatumikira kwa kanthawi koma adachotsedwa mu Mpingo mu Disembala 1832. M’bale Williams adadzodzedwa ku udindo wapaderawu pa 18 Malitchi, 1833.

1–2, Mafungulo a ufumu amakhala nthawi zonse ndi Atsogoleri Oyamba; 3–7, Ngati Frederick G. Williams ali wokhulupirika mu utumiki wake, iye adzakhala ndi moyo wamuyaya.

Indetu, indetu, ndinena kwa iwe mtumiki wanga Frederick G. Williams: Mvetsera ku mawu a iye amene akuyankhula, ku mawu a Ambuye Mulungu wako, ndipo mvetsera ku maitanidwe amene iwe waitanidwa, ngakhale kukhala wansembe wamkulu mu mpingo wanga, ndi mlangizi kwa mtumiki wanga Joseph Smith, Jun.;

Kwa amene ndapereka mafungulo a ufumu, amene amakhala nthawi zonse kwa atsogoleri a Unsembe Waukulu:

Kotero, indetu ndikumuvomeleza iye ndi kumudalitsa iye, ndiponso iwe, pamene iwe uli okhulupirika mu uphungu, mu udindo umene ndakusankhira kwa iwe, mu pemphero nthawi zonse, mofuula komanso mumtima mwako, pagulu ndi pobisika, komanso mu utumiki wako polengeza uthenga wabwino mu dziko la amoyo, ndi pakati pa abale ako.

Ndipo pokuchita zinthu izi iwe udzachita chabwino chachikulu kwa anthu anzako, ndipo udzakweza ulemelero wa iye amene ali Ambuye wako.

Kotero, khala okhulupirika; ima mu udindo wako umene ine ndakusankhira kwa iwe; thandiza ofooka, kweza manja a iwo amene alema, ndi kulimbikitsa mawondo olefuka.

Ndipo ngati uli wokhulupirika mpaka kumapeto iwe udzakhala ndi korona wa chisavundi, ndi moyo wamuyaya mu nyumba zimene ine ndakonza mu nyumba ya Atate anga.

Taona, ndipo ona, awa ndi mawu a Alefa ndi Omega, ngakhale Yesu Khristu, Ameni.