Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 123


Mutu 123

Udindo wa Oyera mtima mogwirizana ndi owasautsa awo, monga zidalembedwa ndi Joseph Smith Mneneri pamene adali mkaidi mu ndende ya Liberty, Missouri. Gawo ili ndi lochokera ku kalata ya kumpingo yolembedwa cha m’Malitchi 22, 1839, (onani mutu wa gawo 122).

1–6, Oyera mtima akuyenera kusonkhanitsa ndi kusindikiza nkhani yokhudza mavuto ndi masautso awo; 7–10, Mzimu womwewo umene udakhazikitsa zipembedzo zabodza umatsogoleranso masautso kwa Oyera mtima; 11–17, Ambiri mwa zipembedzo zonse adzalandirabe choonadi.

1 Ndiponso, tidzapereka malingaliro kuti muganizirepo zakuyenera kwa oyera mtima onse kusonkhanitsa kwa chidziwitso cha zoona zake zonse, ndi mavuto ndi nkhanza zomwe zimaikidwa pa iwo ndi anthu a mu Dziko lino;

2 Ndiponso za katundu yense ndi mtengo wa zowonongeka zimene iwo zawachitikira, zonse za zinthu kapena kupwetekedwa kwamwini, chimodzimodzinso chuma chenicheni;

3 Ndiponso maina a anthu onse amene aikirapo dzanja pa kuponderezedwa kwawo, m’mene iwo angathere kuwadziwa ndi kuwapeza iwo.

4 Ndipo mwina bungwe litha kusankhidwa kuti lifufuze zinthu izi, ndi kutenga madandaulo ndi zilumbiro; ndiponso kusonkhanitsa nkhani zabodza zimene zikufalitsidwa;

5 Ndipo zonse zimene zili m’magazini, ndi mabuku ophunzitsa, ndi zonse za mbiri yabodza zimene zalembedwa, ndi zomwe zikulembedwa, ndi amenewo, ndi kupereka zonse zogwirizana ndi zankhanza zaudyerekezi ndi zonyansa, ndi zakupha zimene zakhala zikuchitika pa anthu awa—

6 Kuti tisangozifalitsa kokha ku dziko lonse lapansi, koma kuzipereka kwa atsogololeri adziko mu zawo zonse zamdima ndi ntchito zochokera ku gahena, ngati kuyesetsa komaliza kumene kwalamulidwa pa ife ndi Atate athu Akumwamba, tisadafike ndi kudzinenera kwathunthu lonjezo lija limene tidzamuitana iye kuchokera ku malo ake obisika; ndiponso kuti dziko lonse likathe kusiidwa opanda choletsa iye asadatumize mphamvu ya mkono wake wamphamvu.

7 Ndi ntchito yofunikira imene ife tilinayo kwa Mulungu, kwa angelo, amene ife tidzaimitsidwa nawo, ndiponso kwa ife eni, kwa akazi athu ndi ana, amene apangitsidwa kuzyolika kamba ka chisoni, maliro ndi madandaulo, pansi pa dzanja loopsya kwambiri la kupha, nkhanza, ndi kupondelezana, kothandizidwa ndi kupsepserezedwa ndi kulimbikitsidwa ndi chikoka cha mzimu umene wasintha mwamphamvu zikhulupiliro za makolo, amene aphunzira mabodza, pa mitima ya ana a anthu, ndi kudzadzitsa dziko ndi chisokonezo, ndipo wakhala akukula mphamvu ku mphamvu, ndipo tsopano ndi gwero lenileni la chinyengo chonse, ndipo dziko lapansi lonse likubuula pansi pa kulemera kwa kusaweruzika kwake.

8 Ndi goli lachitsulo, ndi chingwe champhamvu; iwo ndiwo maunyolo omwe, ndi nsinga, ndi matangadza a gahena.

9 Kotero ndi udindo ofunikira umene ife tilinawo, osati kwa akazi athu okha ndi ana, koma kwa akazi amasiye ndi opanda tate, amene amuna awo ndi atate awo aphedwa pansi pa dzanja lachitsulo chake;

10 Chimene mdima wake ndi ntchito zake zodetsa ndi zokwanira pakupangitsa gahena yemwe kunjenjemera, ndi kuima modabwitsika ndi kutumbululuka, ndipo manja a mdyerekezi yemweyo kunjenjemera ndi manjenje,

11 Ndiponso ndi udindo ofunikira umene ife tilinawo kwa m’badwo wonse watsopano, ndi kwa onse oyera mu mtima—

12 Pakuti adakalipo ambiri pa dziko lapansi pakati pa zipembedzo zonse, zipani, ndi mipingo, amene achititsidwa khungu ndi kuchenjera kwa anthu, kotero iwo amakhala nkuyembekezera kuti anamize, ndi amene akungokanizidwa kudziwa choonadi chifukwa iwo sakudziwa kumene angachipeze—

13 Kotero, kuti titaye ndi kutopetsa miyoyo yathu pakubweretsa m’kuwala zinthu zonse zobisika za mdima, zimene ife tikuzidziwa; ndipo ndi zoonetseredwadi kuchokera kumwamba—

14 Zimenezi zikuyenera kusamalidwa mwa khama lalikulu.

15 Pasapezeke munthu ozitenga ngati zinthu zazing’ono; pakuti pali zambiri zimene zili mtsogolo, zokhudzana ndi oyera mtima, zimene zikudalira pa zinthu izi.

16 Inu mukudziwa, abale, kuti bwato lalikulu limapindula kwambiri ndi kachiwongolero kakang’ono mu nthawi ya namondwe, pakuzembazemba mphepo ndi mafunde.

17 Kotero, abale anga okondwedwa, tiyeni mwamsangala tichite zinthu zonse zimene zili mu mphamvu yathu; ndipo kenako tiime nji, ndi chitsimikizo chenicheni, kuona chipulumutso cha Mulungu, ndipo kuti mkono wake ukavumbulutsidwe.