Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 91


Gawo 91

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Malitchi 9, 1833. Mneneri panthawiyi adali atatanganidwa mu kumasulira kwa Chipangano Chakale. Atafika ku gawo la malemba akale otchedwa Apokrifa, iye adafunsa Ambuye ndipo adalandira langizo ili.

1–3, Apokrifa ndi lomasulilidwa molondola koma lili ndi zomasulira zambiri ndi manja a anthu zimene sizoona; 4–6, Zimapindulira iwo owunikiridwa ndi Mzimu.

1 Indetu, atero Ambuye kwa inu zokhudzana ndi Apokrifa—Muli zinthu zambiri zomwe zili m’menemo zomwe ndizoona, ndipo mochuluka zamasuliridwa molondola;

2 Muli zinthu zambiri zomwe zili m’menemo zimene sizoona, zimene zili zomasuliridwa pa manja a anthu.

3 Indetu, ndikunena kwa iwe, kuti izo sizofunikira kuti Apokrifa amasuliridwe,

4 Kotero, amene aliwerenga ilo, mloleni iye amvetse, pakuti Mzimu umaonetsera choona;

5 Ndipo amene waunikiridwa ndi Mzimu adzapeza phindu lake m’menemo;

6 Ndipo amene salandira mwa Mzimu, sangapindule. Kotero sikofunikira kuti limasuliridwe. Ameni.