Gawo 103
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Febuluwale 24, 1834. Vumbulutso ili lidalandiridwa tsiku lomwelo lofikira ku Kirtland, Ohio, la Parley P. Pratt ndi Lyman Wight, amene adabwera kuchokera ku Missouri kudzakambirana ndi Mneneri monga momwe angathandizire ndi kubwenzeretsera Oyera mtima ku malo awo mu dera la Jackson.
1–4, Chifukwa chiyani Ambuye adalolera Oyera mtima mu dera la Jackson kuti azunzidwe; 5–10, Oyera mtima adzapambana ngati iwo asunga malamulo; 11–20, Chiwombolo cha Ziyoni chidzabwera mwa mphamvu, ndipo Ambuye adzapita patsogolo pa anthu Ake; 21–28, Oyera Mtima akuyenera kusonkhana mu Ziyoni, ndipo iwo amene ataya miyoyo yawo adzaipezanso; 29–40, Abale osiyanasiyana aitanidwa kuti akhazikitse Msasa wa Ziyoni, ndi kupita ku Ziyoni; iwo alonjezedwa chipambano ngati akhala okhulupirika.
1 Indetu ndinena kwa inu, abwenzi anga, taonani, ndidzapereka kwa inu vumbulutso ndi lamulo, kuti inu muthe kudziwa m’mene mungachitire ntchito zanu zokhudzana chipulumutso ndi chiwombolo cha abale anu, amene abalalitsidwa mu dziko la Ziyoni;
2Â Pothamangisidwa ndi kukanthidwa ndi manja a adani anga, pa amene ine ndidzatsanulira mkwiyo wanga wopanda muyezo mu nthawi yanga.
3Â Pakuti ndawalora iwo kufikira tsopano, kuti iwo akathe kudzadza mlingo wa mphulupulu zawo, kuti chikho chawo chikathe kudzadza;
4Â Ndipo kuti iwo amene amadzitchula okha pa dzina langa akathe kulangidwa kwa ka nyengo kochepa ndi chilango choopsya ndi chowawa, chifukwa iwo sadamvetsere kwathunthu ku mfundo ndi malamulo amene ine ndidapereka kwa iwo.
5Â Koma indetu ndinena kwa inu, kuti ndalamula lamulo limene anthu anga adzazindikira, kufikira kuti pamene iwo amvetsera kuyambira pa ola lomwe lino ku malangizo amene ine, Ambuye Mulungu wawo, ndidzapereka kwa iwo.
6Â Taonani iwo, pakuti ndachilengeza ichi, adzayamba kupambana motsutsana ndi adani anga kuyambira ku ola lomwelino.
7Â Ndipo pa kumvetsera kusunga mawu anga onse amene ine, Ambuye Mulungu wawo, ndidzawayankhule kwa iwo, iwo sadzaleka kupambana kufikira maufumu apadziko atagonjetsedwa pansi pa mapazi anga, ndipo dziko lapansi lapatsidwa kwa oyera mtima, kuti alitenge ilo kunthawi za nthawi.
8Â Koma pamene iwo sasunga malamulo anga, ndi kusamvetsera kusunga mawu anga wonse, maufumu apa dziko adzawapambana iwo.
9Â Pakuti iwo adaikidwa kukhala kuwala kwa dziko, ndipo kukhala apulumutsi a anthu;
10Â Ndipo pamene iwo si apulumutsi a anthu, iwo ali monga mchere umene wataya kukoma kwake, ndipo tsopano ndi wopanda phindu koma kutaidwa ndi kupondedwa pansi pamapazi a anthu.
11Â Koma indetu ndikunena kwa inu, ndalamula kuti abale anu amene abalalitsidwa adzabwelera ku malo a zolowa zawo, ndipo adzamanga malo abwinja a Ziyoni.
12Â Pakuti pambuyo pa masautso ochuluka, monga ine ndanena kwa inu mu lamulo lakale, pamabwera mdalitso.
13 Taonani, ili ndi dalitso limene ine ndalonjeza pambuyo pa masautso anu, ndi masautso a abale anu—chiwombolo chanu, ndi chiwombolo cha abale anu, ngakhale chibwenzeretso chawo ku dziko la Ziyoni, kukakhazikika, osadzagwetsedwanso.
14Â Komabe, ngati iwo aipitsa zolowa zawo iwo adzagwetsedwa; pakuti ine sindidzawalekelera iwo ngati iwo aipitse zolowa zawo.
15Â Taonani, ndikunena kwa inu, chiwombolo cha Ziyoni chikuyenera kubwera mwa mphamvu;
16Â Kotero, ndidzadzutsira kwa anthu anga munthu, amene adzawatsogolera iwo monga Mose adatsogolera ana a Israeli.
17Â Pakuti inu ndi ana a Israeli, ndipo a mbewu ya Abrahamu, ndipo mukuyenera kutsogoleledwa kuchoka kuukapolo ndi mphamvu, ndipo ndi dzanja lotambasulidwa.
18Â Ndipo monga makolo anu adatsogozedwera pachiyambi, ngakhale momwemo chiwombolo cha Ziyoni chidzakhala.
19Â Kotero, mitima yanu isafooke, pakuti ine sindikunena kwa inu monga ndidanenera kwa makolo anu: Angelo anga adzapita patsogolo panu, koma osati kupezeka kwanga.
20Â Koma ine ndikunena kwa inu: Angelo anga adzapita patsogolo panu, ndiponso kupezeka kwanga, ndipo mu nthawi yake inu mudzalandira dziko labwino.
21Â Indetu, indetu ndinena kwa inu, kuti mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi munthu amene ine ndimufaniza kwa mtumiki amene Ambuye wa munda wa mpesa adayankhula mu fanizo limene ine ndapereka kwa inu.
22 Kotero mloleni mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., anene kwa mphamvu za nyumba yanga, amsinkhu wachisodzera ndi achinyamata anga—Sonkhanani nokha pamodzi ku dziko la Ziyoni, pa dziko limene ine ndagula ndi ndalama zimene zapatulidwa kwa ine.
23Â Ndipo lolani mipingo yonse itumize anthu anzeru ndi ndalama zawo, ndi kugula malo ngakhale monga ine ndawalamulira.
24Â Ndipo pamene adani anga abwera motsutsana nanu kuti akuthamangitseni inu kuchokera ku malo anga abwino, amene ine ndawapatulira kukhala dziko la Ziyoni, ngakhale kuchokera ku malo anu malinga ndi maumboni awa, amene inu mwagula pamaso panga motsutsana nawo, inu mudzawatembelere iwo;
25Â Ndipo aliyense amene inu mwamutembelera, ine ndadzamutembelera, ndipo inu mudzandibwenzela adani anga.
26 Ndipo kupezeka kwanga kudzakhala nanu ngakhale mukubwenzera kwa adani anga, kufikira m’badwo wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.
27Â Munthu asaope kutaya moyo wake chifukwa cha ine; pakuti aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha ine adzaupezanso.
28Â Ndipo amene sakufuna kutaya moyo wake chifukwa cha ine si wophunzira wanga.
29 Ndichifuniro changa kuti mtumiki wanga Sidney Rigdon akakweze mawu ake mu mipingo ya ku maiko a kum’mawa, pokonzekeretsa mipingoyo kusunga malamulo amene ine ndapereka kwa iwo okhudzana ndi chibwenzeretso ndi chiwombolo cha Ziyoni.
30 Ndi chifuniro changa kuti mtumiki wanga Parley P. Pratt ndi mtumiki wanga Lyman Wight asabwelere ku dziko la abale awo, kufikira iwo atapeza magulu oti akapite ku dziko la Ziyoni, mwa makumi, kapena mwa Makumi awiri, kapena mwa makumi asanu, kapena mwa mazana, kufikira iwo atapeza mpaka chiwerengero cha mazana asanu a mphamvu za nyumba yanga.
31Â Taonani ichi ndi chifuniro changa; pemphani ndipo mudzalandira; koma anthu sachita chifuniro changa nthawi zonse.
32Â Kotero, ngati inu simungathe kupeza mazana asanu, funafunani mwakhama kuti mwina mukathe kupeza mazana atatu.
33Â Ndipo ngati simungathe kupeza mazana atatu, funafunani mwakhama kuti mwina mukathe kupeza zana limodzi.
34Â Koma indetu ndikunena kwa inu, lamulo ndikupereka kwa inu, kuti musadzapite ku dziko la Ziyoni kufikira inu mutapeza zana limodzi za mphamvu za nyumba yanga, kuti zipite nanu ku dziko la Ziyoni.
35Â Kotero, monga ine ndanena kwa inu, pemphani ndipo mudzalandira; pempherani kwambiri kuti mwina mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., akathe kupita nanu, ndi kutsogolera pakati pa anthu anga, ndi kukhazikitsa ufumu wanga pa dziko lopatulidwalo, ndi kukhazikitsa ana a Ziyoni pa zilamulo ndi malamulo amene alipo ndi amene adzaperekedwe kwa inu.
36Â Chigonjetso chonse ndi ulemelero zimabwera kwa inu kudzera ku khama lanu, kukhulupirika ndi mapemphero a chikhulupiliro.
37 Mloleni mtumiki wanga Parley P. Pratt ayende ndi mtumiki wanga Joseph Smith, Jun.
38Â Mloleni mtumiki wanga Lyman Wight ayende ndi mtumiki wanga Sidney Rigdon.
39 Mloleni mtumiki wanga Hyrum Smith ayende ndi mtumiki wanga Frederick G. Williams.
40 Mloleni mtumiki wanga Orson Hyde ayende ndi mtumiki wanga Orson Pratt, kwinakulikonse mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., adzawauza iwo, mu kupeza chikwaniritso cha malamulo amene ine ndapereka kwa inu, ndi kusiya zotsarazo m’manja mwanga. Ngakhale choncho. Ameni.