Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 119


Gawo 119

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Mneneri, ku Far West, Missouri, Julayi 8, 1838, poyankha ku pembedzero lake: “O Ambuye! Onetserani kwa atumiki anu kuchuluka kotani kumene mukufuna pa katundu wa anthu anu pa chakhumi.” Lamulo la Chakhumi, monga limadziwika lero, lidali lisadaperekedwe ku Mpingo pambuyo pa vumbulutso ili. Mawuwa chakhumi mu pemphero lomwe langonenedwanso ndi mu mavumbulutso a m’mbuyo (64:23; 85:3; 97:11) sankatanthauza chimodzi mwa khumi chokha, koma zonse zopereka mwakufuna, kapena zosonkha, ku ndalama za Mpingo. Vumbulutso ili lidabwera potsatira Oyera mtima atavutika ndi zovuta zachuma ku Missouri ndi Ohio chifukwa cha kumangidwa kwa Kachisi wa Kirtland; mazunzo ku Jackson County, Missouri; ndi mavuto azachuma adziko lonse. Oyera mtima adalinso akupitilizabe kumanga midzi ku Missouri.

1–5, Oyera mtima akuyenera kupereka katundu wawo wotsala ndipo kenako kupereka, ngati chakhumi, limodzi mwa magawo khumi a chiwongola dzanja pa chaka; 6–7, Njira yotero idzayeretsa dziko la Ziyoni.

Indetu, akutero Ambuye, ndikufuna katundu wawo yense wotsala kuti aikidwe m’manja mwa bishopu wa mpingo wanga mu Ziyoni.

Pa kumanga kwa nyumba yanga, ndi kuyala maziko a Ziyoni ndi ku unsembe, ndi ku ngongole za Atsogoleri a Mpingo wanga.

Ndipo ichi chidzakhala chiyambi cha chakhumi cha anthu anga.

Ndipo pambuyo pake, iwo amene apereka chachikhumi adzapereka gawo limodzi mwa magawo khumi a chiwongola dzanja chawo pachaka; ndipo ili lidzakhala lamulo lokhazikika kwa iwo kwamuyaya, kwa unsembe wanga woyera, atero Ambuye.

Indetu ndikunena kwa inu, zidzachitika kuti iwo onse amene asonkhana ku dziko la Ziyoni adzapereka chachikhumi cha katundu wawo wotsala, ndipo adzatsatira lamulo limeneli, kapena iwo sadzapezeka oyenera kukhala pakati panu.

Ndipo ndinena kwa inu, ngati anthu anga satsatira lamulo ili, kulisunga loyera, ndipo mwa lamuloli kuyeretsa dziko la Ziyoni kwa ine, kuti malamulo anga olembedwa ndi ziweruzo zanga zikathe kusungidwa kumeneko, kuti likathe kukhala loyera kwambiri, taonani, indetu ndikunena kwa inu, silidzakhala dziko la Ziyoni kwa inu.

Ndipo ichi chidzakhala chitsanzo kwa masiteki onse a Ziyoni. Ngakhale choncho. Ameni.