Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 74


Gawo 74

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Dera la Wayne, New York, mu 1830. Ngakhale kukhazikitsidwa kwa Mpingo kusadayambe, mafunso adali atabuka okhudza njira yoyenera ya ubatizo, zomwe zidatsogolera Mneneri kufunafuna mayankho pankhaniyi. Mbiri ya Joseph Smith imanena kuti vumbulutso ili ndi kufotokozera kwa 1 Akorinto 7:14, malemba oyera omwe nthawi zambiri ankagwiritsidwa ntchito kuti alungamitse ubatizo wa ana.

1–5, Paulo alangiza Mpingo wa m’tsiku lake kuti asasunge chilamulo cha Mose; 6–7, Ana aang’ono ali oyera ndipo amayeretsedwa kudzera mu Chitetezero.

1 Pakuti mwamuna wosakhulupilirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupilira ayeretsedwa mwa mwamunayo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka koma tsopano akhala oyera.

2 Tsopano, m’masiku a atumwi lamulo la mdulidwe lidali pakati pa Ayuda onse amene sadakhulupilire uthenga wabwino wa Yesu Khristu.

3 Ndipo zidachitika kuti padabuka mkangano waukulu pakati pa anthu wokhudzana ndi lamulo la mdulidwe, pakuti mwamuna wosakhulupilira ankafuna kuti ana ake adulidwe ndi kukhala pansi pa chilamulo cha Mose, chimene chidakwaniritsidwa.

4 Ndipo zidachitika kuti anawo, akuleredwa pansi pa chilamulo cha Mose, adamvera miyambo ya makolo awo, ndipo sadakhulupilire uthenga wabwino wa Khristu, m’menemo iwo adakhala osayera.

5 Kotero, chifukwa cha ichi mtumwi adalembera kwa mpingo, kuwapatsa iwo lamulo, osati la Ambuye, koma la iye yekha, kuti wokhulupilira asaphatikizidwe ndi wosakhulupilira; pokhapokha chilamulo cha Mose chikuyenera chithetsedwe pakati pawo;

6 Kuti ana awo akhale opanda mdulidwe; ndi kuti mwambo ukathe kuthetsedwa, umene umanena kuti ana aang’ono ndi osayera; pakuti udali wa pakati pa Ayuda;

7 Koma ana aang’ono ndi oyera, kukhala oyeretsedwa kudzera mu chitetezero cha Yesu Khristu; ndipo ichi ndi chimene malembo amatanthauza.