Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 66


Gawo 66

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Okotobala 29, 1831. William E. McLellin adapempha Ambuye mwachinsinsi kuti adziwitse kudzera mwa Mneneri yankho ku mafunso asanu, amene sankadzikwika kwa Joseph Smith. Popemphedwa ndi McLellin, Mneneri adafunsa kwa Ambuye ndipo adalandira vumbulutsoli.

1–4, Pangano losatha ndi chidzalo cha uthenga wabwino; 5–8, Akulu akuyenera kulalikira, kupereka umboni, komanso kukambirana ndi anthu; 9–13, Ntchito ya utumiki okhulupirika imatsimikizira cholowa cha moyo wosatha.

1 Taonani, akutero Ambuye kwa mtumiki wanga William E. McLellin—Ndiwe odala, pamene iwe watembenuka kuchokera ku mphulupulu zako, ndopo walandira zoonadi zanga, atero Ambuye Muwomboli wako, Mpulumutsi wa dziko, ngakhale wa onse amene akhulupilira mu dzina langa.

2 Indetu ndikunena kwa iwe, ndiwe odala pakulandira pangano langa losatha, ngakhale chidzalo cha uthenga wanga wabwino, wotumizidwa kwa ana a anthu, kuti iwo akathe kukhala moyo ndi kupangidwa olandira ma ulemelero amene adzaululidwe mu masiku otsiriza, monga zidalembedwera ndi aneneri ndi atumwi mu masiku akale.

3 Indetu ndikunena kwa iwe, mtumiki wanga William, kuti iwe ndi oyera, koma osati konse; lapa, kotero, pa zinthu izo zimene sizili zokondweretsa pamaso panga, atero Ambuye, pakuti Ambuye adzazionetsa izo kwa iwe.

4 Ndipo tsopano, indetu, ine, Ambuye, ndidzaonetsa kwa iwe chimene ine ndikufuna zokhudzana ndi iwe, kapena chimene chili chifuniro changa pazokhudzana ndi iwe.

5 Taona, indetu ndikunena kwa iwe, kuti ndi chifuniro changa kuti iwe ulengeze uthenga wanga wabwino kuchokera ku malo ndi malo, ndipo kuchokera ku mzinda ndi mzinda, inde, mu zigawo izo zozungulira zimene siudalengezedwe.

6 Usadikire masiku ambiri mu malo ano; usapite kaye ku dziko la Ziyoni, koma pamene iwe ungathe kutumiza, tuma, apo ayi, usaganizire za katundu wako.

7 Pita ku maiko akum’mawa, chitira umboni mu malo aliwonse, kwa anthu onse, ndi mu masunagoge awo, kukambirana ndi anthu.

8 Mulekeni mtumiki wanga Samuel H. Smith apite nawe, ndipo usamusiye iye. Ndipo umupatse malangizo ako; ndipo iye amene ali wokhulupirika adzapangidwa wamphamvu mu malo aliwonse; ndipo ine, Ambuye, ndidzapita nanu,

9 Sanjikani manja anu pa odwala, ndipo iwo adzachira. Musabwelere kufikira ine, Ambuye ndidzakutumizeni. Khalani opilira mu masautso. Pemphani, ndipo mudzalandira; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.

10 Musafunefune kukhala okhumudwa. Musiye kusalungama konse. Musachite chigololo—yesero limene inu mwavutitsidwa nalo.

11 Sungani zonena izi, pakuti ndi zoona ndi zokhulupirika; ndipo inu mudzakuza udindo wanu, ndi kukankhira anthu ambiri ku Ziyoni ndi nyimbo za chisangalalo chosatha pa mitu yawo.

12 Pitilizani mu zinthu izi ngakhale kufikira kumepeto, ndipo mudzakhala ndi kolona wa moyo waosatha pa dzanja lamanja la Atate anga, amene ali odzadza ndi chisomo ndi choonadi.

13 Indetu, akutero Ambuye Mulungu wanu, Muwomboli wanu, ngakhale Yesu Khristu. Ameni.