Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 45


Gawo 45

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Mpingo, ku Kirtland, Ohio, Malichi 7, 1831. Potsogolera mbiri ya vumbulutso ili, mbiri ya Joseph Smith ikunena kuti “pamsinkhu uwu wa Mpingo … malipoti abodza ochuluka … ndi nkhani zopusa, zidasindikizidwa …ndi kufalitsidwa, … kuletsa anthu kufufuza ntchitoyi, kapena kulandira chikhulupiliro. … Koma ku chisangalalo cha Oyera Mtima, … ndidalandira zotsatirazi.”

1–5, Khristu ndiye nkhoswe wathu ndi Atate; 6–10, Uthenga wabwino ndi mthenga wokonza njira pamaso pa Ambuye; 11–15, Enoki ndi abale ake adalandilidwa ndi Ambuye kwa Iyemwini; 16–23, Khristu adaulula zizindikiro za kudza Kwake monga kudaperekedwa pa Phiri la Azitona; 24–38, Uthenga wabwino udzabwenzeretsedwa, nthawi za Amitundu zidzakwaniritsidwa, ndipo matenda owononga adzakuta dziko; 39–47, Zizindikiro, zodabwitsa, ndi Chiukitso zikuyenera kupezeka pa Kudza Kwachiwiri; 48–53, Khristu adzaima pa Phiri la Azitona, ndipo Ayuda adzaona mabala m’manja ndi m’mapazi Ake; 54–59, Ambuye adzalamulira nthawi ya Zakachikwi; 60–62, Mneneri akulangizidwa kuti ayambe kumasulira kwa Chipangano Chatsopano, m’mene uthenga ofunikira udzadziwika; 63–75, Oyera mtima akulamulidwa kusonkhanitsa ndi kumanga Yerusalemu Watsopano, kumene anthu ochokera m’maiko onse adzabwera.

1 Mvetserani, inu anthu a mpingo wanga, kwa amene ufumu wapatsidwa; mvetserani ndipo tcherani khutu kwa iye amene adayala maziko a dziko lapansi, amene adalenga kumwamba ndi makamu ake onse, ndi amene zinthu zonse zidalengedwa zimene zili moyo, ndi zoyenda, ndipo zili ndi umoyo.

2 Ndiponso ndikunena, mvetserani ku mawu anga, kuopa imfa ingakupezeni inu; mu ola limene simuliganizira kuti chilimwe chidzapita, ndipo kukolora kudatha, ndipo miyoyo yanu sidapulumutsidwe.

3 Mverani iye amene ali nkhoswe ndi Atate, amene akukuchondelerani mlandu wanu pamaso pawo—

4 Atero: Atate, taonani mazunzo ndi imfa ya iye amene sadachite tchimo, mwa amene mudakondwera naye; taonani mwazi wa Mwana wanu wokhetsedwa, mwazi wa iye amene mudampereka, kuti inu nokha mukathe kulemekezedwa;

5 Kotero, Atate, pulumutsani abale anga awa amene amakhulupilira dzina langa, kuti abwere kwa ine ndi kukhala nawo moyo wosatha.

6 Mvetserani, O inu anthu a mpingo wanga, ndipo inu akulu mvetserani pamodzi, ndi kumva mawu anga pamene likutchedwa lero, ndipo musaumitse mitima yanu;

7 Pakuti indetu ndinena kwa inu kuti ndine Alefa ndi Omega, oyamba ndi otsiriza, kuunika ndi moyo wa dziko lapansi—kuunika kumene kumawala mu mdima ndipo mdimawo sumakuzindikira.

8 Ndidadza kwa anga, ndipo anga sadandilandire ine; koma kwa onse amene adandilandira ine ndidapereka mphamvu yakuchita zozizwitsa zambiri, ndikukhala ana a Mulungu; ndipo ngakhale kwa iwo akukhulupilira dzina langa ndidapereka mphamvu yakulandira moyo wosatha.

9 Ndipo ngakhale choncho ine ndatumiza pangano langa losatha ku dziko lapansi, kuti likhale kuunika kwa dziko lapansi, ndi kukhala mbendera kwa anthu anga, ndi kwa Amitundu kulifunafuna, ndi kukhala mthenga pamaso panga wokakonza njira pamaso panga.

10 Kotero bwerani inu kwa ilo, ndipo ndi iye amene akudza ine ndidzaweruza monga ndi anthu mu masiku akale, ndipo ine ndidzakuonetsani inu kuweruzidwe kanga kolimba.

11 Kotero, mvetserani inu limodzi ndipo ndiloleni ine ndikuonetseni kwa inu ngakhale nzeru zanga—nzeru za iye amene inu mumati ndi Mulungu wa Enoki, ndi abale ake,

12 Omwe adalekanitsidwa ndi dziko lapansi, ndipo adalandiridwa kwa ine—mzinda wosungidwa kufikira tsiku la chilungamo lidzafika—tsiku limene lidafunidwa ndi anthu onse oyera, ndipo sadalipeze chifukwa cha zoipa ndi zonyansa;

13 Ndipo adavomereza kuti iwo ndi alendo ndi oyendayenda pa dziko lapansi;

14 Koma adalandira lonjezano kuti akuyenera kudzalipeza, ndikuliona muthupi mwawo.

15 Kotero, mvetserani ndipo ndidzaweruzana nanu, ndipo ndidzayankhula kwa inu ndi kunenera, monga kwa anthu mu masiku akale.

16 Ndipo ndidzalionetsa momveka bwino monga ndidalionetsera kwa ophunzira anga pamene ndidaima pamaso pawo mu thupi, ndi kunena kwa iwo, nati: Monga mudandifunsa zokhudza zizindikiro za kudza kwanga, tsiku limene ndidzabwera mu ulemelero wanga m’mitambo ya kumwamba, kudzakwaniritsa malonjezo amene ndidawalonjeza kwa makolo anu,

17 Pakuti monga mudayang’ana pa kusapezeka kwa nthawi yaitali kwa mizimu yanu m’matupi anu kukhala ukapolo, ndidzakuonetsani inu m’mene tsiku la chiwombolo lidzafikile, ndiponso kubwenzeretsedwa kwa Israeli wobalalitsidwa.

18 Ndipo tsopano mukuona kachisi uyu amene ali mu Yerusalemu, amene inu mumamutcha Nyumba ya Mulungu, ndipo adani anu akunena kuti nyumba iyi sidzagwa konse.

19 Koma, indetu, ndinena kwa inu, kuti chipululuko chidzafika pa m’badwo uno monga mbala usiku, ndipo anthu awa adzawonongedwa ndi kubalalitsidwa mwa mitundu yonse.

20 Ndipo kachisi uyu amene mukumuona tsopano adzagwetsedwa pansi kuti sipadzasiidwa mwala umodzi pamwamba pa umzake.

21 Ndipo zidzachitika kuti m’badwo uwu wa Ayuda sudzatha mpaka chipululuko chilichonse chimene ine ndakuuzani inu chokhudza iwo chidzachitike.

22 Inu mumanena kuti mumadziwa kuti chimaliziro cha dziko lapansi chikudza; mukunenanso kuti mukudziwa kuti kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha;

23 Ndipo mu ichi mukunena zoona, pakuti zili choncho; koma zinthu izi zimene ine ndakuuzani inu sizidzatha kufikira zonse zidzakwaniritsidwa.

24 Ndipo izi ndakuuzani inu zokhudza Yerusalemu; ndipo pamene tsikulo lidzafika, otsala adzabalalitsidwa mwa maiko onse;

25 Koma iwo adzasonkhanitsidwanso; koma adzakhala kufikira nthawi za anthu Amitundu zikwaniritsidwe.

26 Ndipo mu tsiku limenelo zidzamveka za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala mu chipwirikiti, ndipo mitima ya anthu idzawalephera, ndipo iwo adzanena kuti Khristu akuchedwetsa kubwera kwake kufikira mapeto a dziko lapansi.

27 Ndipo chikondi cha anthu chidzazilala, ndipo kusaweruzika kudzachuluka.

28 Ndipo pamene nthawi za Amitundu zidzalowa, kuunika kudzatulukila pakati pa iwo amene amakhala mumdima, ndipo kudzakhala chidzalo cha Uthenga wabwino wanga;

29 Koma iwo sakuulandira; pakuti iwo sazindikira kuunikako, ndipo atembenuzira mitima yawo kwa ine chifukwa cha malangizo a anthu.

30 Ndipo mu m’badwo umenewo nthawi za Amitundu zidzakwaniritsidwa.

31 Ndipo padzakhala anthu amene adzaimilira mu m’badwo umenewo, amene sadzapita kufikira pamene adzaona mliri wosefukira; pakuti nthenda yachipululuko idzakuta dziko.

32 Koma ophunzira anga adzaimilira m’malo opatulika, ndipo sadzagwedezeka; koma pakati pa oipa, anthu adzakweza mawu awo ndi kutembelera Mulungu ndi kufa.

33 Ndipo padzakhala zivomerezi m’malo osiyanasiyana, ndi mabwinja ambiri; koma anthu adzalimbitsa mitima yawo motsutsa ine, ndipo adzanyamula lupanga, wina ndi mnzake, ndipo adzaphana.

34 Ndipo tsopano, pamene ine Ambuye ndidanena mawu awa kwa ophunzira anga, iwo adavutitsika.

35 Ndipo ine ndidati kwa iwo: Musadere nkhawa, pakuti, pamene zinthu zonsezi zidzachitika, mudzatha kudziwa kuti malonjezo amene adapangidwa kwa inu adzakwaniritsidwa.

36 Ndipo pamene kuwala kudzayamba kutulukira, kudzakhala ndi iwo monga fanizo limene ndidzakuonetsani inu—

37 Inu mumapenya ndipo mumaona mitengo ya mkuyu, ndipo mumaiona ndi maso anu; ndipo mumanena, pamene imayamba kuphuka, ndipo masamba ake akali anthete, kuti chilimwe chayandikira tsopano;

38 Momwemonso kudzakhala tsiku limenelo pamene iwo adzaona zinthu zonsezi, pamenepo adzadziwa kuti nthawi yayandikira.

39 Ndipo zidzachitika kuti iye amene amandiopa ine adzayembekezera tsiku lalikulu la Ambuye likudza, ngakhale zizindikiro za kudza kwa Mwana wa Munthu.

40 Ndipo adzaona zizindikiro ndi zozizwa, pakuti zidzaonetsedwa kumwamba, ndi pansi pa dziko lapansi.

41 Ndipo adzaona mwazi, ndi moto, ndi nthunzi ya utsi.

42 Ndipo lisadadze tsiku la Ambuye, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi udzasanduka mwazi, ndipo nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba.

43 Ndipo otsalawo adzasonkhanitsidwa kumalo ano;

44 Ndipo pamenepo adzandifunafuna ine, ndipo, taonani, ndidzabwera; ndipo adzandiona ine m’mitambo ya kumwamba, wovala mphamvu ndi ulemelero waukulu; ndi angelo onse oyera; ndipo iye wosandidikira adzadulidwa.

45 Koma dzanja la Ambuye lisadagwe, mngelo adzaomba lipenga lake, ndipo oyera mtima amene adagona adzatuluka kudzakumana nane mu mitambo.

46 Kotero, ngati mwagona mumtendere odala ndinu; pakuti monga mundionera tsopano ndi kudziwa kuti ine ndine, ngakhale motero inu mudzabwera kwa ine ndipo miyoyo yanu idzakhala ndi moyo, ndipo chiwombolo chanu chidzakhala changwiro; ndipo oyera mtima adzatuluka kuchokera ku ngodya zinayi za dziko lapansi.

47 Pamenepo mkono wa Ambuye udzagwera pa maiko.

48 Ndipo pamenepo Ambuye adzaponda phazi lake pa phiri ili, ndipo lidzang’ambika pakati; ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka; ndi kugwedezeka uku ndi uko, ndipo kumwambanso kudzagwedezeka.

49 Ndipo Ambuye adzayankhula mawu ake, ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamva; ndipo maiko a dziko lapansi idzalira, ndipo iwo akuseka adzaona kupusa kwawo.

50 Ndipo tsoka lidzaphimba wonyoza, ndi wonyoza adzatenthedwa; ndipo iwo amene amadikira mphulupulu adzadulidwa, ndi kuponyedwa kumoto.

51 Pamenepo Ayuda adzandiyang’ana, nati: Mabala awa ali m’manja mwanu ndi m’mapazi anu n’chiyani?

52 Pamenepo adzadziwa kuti ine ndine Ambuye; pakuti ndidzati kwa iwo: Mabala awa ndiwo mabala amene ndidavulazidwa nawo m’nyumba ya anzanga. Ine ndine amene ndidakwezedwa. Ine ndine Yesu amene adapachikidwa. Ine ndine Mwana wa Mulungu.

53 Ndipo pamenepo adzalira chifukwa cha mphulupulu zawo; pamenepo adzalira chifukwa adazunza mfumu yawo.

54 Ndipo pamenepo maiko achikunja adzawomboledwa, ndipo iwo amene sadadziwe lamulo adzakhala nawo gawo mu chiwukitso choyamba; ndipo kudzaloredwa kwa iwo.

55 Ndipo Satana adzamangidwa, kuti sadzakhala ndi malo m’mitima ya ana a anthu.

56 Ndipo pa tsiku limenelo, pamene ine ndidzafika mu ulemelero wanga, fanizo limene ine ndidayankhula zokhudza anamwali khumi lidzakwaniritsidwa.

57 Pakuti iwo amene ali anzeru ndipo alandira choonadi, ndipo atenga Mzimu Woyera kukhala mtsogoleri wawo, ndipo sadanyengedwe—indetu ndinena kwa inu, iwo sadzadulidwa ndi kuponyedwa m’moto, koma adzakhalabe m’tsikulo.

58 Ndipo dziko lapansi lidzapatsidwa kwa iwo ngati cholowa; ndipo iwo adzachulukana, ndikudzakhala amphamvu, ndipo ana awo adzakula opanda uchimo kufikira chipulumutso.

59 Pakuti Ambuye adzakhala pakati pawo, ndipo ulemelero wake udzakhala pa iwo, ndipo iye adzakhala mfumu yawo ndi wopereka malamulo wawo.

60 Ndipo tsopano, taonani, ndinena kwa inu, sikudzapatsidwa kwa inu kudziwa kopitilira zokhudza mutu uwu, kufikira kuti Chipangano Chatsopano chimasuliridwe, ndipo m’menemo zinthu zonsezi zidzadziwika;

61 Kotero ndipereka kwa inu kuti tsopano mukathe kumasulira izo, kuti inu mukathe kukhala okonzekera zinthu zimene zili nkudza.

62 Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti zinthu zazikulu zikukuyembekezerani inu;

63 Mukumva za nkhondo m’maiko akunja; koma, taonani, ndinena kwa inu, zili pafupi, inde pa makomo anu, ndipo si zaka zambiri kuchokera pano mudzamva za nkhondo m’maiko anu omwe.

64 Kotero ine, Ambuye, ndati, sonkhanitsani inu kuchokera m’maiko akum’mawa, sonkhanitsani inu eni pamodzi akulu a mpingo wanga; tulukani kumaiko akumadzulo;itanani pa okhalamo kuti alape, ndipo pamene iwo akulapa, mangani mipingo kwa ine.

65 Ndipo ndi mtima umodzi ndi malingaliro amodzi, sonkhanitsani chuma chanu kuti mugule cholowa chimene chidzaikidwa kwa inu pambuyo pake.

66 Ndipo lidzatchedwa Yerusalemu Watsopano, dziko la mtendere, mzinda othawirako, malo achitetezo a oyera mtima a Mulungu Wam’mwambamwamba;

67 Ndipo ulemelero wa Ambuye udzakhala komweko, ndi kuopsa kwa Ambuye kudzakhala komweko, kotero kuti oipa sadzabwerako, ndipo lidzatchedwa Ziyoni.

68 Ndipo zidzachitika pakati pa oipa, kuti munthu aliyense amene sadzatenga lupanga lake motsutsana ndi mnansi wake akuyenera kuthawira ku Ziyoni chifukwa cha chitetezero.

69 Ndipo adzasonkhanitsidwa kwa ilo ochokera ku dziko lililonse pansi pa thambo; ndipo adzakhala anthu okhawo amene sadzamenyana wina ndi mnzake.

70 Ndipo kudzanenedwa pakati pa oipa: Tisapite kukamenyana ndi Ziyoni, pakuti okhala mu Ziyoni ndi oopsa; kotero sitingathe kuyima.

71 Ndipo zidzachitika kuti olungama adzasonkhanitsidwa kuchokera pakati pa maiko onse, ndipo adzabwera ku Ziyoni, akuyimba ndi nyimbo za chisangalalo chosatha.

72 Ndipo tsopano ndinena kwa inu, sungani zinthu izi kuti zisapitilire kudziko kufikira pamene kuli koyenera mwa ine, kuti mukathe kukwaniritsa ntchito iyi pamaso pa anthu, ndi pamaso pa adani anu, kuti asathe kudziwa ntchito zanu kufikira mutakwaniritsa chinthu chimene ndidakulamulani;

73 Kuti pamene iwo adzachidziwa, kuti akathe kuganizira zinthu izi.

74 Pakuti pamene Ambuye adzaonekera adzakhala oopsa kwa iwo, kuti mantha adzawagwira, ndipo adzaima patali ndi kunjenjemera.

75 Ndipo maiko onse adzaopa chifukwa cha kuopsa kwa Ambuye, ndi mphamvu ya mphamvu yake. Ngakhale choncho. Ameni.