Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 70


Gawo 70

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, Novembala 12, 1831. Mbiri ya Mneneri imakamba kuti misonkhano yapadera inayi idachitika kuyambira pa 1 mpaka pa 12 Novembala, yoonjezedwa. Mu womaliza wa misonkhanoyi, kufunikira kwakukulu kwa mavumbulutso amene adzasindikizidwe pambuyo pake ngati Book of Commandments ndipo kenako Chiphunzitso ndi Mapangano adaganiziridwa. Vumbulutso ili lidaperekedwa potsatira chisankho cha msonkhanowo kuti mavumbulutsowo adali “ofunika ku Mpingo chuma cha dziko lonse lapansi.” Mbiri ya Joseph Smith imatchula mavumbulutsowa kuti “maziko a Mpingo mu masiku ano otsiriza, ndipo opindulitsa ku dziko, kuonetsera kuti mafungulo a zinsinsi za ufumu wa Mpulumutsi wathu aperekedwanso kwa munthu.”

1–5, Adindo asankhidwa kuti asindikize mavumbulutso; 6–13, Iwo amene amagwira ntchito mu zinthu za uzimu ndi woyenera malipiro awo; 14–18, Oyera Mtima akuyenera kukhala ofanana mu zinthu zakuthupi.

1 Taonani, ndipo mvetserani, O inu okhala mu Ziyoni, ndi anthu nonse a mpingo wanga amene muli kutali, ndipo mverani mawu a Ambuye amene ine ndapereka kwa mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndiponso kwa mtumiki wanga Martin Harris, ndipo kwa mtumiki wanga Oliver Cowdery, ndiponso kwa mtumiki wanga John Whitmer, ndiponso kwa mtumiki wanga Sidney Rigdon, ndiponso kwa mtumiki wanga William W. Phelps, mwa njira ya lamulo kwa iwo.

2 Pakuti ndapereka kwa iwo lamulo; kotero mvetserani ndipo imvani, pakuti atero Ambuye kwa iwo—

3 Ine, Ambuye, ndawasankha iwo, ndikuwadzodza iwo kukala adindo pa mavumbulutso ndi malamulo amene ine ndawapereka kwa iwo, ndipo amene ndidzapereke pambuyo pake kwa iwo;

4 Ndipo kulongosola kwa udindowu ndidzakufuna kwa iwo mu tsiku la chiweruzo.

5 Kotero, ndawasankhira kwa iwo, ndipo iyi ndi ntchito yawo mu mpingo wa Mulungu, kuti azisamalire izo ndi zokhudza zimenezo, inde, phindu lake.

6 Kotero, lamulo ine ndikupereka kwa inu, kuti iwo asadzapereke zinthu izi ku mpingo, ngakhale ku dziko;

7 Komabe, pamene iwo alandira zochuluka kuposa zoyenelera pa zofinikira zawo ndi zosowa zawo, zidzaperekedwa ku nkhokwe yanga;

8 Ndipo phindulo lidzapatulidwa kwa okhala mu Ziyoni, ndi kwa mibadwo yawo, pamene iwo akhala acholowa molingana ndi malamulo a ufumu.

9 Taonani, izi ndi zimene Ambuye akufuna kwa munthu aliyense mu udindo wake, ngakhale monga ine, Ambuye, ndasankhira kapena ndidzasankhire pambuyo pake kwa munthu aliyense.

10 Ndipo taonani, palibe amene sakukhudzidwa kuchokera ku lamuloli amene ali wa mpingo wa Mulungu wamoyo;

11 Inde, ngakhale bishopu, ngakhale mtumiki amene akusunga nkhokwe ya Ambuye, ngakhale iye amene wasankhidwa mu udindo wa zinthu zakuthupi.

12 Iye amene wasankhidwa kuti aziyang’anira zinthu za uzimu, yemweyo ndi woyenera malipiro ake, ngakhale monga iwo amene ali osankhidwa ku udindo woyang’anira mu zinthu zakuthupi;

13 Inde, ngakhale mochuluka kwambiri, kumene kuchulukako kwachulukitsidwa kwa iwo kudzera mu maonetseredwe a Mzimu.

14 Komabe, mu zinthu zanu zakuthupi mudzakhala ofanana, ndipo izi osati monyinyirika, apo ayi kuchuluka kwa maonetseredwe a Mzimu kudzachotsedwa.

15 Tsopano, lamulo ili ndikupereka kwa atumiki anga kuti ziwapindulire pamene iwo adakali, pa maonetseredwe a madalitso anga pa mitu yawo, ndi mphotho ya khama lawo ndi chitetezo chawo;

16 Pa chakudya ndi chovala; pa cholowa; pa nyumba ndi pa malo, mu nyengo iliyonse ine, Ambuye, ndidzawaika iwo, ndipo kwinakulikonse ine, Ambuye, ndidzawatuma iwo.

17 Pakuti iwo akhala okhulupirika pa zinthu zambiri, ndipo achita bwino pamene iwo sadachimwe.

18 Taonani, ine, Ambuye, ndili wachifundo ndipo ndidzawadalitsa iwo, ndipo iwo adzalowa mu chikondwelero cha zinthu izi. Ngakhale choncho. Ameni.