Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 108


Gawo 108

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Disembala 26, 1835. Gawo ili lidalandiridwa pa pempho la Lyman Sherman, amene adali poyamba adadzodzedwa m’modzi wa atsogoleri asanu ndi awiri a Makumi Asanu ndi Awiri ndi amene adabwera kwa Mneneri ndi pempho la vumbulutso lodziwitsa udindo wake.

1–3, Lyman Sherman akhululukidwa machimo ake; 4–5, Iye akuyenera kuwerengedwa ndi akulu otsogolera a Mpingo; 6–8, Iye aitanidwa kukalalikira uthenga wabwino ndi kulimbikitsa abale ake.

1Ā Indetu akutero Ambuye kwa iwe, mtumiki wanga Lyman: Machimo ako akhululukidwa, chifukwa iwe wamvera mawu anga pobwera kuno m’mawa uno kudzalandira langizo kwa iye amene ine ndamusankha.

2Ā Kotero, mzimu wako upumule zokhudza maimidwe ako auzimu, ndipo usakanenso mawu anga.

3Ā Ndipo dzuka ndi kukhala wosamala kwambiri kuyambira tsopano mu kusunga malonjezo ako, amene iwe udapanga ndipo ukupanga, ndipo iwe udzadalitsidwa ndi madalitso aakulu kwambiri.

4Ā Dikira modekha kufikira msonkhano waukulu udzaitanidwe ndi atumiki anga, pamenepo mudzakumbukiridwa pamodzi ndi akulu anga oyamba, ndi kulandira ufulu mwa kudzodzedwa pamodzi ndi akulu anga onse amene ine ndawasankha.

5Ā Taona, ili ndi lonjezo la Atate kwa iwe ngati iwe upitiliza kukhulupirika.

6Ā Ndipo chidzakwaniritsidwa pa iwe mu tsiku limenelo limene iwe udzakhala ndi ufulu wolalikira uthenga wanga kulikonse kumene ine ndidzakutuma iwe, kuyambira pa nthawi imeneyo.

7Ā Kotero, limbikitsa abale ako mu zoyankhula zako zonse, mu mapemphero ako onse, mu chilimbikitso chako chonse ndi muzochita zako zonse.

8Ā Ndipo taona, ndipo ona, Ine ndili nawe kuti ndikudalitse ndi kukupulumutsa iwe kwamuyaya. Ameni.