Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 82


Gawo 82

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Independence, Dera la Jackson, Missouri, Epulo 26, 1832. Chochitikacho chidali msonkhano wa ansembe aakulu ndi akulu a Mpingo. Pa msonkhanowo, Joseph Smith adachirikizidwa ngati Mtsogoleri wa Unsembe Waukulu, umene udindo wake m’mbuyomo iye adadzodzedwa pa msonkhano wa akulu ansembe, akulu ndi mamembala, ku Amherst, Ohio, Januwale 25, 1982 (onani mutu wa gawo 75). Vumbulutso ili likubwereza malangizo a mu vumbulutso lakale (gawo 78) kuti akhazikitse kampani—yodziwika kuti United Firm (pansi pa utsogoleri wa Joseph Smith, mawu oti “dongosolo” pambuyo pake adasinthidwa ku “kampani”)—kutsogolera zichitochito za malonda ndi kusindikiza za Mpingo.

1–4, Pamene zambiri zaperekedwa, zambiri zimafunikira; 5–7, Mdima ulamulira mu dziko; 8–13, Ambuye ndi womangidwa pamene tichita zomwe iye wanena; 14–18, Ziyoni akuyenera kukula m’makongoledwe ndi mchiyero; 19–24, Munthu aliyense akuyenera kufunafuna zosangalatsa mnasi wake.

Indetu, indetu, ndinena kwa inu, atumiki anga, kuti pamene inu mukhululukirana wina ndi mzake zolakwa zanu, ngakhale chomwecho ine, Ambuye wanu, ndikukhululukirani.

Komabe, alipo ena pakati panu amene achimwa kopambana; inde, ngakhale nonsenu mwachimwa; koma indetu ndikunena kwa inu, chenjerani tsopano, ndi kupewa tchimo, kuopa chiweruzo choopsya chingakugwereni pa mutu panu.

Pakuti kwa iye amene wapatsidwa zambiri zambiri zimafunikira; ndipo iye amene achimwa motsutsana ndi kuwala kwakukulu adzalandira chiweruzo chachikulu.

Inu mumaitanira pa dzina langa pa mavumbulutso, ndipo ine ndimapereka kwa inu; ndipo pamene inu simusunga zonena zanga, zimene ndikupatsani, mumakhala olakwa; ndipo chilungamo ndi chiweruzo ndi chilango chimene chaikidwa ku lamulo langa.

Kotero, zimene ndikunena kwa m’modzi ndimanena kwa onse: Chenjerani, pakuti mdaniyo akufalitsa ulamuliro wake, ndipo mdima ukulamulira;

Ndipo mkwiyo wa Mulungu wayaka motsutsana ndi okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe akuchita zabwino, pakuti onse achoka mu njirayo.

Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa inu, ine, Ambuye, sindidzayala tchimo lililonse pa mlandu wanu; pitani m’njira zanu ndipo musachimwenso; koma kwa moyo wa iye amene achimwa, machimo akale adzabwelera, atero Ambuye Mulungu wanu.

Ndiponso, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu lamulo latsopano, kuti mukathe kumvetsa chifuniro changa chokhudza inu;

Kapena, mu mawu ena, ndikukupatsani inu chitsogozo m’mene mungachitire pamaso panga, kuti zikatembenukire kwa inu kukhala chipulumutso chanu.

10 Ine, Ambuye, ndimamangika pamene inu muchita zimene ine ndanena; koma pamene simuchita zimene ine ndanena, mulibe lonjezo.

11 Kotero, indetu ndinena kwa inu, kuti ndikofunikira kwa mtumiki wanga Edward Partridge ndi Newel K. Whitney, A. Sidney Gilbert ndi Sidney Rigdon, ndi mtumiki wanga Joseph Smith, ndi John Whitmer ndi Oliver Cowdery, ndi W. W. Phelps ndi Martin Harris kumangidwa pamodzi ndi chikole ndi pangano limene silingaphwanyidwe ndi zolakwa, kupatula chiweruzo chidzatsatira mwachangu, mu maudindo anu ochuluka—

12 Kutsogolera zochitika za osauka, ndi zinthu zonse zokhudzana ndi ubishopu monse mu dziko ndi mu Ziyoni ndi mu dziko la Kirtland;

13 Pakuti ine ndapatula dziko la Kirtland mu nthawi yanga yoikika pa kupindula kwa oyera mtima a Wam’mwambamwamba, ndi pa siteki ku Ziyoni.

14 Pakuti Ziyoni akuyenera kukula m’makongoledwe ndi mu chiyero; malire ake akuyenera kukulitsidwa; masiteki ake akuyenera kulimbikitsidwa; inde, indetu ndikunena kwa inu, Ziyoni akuyenera kudzuka ndi kuvala zovala zake zokongola.

15 Kotero, ndikupereka kwa inu lamulo ili, kuti mudzimangilire nokha ndi panganoli, ndipo zidzachitika molingana ndi malamulo a Ambuye.

16 Taonani, iyi ndi nzerunso mwa ine pa ubwino wanu.

17 Ndipo mukuyenera kukhala ofanana, kapena mu mawu ena, mukuyenera kukhala ndi zonena zofanana pa katunduyo, kuti zipindule posamalira nkhawa za undindo wanu, munthu aliyense molingana ndi zofuna zake ndi zosowa zake, ngati zofunazo zili zolungama—

18 Ndipo zonsezi kuti zipindulire mpingo wa Mulungu wamoyo, kuti munthu aliyense akathe kuwonjezera pa luso lake, kuti munthu aliyense akathe kupeza maluso ena, inde, ngakhale mazanamazana, kuti ziponyedwe mu nkhokwe ya Ambuye, kuti zikhale katundu wosonkhanitsidwa wa mpingo wonse—

19 Munthu aliyense kufunafuna zomusangalatsa mnasi wake, ndi kuchita zinthu zonse ndi diso lolunjika ku ulemelero wa Mulungu.

20 Dongosolo ili ndasankhira kuti likhale dongosolo la muyaya kwa inu, ndi kwa olowa m’malo mwanu, ngati inu simuchimwa.

21 Ndipo moyo umene uchimwira pangano limeneli, ndi kulimbitsa mtima wake motsutsana nalo, udzachitiridwa molingana ndi malamulo a mpingo wanga, ndipo udzaperekedwa ku madyelero a Satana kufikira tsiku la chiwombolo.

22 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa inu, ndipo iyi ndi nzeru, dzipangireni nokha anzanu ndi mamoni wa kusalungama, ndipo iwo sadzakuwonongani inu.

23 Lekani chiweruzo kwa ine ndekha, pakuti ndi changa ndipo ndidzabwenzera. Mtendere ukhale nanu; madalitso anga apitilire nanu.

24 Pakuti ngakhale tsopano ufumu ndi wanu, ndipo udzakhala kwa muyaya, ngati simugwa mu kukhazikika kwanu. Ngakhale choncho. Ameni.