Gawo 86
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Disembala 6, 1832. Vumbulutso ili lidalandiridwa pamene Mneneri adali kuunikanso ndi kukonza malembo apamanja a kumasulira kwa Baibulo.
1–7, Ambuye akupereka tanthauzo la fanizo la tirigu ndi nansongole; 8–11, Iye akufotokoza madalitso a unsembe kwa iwo amene ali acholowa mwalamulo monga mwa thupi.
1Â Indetu, akutero Ambuye kwa inu atumiki anga, zokhudzana ndi fanizo la tirigu ndi nansongole:
2Â Taonani, indetu ndinena, Mundawo udali dziko lapansi, ndipo atumwiwo ndiwo akufesa mbewu;
3 Ndipo atagona tulo wozunza wamkulu wa mpingo, wampatuko, wadama, ngakhale Babulo, amene amapangitsa mafuko onse kumwera chikho chake, amene m’mitima mwawo mdani, inde Satana, amakhala kuti alamulire—taonani afesa nansongole; kotero, nansongole atsamwitsa tirigu ndi kukankhira mpingo ku chipululu.
4 Koma taonani, m’masiku omaliza, ngakhale tsopano pamene Ambuye akuyamba kutulutsa mawu, ndipo tsamba likuphuka ndipo likadali lanthete—
5Â Taonani, indetu ndinena kwa inu, angelo akufuulira kwa Ambuye usana ndi usiku, amene ali okonzeka ndi kuyembekezera kutumizidwa kukakolora minda;
6Â Koma Ambuye akunena kwa iwo, musazule nansongole pamene tsamba likadali lanthete (pakuti ndithudi chikhulupiliro chanu chili chofooka), kuti mungawonongenso tirigu.
7Â Kotero lolani tirigu ndi nansongole zikulire limodzi mpaka nthawi yokolola yakwana ndithu; pamenepo mudzayamba kusonkhanitsa tirigu mwa nansongole, ndipo pambuyo pa kusonkhanitsa kwa tirigu, taonani ndipo onani, nansongole wamangidwa mitolo, ndipo munda watsala kuti utenthedwe.
8 Kotero, akutero Ambuye kwa inu, amene unsembe udapitilira kudzera mu m’badwo wa makolo anu—
9 Pakuti muli olandira cholowa mwalamulo, monga mwa thupi, ndipo mudabisidwa ku dziko pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu—
10 Kotero moyo wanu ndi unsembe zakhalabe, ndipo zikuyenera kukhalabe kudzera mwa inu ndi m’badwo wanu mpaka kubwenzeretsa kwa zinthu zonse zoyankhulidwa ndi m’kamwa mwa aneneri oyera kuyambira chiyambi cha dziko.
11Â Kotero, odala muli inu ngati mupitiriza mu ubwino wanga, kuunika kwa Amitundu, ndi kudzera mu unsembe uwu, mpulumutsi kwa anthu anga Israeli. Ambuye anena izi. Ameni.