Chiphunzitso ndi Mapangano
Gawo 1
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, pa 1 Novembala 1831, pa nthawi ya msonkhano waukulu wapadera wa akulu Ampingo, omwe udachitikira ku Hiram, Ohio. Mavumbulutso ambiri adalandiridwa kuchokera kwa Ambuye isadafike nthawiyi, ndipo kuphatikiza kwa zosindikizidwazi ngati buku kudali imodzi mwa mfundo zikuluzikulu zomwe zidaperekedwa pa msonkhanowo. Gawo ili limakhazikitsa mawu oyambilira a Ambuye ku ziphunzitso, mapangano ndi malamulo operekedwa mu nyengo yanthawi ino.
1–7, Mawu a chenjezezo ndi a kwa anthu onse; 8–16, Kugwa ndi kuipa kudzatsogolera Kubwera Kwachiwiri; 17–23, Joseph Smith waitanidwa kubwenzeretsanso ku dziko lapansi choonadi ndi mphamvu za Ambuye; 24–33, Buku la Mormoni libweretsedwa ndipo Mpingo oona ukhazikitsikidwa; 34–36,Mtendere udzachotsedwa padziko lapansi; 37–39, Fufuzani malamulo awa.
1 Mvetserani, O inu anthu a mpingo wanga, atero mawu a iye amene amakhala kumwamba, ndipo amene maso ake ali pa anthu onse; inde, indetu ndinena: Mvetserani inu anthu achokera kutali; ndi inu amene muli pa zilumba za nyanja, mvetserani limodzi.
2 Pakuti indetu mawu a Ambuye ali kwa anthu onse, ndipo palibe amene angathawe; ndipo palibe diso limene silidzaona, ngakhale khutu limene silidzamva, ngakhale mtima umene sadzabooleza.
3 Ndipo wopandukira adzalasidwa ndi chisoni chambiri; pakuti zoipa zawo zidzakambidwa pamadenga a nyumba, ndipo ntchito zawo zachinsinsi zidzaululika.
4 Ndipo mawu achenjezo adzakhala kwa anthu onse, ndi pakamwa pa ophunzira anga, amene ine ndawasankha m’masiku omalizawa.
5 Ndipo adzapita ndipo palibe adzawaletse iwo, pakuti ine Ambuye ndawalamula iwo.
6 Taonani, uwu ndi ulamuliro wanga ndi ulamuliro wa atumiki anga, ndi mawu oyamba anga ku buku la malamulo anga, limene ndawapatsa iwo kuti asindikize kwa inu, O inu okhala padziko lapansi.
7 Kotero, chitani mantha ndi kunjenjemera, O inu anthu, pakuti chimene ine Ambuye ndachilengeza mwa iwo chidzakwaniritsidwa.
8 Ndipo indetu, ndinena kwa inu, kuti iwo amene apita, kulalikira uthengawu kwa wokhala pa dziko lapansi, kwa iwo mphamvu yapatsidwa kutsindikiza ponse padziko lapansi ndi kumwamba, osakhulupilira ndi wopandukira;
9 Inde, indetu, kuwatsindikizira iwo mpaka tsiku limene mkwiyo wa Mulungu udzatsanuliridwa pa oipa kopanda mulingo—
10 Kufikira tsiku limene Ambuye adzabwera kudzalipira kwa munthu aliyense molingana ndi ntchito zake, ndi mlingo wa munthu aliyense molingana ndi mlingo umene iye adayesera munthu mzake.
11 Kotero mawu a Ambuye ali kwa mathero a dziko lapansi, kuti aliyense amene adzamve adzathe kumva;
12 Konzekerani inu, konzekerani pa icho chimene chili nkudza, pakuti Ambuye ayandikira.
13 Ndipo mkwiyo wa Ambuye wayaka, ndipo lupanga lake lakhuta kumwamba, ndipo lidzagwera pa wokhala pa dziko lapansi.
14 Ndipo mkono wa Ambuye udzauluridwa; ndipo tsiku likudza limene iwo amene sadzamvera mawu a Ambuye, kapena mawu a atumiki ake, ngakhale kumvera ku mawu a aneneri ndi atumwi, adzadulidwa kuchoka pakati pa anthu;
15 Pakuti iwo asochela ku miyambo yanga, ndipo aphwanya pangano langa losatha.
16 Iwo safuna Ambuye kuti akhazikitse chilungamo chake, koma munthu aliyense akuyenda mu njira ya iye yekha, ndi kutsatira chifanizo cha mulungu wake, amene chifaniziro chake chili m’chifaniziro cha dziko lapansi, ndipo thunthu lake lili la fano, limene limakalamba ndi kuwonongeka mu Babulo, ngakhale Babulo wamkulu, amene adzagwa.
17 Kotero, ine Ambuye, podziwa tsoka limene lidzabwere pa anthu okhala pa dziko lapansi, ndidaitana mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndipo ndidayankhula naye kuchokera kumwamba, ndi kumupatsa iye malamulo;
18 Ndiponso ndapereka malamulo kwa ena, kuti iwo alengeze zinthu izi ku dziko; ndipo zonsezi kuti zikathe kukwaniritsidwa, zimene zidalembedwa ndi aneneri—
19 Zinthu zofooka za dziko lapansi zidzabwera ndi kuphwanya za mphamvu ndi nyongazo, kuti munthu sayenela kulangiza munthu mzake, ngakhale kukhulupilira mkono wa thupi.
20 Koma kuti munthu aliyense akathe kuyankhula mu dzina la Mulungu Ambuye, ngakhale Mpulumutsi wa dziko lapansi;
21 Kuti chikhulupilironso chithe kukula pa dziko lapansi;
22 Kuti chipangano changa chosatha chikathe kukhazikitsidwa;
23 Kuti chidzalo cha uthenga wanga wabwino chikathe kulengezedwa ndi ofooka ndi opepuka ku malekezero a dziko, ndi pamaso pa mafumu ndi olamulira.
24 Taonani, Ine ndine Mulungu ndi ndachinena; malamulo awa ndi anga, ndipo adaperekedwa kwa atumiki anga mu kufooka kwawo, potsatila njira ya chiyankhulidwe chawo, kuti akathe kumvetsetsa.
25 Ndipo pamene iwo alakwitsa zingathe kuzindikirika.
26 Ndipo pamene iwo afunafuna nzeru angathe kuphunzitsidwa;
27 Ndipo pamene iwo achimwa angathe kudzudzulidwa, kuti iwo athe kulapa;
28 Ndipo pamene iwo adali wodzichepetsa angathe kukhala olimbitsidwa, ndi odalitsidwa kuchokera kumwamba, ndi kulandira chidziwitso ku nthawi ndi nthawi.
29 Ndipo atatha kulandira zolemba za Anefi, inde, ngakhale mtumiki wanga Joseph Smith Jun., angathe kukhala ndi mphamvu ya kumasulira kudzera mu chifundo cha Mulungu, ndi mphamvu ya Mulungu, Buku la Mormoni.
30 Ndiponso iwo amene malamulo awa adapatsidwa, angathe kukhala ndi mphamvu yoika maziko a mpingo uwu, ndi kuubweretsa kuchoka kobisika ndi kuchoka ku mdima, mpingo wokhawo oona ndi wamoyo pamaso pa dziko lonse lapansi, ndi umene ine, Ambuye, ndili okondwera nawo, kuyankhula kwa mpingo wonse osati payekhapayekha—
31 Pakuti ine, Ambuye Mulungu sindingathe kuyang’ana pa tchimo ndi kamlingo ngakhale kochepa ka chilolezo;
32 Komabe, iye amene walapa ndi kuchita malamulo a Ambuye adzakhululukidwa;
33 Ndipo iye amene salapa, kuchokera kwa iye kudzalandidwa ngakhale kuwala komwe iye adakulandira; pakuti Mzimu wanga sudzalimbana nthawi zonse ndi munthu, atero Ambuye Wamakamu.
34 Ndiponso, indetu ndinena ndi inu, O okhala pa dziko lapansi, Ine Ambuye ndili wofuna kudziwitsa zinthu izi kwa anthu onse;
35 Pakuti ine sindine wa tsankho, ndipo ndikufuna kuti anthu onse adzadziwe kuti tsiku likudza msanga; ola silidafike, koma liri pafupi, pamene mtendere udzachotsedwa kuchoka padziko lapansi, ndipo mdyelekezi adzakhala ndi mphamvu pa ulamuliro wake.
36 Ndiponso Ambuye adzakhala ndi mphamvu pa oyera mtima ake, ndipo adzalamulira pakati pawo, ndipo adzatsika pansi mu chiweruzo pa Idumeya, kapena dziko.
37 Fufuzani malamulowa, pakuti ndi oona ndi okhulupirika, ndi mauneneri ndi malonjezano amene ali m’menemo adzakwaniritsidwa onse.
38 Chimene ine Ambuye ndayankhula, ndayankhula, ndipo sindidziwiringula ndekha; ndipo ngakhale kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, mawu anga sadzatha, koma onse adzakwaniritsidwa, ngakhale ndi mawu anga omwe kapena ndi mawu a atumiki anga, ndi chimodzimodzi.
39 Pakuti taonani, ndipo onani, Ambuye ndi Mulungu, ndipo Mzimu umachitira umboni, ndipo umboniwo ndi oona, ndipo choonadi chimakhala kwamuyaya ndi muyaya. Ameni.