Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 127


Gawo 127

Kalata yochokera kwa Joseph Smith Mneneri kwa Oyera Mtima a M’masiku Otsiriza ku Nauvoo, Illinois, yokhala ndi malangizo pa ubatizo wa akufa, ku Nauvoo, Seputembala 1, 1842.

1–4, Joseph Smith akondwera mu mazunzo ndi masautso; 5–12, Zolemba zikuyenera kusungidwa zokhudzana ndi maubatizo a akufa.

1 Chifukwa chakuti Ambuye waululira kwa ine kuti adani anga, onse mu Missouri ndi Boma lino, adalinso akundilondola; ndipo popeza anditsata ine popanda chifukwa, ndipo alibe mthunzi waung’ono kapena maonekedwe a chilungamo kapena kumbali yawo pakuwutsa mazunzo awo kwa ine; ndipo popeza kuti zotsutsa zawo zili zozikidwa mu bodza la utoto wakuda kwambiri, ndaganiza kuti ndikofunika ndi nzeru mwa ine kusiya malowa kwa nyengo yochepa, chifukwa cha chitetezo changa ndi chitetezero cha anthu awa. Ndikufuna kunena kwa onse amene ndimachita nawo malonda, kuti ndasiya zinthu zanga kwa othandizira ndi akalaliki omwe adzachita malonda onse mwachangu komanso moyenera, ndipo adzaona kuti ngongole zanga zonse zaperekedwa mu nthawi yake, mwa kubweza katundu, kapena mwanjira ina, monga momwe zingafunikire, kapena momwe zochitika zingavomerezere. Ndikadzamva kuti mphepo yamkuntho yabalalika, pamenepo ndidzabweranso kwa inu.

2 Ndipo za zoopsa zomwe ndaitanidwa kuti ndidutsemo, ndikuziona ngati zazing’ono kwa ine, pamene nsanje ndi mkwiyo wa anthu zakhala mbali yanga masiku onse a moyo wanga; ndipo pachifukwa chake zimaoneka zachinsinsi, kupatula kuti ine ndidadzodzedwa kuyambira asadaikidwe maziko a dziko lapansi ku cholinga chabwino, kapena choipa, monga momwe mungasankhire kuzitchulira. Weruzani nokha. Mulungu akudziwa zonsezi, ngati zili zabwino kapena zoipa. Komabe, madzi akuya ndi omwe ndimakonda kusambiramo. Zonsezi zakhala chikhalidwe chachiwiri kwa ine; ndipo ndikumva, monga Paulo, kudzitamandira m’masautso; pakuti kufikira lero Mulungu wa makolo anga adawawombola mwa iwo onse, ndipo adzandilanditsa kuyambira tsopano; pakuti taonani, ndidzapambana adani anga onse, pakuti Ambuye Mulungu wanena izi.

3 Kotero, oyera mtima onse akondwere, ndikukhala osangalala kwambiri; pakuti Mulungu wa Israeli ndiye Mulungu wawo, ndipo adzawabwenzera mphotho ya olungama pamitu ya opondereza awo onse.

4 Ndiponso, indetu atero Ambuye: Lolani ntchito ya kachisi wanga, ndi ntchito zonse zimene ine ndaziika kwa inu, zipitilirebe ndipo zisaleke; ndipo lolani khama lanu, ndi kuleza mtima kwanu, ndi kupilira, ndi ntchito zanu zionjezereke, ndipo inu simudzataya konse mphotho yanu, akutero Ambuye wa makamu. Ndipo ngati iwo akuzunzani, adazunzanso aneneri ndi anthu olungama omwe adalipo inu musadabadwe. Pa zonsezi pali mphoto kumwamba.

5 Ndiponso, ine ndikupereka kwa inu mawu okhudzana ndi ubatizo wa akufa anu.

6 Indetu, akutero Ambuye kwa inu zokhudzana ndi akufa anu: Pamene wina wa inu abatizidwa chifukwa cha akufa anu, pakhale wolemba, ndipo muloleni iye akhale mboni yoonelera maubatizo anu; muloleni iye amve ndi makutu ake, kuti achitire umboni choonadi, atero Ambuye;

7 Kuti mu zolembedwa zanu zonse zikathe kulembedwa kumwamba; chilichonse chimene mwachimanga pa dziko lapansi, chikathe kukhala chomangidwa kumwamba; chilichonse chimene mwachimasula pa dziko lapansi, chikathe kukhala chomasulidwa kumwamba;

8 Pakuti ndidzabwenzeretsa zinthu zambiri padziko lapansi za unsembe, atero Ambuye wa Makamu.

9 Ndiponso, lolani zolemba zonse zikhale ndi dongosolo, kuti zikathe kuikidwa mu zosungiramo zakale za kachisi wanga woyera, kuti zisungidwe mu chikumbutso kuchokera ku m’badwo kupita ku m’badwo, akutero Ambuye Wamakamu.

10 Ndidzanena kwa oyera mtima onse, kuti ndidakhumba, ndi chikhumbo chachikulu kwambiri, kuti ndiyankhule nawo kuchokera pa gome pa nkhani ya ubatizo wa akufa, pa Sabata lotsatira. Koma chifukwa sizili mwa mphamvu yanga kutero, ndidzalemba mawu a Ambuye ku nthawi ndi nthawi, pa mutu umenewo, ndi kuwatumiza iwo kwa inu mwa makalata, komanso zinthu zina zambiri.

11 Tsopano ndikutseka kalata yanga pa nthawi ino, chifukwa chofuna nthawi yochulukirapo; pakuti mdani ali tcheru, ndipo monga Mpulumutsi adanena, karonga wa dziko lapansi adza, koma alibe kanthu mwa ine.

12 Taonani, pemphero langa kwa Mulungu ndilokuti inu nonse mupulumutsidwe. Ndipo ine ndadzilembera ndekha wantchito wanu mwa Ambuye, mlosi ndi wamasomphenya wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza.

Joseph Smith.