Gawo 92
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Malitchi 15, 1833 Vumbulutsoli liphunzitsa Frederick G. Williams, amene adali atangosankhidwa kukhala mlangizi wa Joseph Smith, pa ntchito zake mu United Firm (onani mitu ya magawo 78 ndi82).
1–2, Ambuye apereka lamulo lokhudzana ndi kuvomerezedwa mu bungwe logwirizana.
1 Indetu, atero Ambuye, ndikupereka kwa bungwe logwirizana, lokhazikitsidwa mogwirizana ndi lamulo loperekedwa kale, vumbulutso ndi lamulo lokhudza mtumiki wanga Frederick G. Williams, kuti mudzamulandire iye mu bungweli. Zomwe ndanena kwa m’modzi ndinena kwa onse.
2 Ndiponso, ndikunena kwa iwe mtumiki wanga Frederick G. Williams, udzakhala membala ofunika mu bungweli; ndipo pamene iwe uli wokhulupirika pakusunga malamulo anga onse akale udzadalitsidwa kwamuyaya. Ameni.