Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 49


Gawo 49

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Sidney Rigdon, Parley P. Pratt, ndi Leman Copley, ku Kirtland, Ohio, Meyi 7, 1831. Leman Copley adali atalandira uthenga wabwino koma adakakamirabe ku ziphunzitso zina za gulu la Shakers (United Society of Believers in Christ’s Second Appearing), limene iye adali nalo poyamba. Zina mwa zikhulupiliro za a Shakers zidali zakuti Kudza Kwachiwiri kwa Khristu kudali kutachitika kale komanso kuti Iye adaonekera mu maonekedwe a mkazi, Ann Lee. Iwo sankaona ubatizo wa m’madzi kukhala wofunikira. Iwo amakana ukwati ndipo amakhulupilira moyo wa umbeta kotheratu. Ma Shakers ena amaletsanso kudya nyama. Mu kutsogoza vumbulutsoli, mbiri ya Joseph Smith ikuti, “Kuti tikhale ndi kumvetsetsa kokwanira pa nkhaniyi, ndidafunsa kwa Ambuye, ndipo ndidalandira zotsatirazi.” Vumbulutsoli limatsutsa mfundo zina zofunikira za gulu la Shaker. Abale amene tawatchulawo adatenga kope la vumbulutsoli ku gulu la Shaker (pafupi ndi Cleveland, Ohio) ndi kuliwerenga lonse kwa iwo, koma ilo lidakanidwa.

1–7, Tsiku ndi ola la kubwera kwa Khristu zidzakhala zosadziwika kufikira Iye atabwera; 8–14, Anthu akuyenera kulapa, kukhulupilira uthenga wabwino, ndi kumvera malamulo kuti alandire chipulumutso; 15–16, Ukwati ndi wodzodzedwa ndi Mulungu; 17–21, Kudya nyama ndi kovomerezedwa; 22–28, Ziyoni adzaphuka ndipo Alamani adzaphuka ngati duwa pamaso pa Kubwera Kwachiwiri.

1 Mvetserani ku mawu anga, atumiki anga Sidney, ndi Parley, ndi Leman; pakuti taonani, indetu ndinena kwa inu, kuti ndikupereka kwa inu lamulo kuti mudzapita ndi kukalalikira uthenga wanga wabwino umene inu mudaulandira, ngakhale monga inu mudaulandilira iwo, kwa ma Shakers.

2 Taonani, ndinena kwa inu, kuti iwo akufuna kudziwa choonadi pang’ono, koma osati chonse, pakuti iwo sakulondola pamaso panga ndipo akuyenera kulapa.

3 Kotero, ndikutumizani inu, atumiki anga Sidney ndi Parley, kuti mukalalikire uthenga wabwino kwa iwo.

4 Ndipo mtumiki wanga Leman adzadzodzedwa ku ntchito iyi, kuti akathe kutsutsana nawo, osati molingana ndi chimene adalandira kwa iwo, koma molingana ndi chimene adzaphunzitsidwa ndi inu atumiki anga; ndipo potero ndidzamudalitsa, apo ayi iye sadzachita bwino.

5 Atero Ambuye; pakuti ine ndine Mulungu, ndipo ndatumiza Mwana wanga Wobadwa Yekha mu dziko chifukwa cha chiwombolo cha dziko, ndipo ndalamulira kuti iye amene amulandira iye adzapulumutsidwa, ndipo iye amene sadzamulandira iye adzalangidwa—

6 Ndipo adachitira Mwana wa munthu monga momwe adafunira; ndipo watenga mphamvu yake pa dzanja lamanja la ulemelero wake, ndipo tsopano akulamulira kumwamba, ndipo adzalamulira kufikira atatsika pa dziko lapansi kudzaika adani onse pansi pa mapazi ake, nthawi imene ili pafupi—

7 Ine, Ambuye Mulungu, ndanena; koma ola ndi tsiku palibe munthu akudziwa, angakhale angelo kumwamba, sadzadziwa kufikira iye atabwera.

8 Kotero, ndikufuna kuti anthu onse alape, pakuti onse ali pansi pa uchimo, kupatula iwo amene ndawasungira kwa ine ndekha, anthu oyera omwe simukuwadziwa.

9 Kotero, ndikunena kwa inu kuti ndatumiza kwa inu pangano langa losatha, ngakhale lomwe lidalipo kuchokera ku chiyambi.

10 Ndipo chimene ndalonjeza ndakwaniritsa, ndipo maiko apadziko lapansi adzaligwadira; ndipo ngati si mwa iwo okha, iwo adzatsika; pakuti chimene tsopano chakwezedwa mwa icho chokha chidzatsitsidwa mu mphamvu.

11 Kotero, ndikupereka kwa inu lamulo kuti mupite pakati pa anthu awa, ndi kunena kwa iwo, monga mtumwi wanga wakale, amene dzina lake lidali Petro:

12 Khulupilirani dzina la Ambuye Yesu, amene adali padziko lapansi, amene ali nkudza, oyamba ndi otsiriza;

13 Lapani ndipo batizidwani mu dzina la Yesu Khristu, molingana ndi lamulo loyera, ku chikhululukiro cha machimo;

14 Ndipo amene amachita ichi adzalandira mphatso ya Mzimu Woyera, mwa kusanjika kwa manja a akulu a Mpingo.

15 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, kuti amene amaletsa kukwatira sadadzodzedwe ndi Mulungu, pakuti ukwati ndi wodzodzedwa ndi Mulungu kwa munthu.

16 Kotero, ndi kololedwa kuti iye akhale ndi mkazi m’modzi, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi, ndipo zonsezi kuti dziko lapansi likathe kuyankha mapeto a chilengedwe chake;

17 Ndipo kuti lidzadzidwe ndi muyeso wa munthu, molingana ndi chilengedwe chake dziko lisadapangidwe.

18 Ndipo amene amaletsa kudya nyama, kuti munthu sakuyenera kudya zomwezo, sadadzodzedwe ndi Mulungu;

19 Pakuti, taonani, nyama zakuthengo, ndi mbalame za m’mlengalenga, ndi izo zimene zimachokera ku dziko lapansi, ndi zodzodedwa kuti zigwiritsidwe ntchito ndi munthu kukhala chakudya ndi zovala, ndi kuti akathe kukhala nazo zochuluka.

20 Koma sikudapatsidwe kuti munthu m’modzi akhale ndi zomwe zili pamwamba pa mnzake, kotero dziko lapansi lagona mu uchimo.

21 Ndipo tsoka lidzakhala kwa munthu amene amakhetsa mwazi kapena amene amawononga nyama koma alibe chochita nayo.

22 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, kuti Mwana wa Munthu sadabwere mu mawonekedwe a mkazi, kapena a mwamuna woyenda pa dziko lapansi.

23 Kotero, musanyengedwe, koma pitirizani kukhala okhazikika, kuyembekezera kumwamba kudzagwedezeke, ndi dziko lapansi kuti lidzanjenjemere ndi kugwedezekera uku ndi uko monga munthu woledzera, ndi kuti zigwa zidzakwezedwe, ndi kuti mapiri adzachepetsedwe, ndi kuti malo amiyala adzakhale osalala—ndipo zonsezi pamene mngelo adzawomba lipenga lake.

24 Koma lisanadze tsiku lalikulu la Ambuye, Yakobo adzaphukira m’chipululu, ndipo Alamani adzaphuka ngati duwa.

25 Ziyoni adzaphukira pazitunda ndipo adzakondwera pamapiri, ndi kudzasonkhanitsidwa ku malo amene ndidasankha.

26 Taonani, ndinena kwa inu, pitani monga ndakulamulani inu; lapani machimo anu onse; pemphani, ndipo mudzalandira; gogodani ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.

27 Taonani, ndidzapita pamaso panu, ndi kukhala pambuyo panu; ndipo ndidzakhala pakati panu, ndipo simudzachita manyazi.

28 Taonani, ine ndine Yesu Khristu, ndipo ndidza msanga. Ngakhale zili choncho. Ameni.