Gawo 72
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Disembala 4, 1831. Akulu angapo ndi mamembala adasonkhana kuti aphunzire udindo wawo ndi kulimbikitsidwa mopitilira mu ziphunzitso za Mpingo. Gawo ili ndi kuphatikiza kwa mavumbulutso atatu omwe adalandiridwa tsiku limodzi. Ndime 1 mpaka 8 zikudziwitsa maitanidwe a Newel K. Whitney ngati bishopu. Kenako adaitanidwa ndi kudzozedwa, pambuyo pake ndime 9 mpaka 23 zidalandiridwa, kupereka zowonjezera zokhudza ntchito za bishopu. Pambuyo pake, ndime 24 mpaka 26 zidaperekedwa, kupereka malangizo okhudzana ndi kusonkhanitsa ku Ziyoni.
1–8, Akulu akuyenera kupereka mbiri ya udindo wawo kwa bishopu; 9–15, Bishopu amasunga nkhokwe ndi kusamalira osauka ndi osowa; 16–26, Mabishopu akuyenera kutsimikizira kuyenera kwa akulu.
1 Mvetserani, ndipo mverani mawu a Ambuye, O inu amene mwasonkhana pamodzi, amene muli akulu ansembe a mpingo wanga, kwa amene ufumu ndi mphamvu zapatsidwa.
2 Pakuti indetu atero Ambuye, kuli koyenera mwa ine kuti bishopu aikidwe kwa inu, kapena wa inu, kwa mpingo mu gawo ili la munda wa mpesa wa Ambuye.
3 Ndipo indetu mu chinthu ichi mwachita mwanzeru, pakuti ndichofunikira kwa Ambuye, pa dzanja la mdindo aliyense, kudzapereka mbiri ya udindo wake, monse mu nthawi ndi muyaya.
4 Pakuti iye amene ali wokhulupirika ndi wanzeru mu nthawi yake amawerengedwa woyenera kulandira malo okhalamo okonzedwera iye ndi Atate anga.
5 Indetu ndinena kwa inu, akulu a mpingo mu chigawo chino cha munda wanga wampesa adzapereka mbiri ya udindo wawo kwa bishopu, amene adzasankhidwa ndi ine mu chigawo chino cha munda wanga wa mpesa.
6 Zinthu izi zidzakhala muzolembedwa, kuti zidzaperekedwe kwa bishopu mu Ziyoni.
7 Ndipo ntchito ya bishopu idzadziwika ndi malamulo omwe aperekedwa, ndi mawu a msonkhano.
8 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa iwe, mtumiki wanga Newel K. Whitney ndiye munthu amene adzasankhidwa ndikudzodzedwa ku mphamvu iyi. Ichi ndi chifuniro cha Ambuye Mulungu wanu, Muwomboli wanu. Ngakhale zili choncho. Ameni.
9 Mawu a Ambuye, mu kuwonjezera pa lamulo limene laperekedwa, kudziwitsa ntchito ya bishopu amene wadzodzedwa kwa mpingo mu chigawo chino cha munda wa mpesa, chimene indetu ndi ichi—
10 Kusunga nkhokwe ya Ambuye; kulandira ndalama za mpingo mu gawo ili la munda wampesa;
11 Kuwerengera akulu monga adalamula kale; ndi kutumikira ku zosowa zawo, amene adzalipira zomwe iwo alandira, pamene ali nazo zolipilira;
12 Kuti ichinso chikathe kukhala chopatulidwa ku ubwino wa Mpingo, kwa osauka ndi osowa.
13 Ndipo iye amene alibe nako kulipira, mbiri idzatengedwa ndi kuperekedwa kwa bishopu wa Ziyoni, amene adzalipira ngongole kuchokera mu icho chimene Ambuye adzachiyika m’manja mwake.
14 Ndipo ntchito za okhulupirika amene akugwira ntchito mu zinthu zauzimu, mu kutumikira uthenga wabwino ndi zinthu za ufumu kwa mpingo, ndi ku dziko lapansi, zidzayankha ngongole kwa bishopu mu Ziyoni;
15 Kotero chimadza kuchokera mu mpingo, pakuti molingana ndi lamulo munthu aliyense amene amabwera ku Ziyoni akuyenera kuyika zinthu zonse pamaso pa bishopu mu Ziyoni.
16 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu, kuti monga mkulu aliyense mu chigawo chino cha munda wa mpesa akuyenera kupereka mbiri ya udindo wake kwa bishopu mu chigawo chino cha munda wa mpesa—
17 Satifiketi kuchokera kwa woweruza kapena bishopu mu chigawo ichi cha munda wa mpesa, kwa bishopu mu Ziyoni, ipereka munthu aliyense kukhala wovomerezeka, ndipo ikuyankha zinthu zonse, pa cholowa, ndi kulandiridwa monga mdindo wanzeru ndi ngati wantchito wokhulupirika;
18 Apo ayi iye sadzalandiridwa ndi bishopu wa Ziyoni.
19 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu, kuti mkulu aliyense amene adzapereke mbiri kwa bishopu wa mpingo mu chigawo ichi cha munda wa mpesa avomerezedwe ndi mpingo kapena mipingo, m’mene iye amagwilira ntchito, kuti akathe kudzipereka yekha ndi mbiri zake zovomerezeka mu zinthu zonse.
20 Ndiponso, lolani atumiki anga amene asankhidwa monga adindo pa zodandaula zamalemba za mpingo wanga apeze thandizo pa bishopu kapena mabishopu mu zinthu zonse—
21 Kuti mavumbulutso akathe kusindikizidwa, ndi kupita ku malekezero a dziko lapansi; kuti iwonso akathe kupeza ndalama zimene zidzapindulira mpingo mu zinthu zonse;
22 kuti iwonso akathe kuyesedwa ovomerezeka mu zinthu zonse, ndi kuwerengedwa ngati adindo anzeru.
23 Ndipo tsopano, taonani, ichi chidzakhala chitsanzo kwa nthambi zambiri za mpingo wanga, mu dziko lililonse lomwe zidzakhazikitsidwe. Ndipo tsopano ndikumaliza zoyankhula zanga. Ameni.
24 Mawu ochepa mu kuwonjezera ku malamulo a ufumu, ponena za mamembala a mpingo—iwo amene asankhidwa ndi Mzimu Woyera kuti apite ku Ziyoni, ndi iwo amene ali ndi mwayi wopita ku Ziyoni—
25 Alekeni iwo anyamule kwa bishopu satifiketi yochokera kwa akulu atatu a mpingo, kapena satifiketi yochokera kwa bishopu;
26 Apo ayi iye amene adzapita ku dziko la Ziyoni sadzawerengedwa ngati mdindo wanzeru. Ichinso ndi chitsanzo. Ameni.