Gawo 84
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Seputembala 22 ndi 23, 1832. Mu mwezi wa Seputembala, akulu adayamba kubwelera kuchokera ku ma utumiki awo ku maiko a kum’mawa ndi kupereka malipoti a ntchito zawo. Padali pamene iwo adali limodzi mu nyengo imeneyi ya chisangalalo kuti malangizo otsatirawa adalandiridwa. Mneneri adaliika kukhala vumbulutso pa unsembe.
1–5, Yerusalemu Watsopano ndi kachisi zidzamangidwa ku Missouri; 6–17, Mndandanda wa unsembe kuchokera kwa Mose mpaka Adamu uperekedwa; 18–25, Unsembe waukulu umakhala ndi mafungulo a chidziwitso cha Mulungu; 26–32, Unsembe waung’ono umakhala ndi mafungulo a utumiki wa angelo ndi kukonzekera uthenga wabwino; 33–44, Anthu amapeza moyo wosatha kudzera ku lumbiro ndi pangano la unsembe; 45–53, Mzimu wa Khristu umazindikiritsa anthu, ndipo dziko lagona mu uchimo; 54–61, Oyera mtima akuyenera kuchitira umboni wa zinthu zomwe iwo azilandira; 62–76, Iwo akuyenera kulalikira uthenga wabwino, ndipo zizindikiro zidzatsatira; 77–91, Akulu akuyenera kupita opanda chikwama kapena thumba, ndipo Ambuye adzasamalira zosowa zawo; 92–97, Miliri ndi matembelero akuyembekezera iwo amene akana uthenga wabwino; 98–102, Nyimbo yatsopano ya chiwombolo cha Ziyoni iperekedwa; 103–110, Lolani munthu aliyense aime mu udindo wake ndi kugwira ntchito mu maitanidwe ake; 111–120, Atumiki a Ambuye akuyenera kulengeza chonyansa cha kupululutsa cha masiku omaliza.
1 Vumbulutso la Yesu Khristu kwa mtumiki wake Joseph Smith, Jun., ndi akulu asanu ndi m’modzi, pamene adalumikiza mitima yawo ndi kukweza mawu awo kumwamba.
2Â Inde, mawu a Ambuye okhudzana ndi mpingo wake, wokhazikitsidwa mu masiku omaliza pa chibwenzeretso cha anthu ake, monga iye wayankhulira ndi pakamwa pa aneneri ake, ndi pakusonkhana kwa oyera ake kukaima pa Phiri la Ziyoni, limene lidzakhale mzinda wa Yerusalemu Watsopano.
3Â Umene mzinda wake udzamangidwa, kuyambira pa malo a kachisi, amene asankhidwa ndi chala cha Ambuye, mu malire a kumadzulo kwa Dziko la Missouri, ndi kupatulidwa ndi dzanja la Joseph Smith, Jun., ndi ena amene Ambuye adali okondwera nawo.
4 Indetu awa ndi mawu a Ambuye, kuti mzinda wa Yerusalemu Watsopano udzamangidwe ndi kusonkhanitsidwa kwa oyera mtima, kuyambira pa malo awa, ngakhale malo a kachisi, amene kachisi wake adzazikidwa mu m’badwo omwe uno.
5 Pakuti indetu m’badwo uno sudzapita kufikira nyumba idzamangidwe kwa Ambuye, ndipo mtambo udzatsikira pa iyo, umene mtambowo udzakhala ulemelero wa Ambuye, umene udzadzadza m’nyumbayo.
6Â Ndipo ana aamuna a Mose, molingana ndi Unsembe Woyera umene iye adalandira pansi pa dzanja la apongozi ake Yetero;
7Â Ndipo Yetero adaulandira pansi pa dzanja la Kalebe;
8Â Ndipo Kalebe adaulandira pansi pa dzanja la Elihu;
9Â Ndipo Elihu pansi pa dzanja la Yeremiya;
10Â Ndipo Yeremiya pansi pa dzanja la Gadi;
11Â Ndipo Gadi pansi pa dzanja la Yesaya;
12Â Ndipo Yesaya adaulandira pansi pa dzanja la Mulungu.
13 Ndipo Yesaya adakhala mu masiku a Abrahamu, ndipo adali odalitsidwa ndi iye—
14 Umene Abrahamu adaulandira unsembewo kuchokera kwa Melkizedeki, amene adaulandira kudzera mu m’badwo wa makolo ake, ngakhale kufikira Nowa;
15 Ndipo kuchokera kwa Nowa kufikira Enoki, kudzera m’badwo wa makolo awo;
16 Ndipo kuchokera kwa Enoki mpaka Abele, amene adaphedwa ndi chiwembu cha m’bale wake, amene adalandira unsembe mwa malamulo a Mulungu, ndi dzanja la Atate ake Adamu, amene adali munthu woyamba—
17Â Umene unsembewu ukupitilira mu mpingo wa Mulungu mu mibadwo yonse, ndipo ulibe chiyambi cha masiku kapena mathero a zaka.
18 Ndipo Ambuye adatsimikiziranso unsembe pa Aroni ndi mbewu yake, m’mibadwo yawo yonse, umene unsembe wake ukupitiliranso ndi kukhala kwamuyaya ndi unsembe umene ukutsatira dongosolo loyera la Mulungu.
19Â Ndipo unsembe waukulu umenewu umatumikira uthenga wabwino ndi kusunga mafungulo a zinsinsi za ufumu, ngakhale mafungulo a chidziwitso cha Mulungu.
20Â Kotero, mu miyambo yake, mphamvu ya umulungu imaonekera,
21Â Ndipo kupanda miyambo yakeyo, ndi ulamuliro wa unsembe, mphamvu ya umulungu singaonekere kwa anthu mu thupi;
22Â Pakuti popanda ichi palibe munthu amene angaone nkhope ya Mulungu, ngakhale Atate, ndi kukhala moyo.
23Â Tsopano Mose ameneyu adaphunzitsa momveka bwino kwa ana a Israeli mu chipululu, ndipo adafuna mwakhama kuti ayeretse anthu ake kuti iwo akathe kuona nkhope ya Mulungu;
24 Koma iwo adalimbitsa mitima yawo ndipo sakadatha kupilira kupezeka kwake; kotero, Ambuye mu ukali wake, pakuti mkwiyo wake udayaka motsutsana nawo, adalumbira kuti iwo asalowe mu mpumulo wake pamene ali m’chipululu, umene mpumulowo ndi chidzalo cha ulemelero wake.
25Â Kotero, iye adatenga Mose kuchoka pakati pawo, ndi Unsembe Oyera womwe;
26 Ndipo unsembe waung’ono udapitilira, umene unsembewo umakhala ndi mafungulo a utumiki wa angelo ndi kukonzekera uthenga wabwino;
27 Umene uthenga wake ndi uthenga wabwino wa kulapa ndi wa ubatizo, ndi wa kuchotsa machimo, ndi lamulo la malamulo azakuthupi lachibadwidwe, amene Ambuye mu mkwiyo wake adachititsa kuti upitilire ndi nyumba ya Aroni pakati pa ana a Israeli kufikira Yohane, amene Mulungu adamudzutsa, pokhala odzadzidwa ndi Mzimu Woyera kuchokera m’mimba mwa mayi wake.
28Â Pakuti iye adabatizidwa pamene iye adakali mu ubwana wake, ndipo adadzodzedwa ndi mngelo wa Mulungu pa nthawi imene adali masiku asanu ndi atatu ku mphamvu imeneyi, kuti agonjetse ufumu wa Ayuda, ndi kukonza njira yopapatiza ya Ambuye pamaso pa nkhope za anthu ake, kuwakonzekeretsa iwo pakubwera kwa Ambuye, amene manja ake apatsidwa mphamvu zonse.
29Â Ndiponso, maudindo a mkulu ndi bishopu ndi ofunika owonjezera okhala ku unsembe waukulu.
30 Ndiponso, maudindo a mphunzitsi ndi dikoni ndi ofunika owonjezera okhala ku unsembe waung’ono, umene unsembewo udatsimikizidwa pa Aroni ndi ana ake aamuna.
31 Kotero, monga ndanena zokhudzana ndi ana aamuna a Mose—pakuti ana aamuna a Mose ndiponso ana aamuna a Aroni adzapereka zopereka zovomerezeka ndi nsembe mu nyumba ya Ambuye, imene nyumbayo idzamangidwa kwa ambuye mu m’badwo uno, pa malo opatulika amene ine ndasankha—
32Â Ndipo ana aamuna a Mose ndi a Aroni adzadzadzidwa ndi ulemelero wa Ambuye, pa Phiri la Ziyoni mu nyumba ya Ambuye, amene ana aamuna ake ndi inu; ndiponso ambiri amene ine ndawaitana ndi kuwatuma kukamanga mpingo wanga.
33Â Pakuti amene ali okhulupirika mpaka kupeza unsembe uwiri umenewu umene ine ndayankhula, ndi kukuza maitanidwe awo, ali oyeretsedwa ndi Mzimu kwa kukonzanso matupi awo.
34Â Iwo amakhala ana aamuna a Mose ndi a Aroni, ndi mbewu ya Abrahamu, ndi mpingo ndi ufumu, ndi osankhidwa a Mulungu.
35Â Ndiponso onse amene alandira unsembe umenewu alandira ine, akutero Ambuye;
36Â Pakuti iye amene alandira atumiki anga amalandira ine;
37Â Ndipo iye amene amalandira ine amalandira Atate;
38Â Ndipo iye amene amalandira Atate amalandira ufumu wa Atate anga; kotero zonse zimene Atate anga ali nazo zidzaperekedwa kwa iye.
39Â Ndipo izi zili molingana ndi lumbiro ndi pangano limene lili ku unsembe.
40Â Kotero, onse amene amalandira unsembewu, amalandira lumbiro ndi pangano la Atate anga, limene sangaliphwanye, ngakhale kulichotsa.
41 Koma amene aphwanya pangano limeneli atatha kulilandira, ndipo pakamodzi n’kubwelera m’mbuyo, sadzakhala ndi chikhululukiro cha machimo ake mu dzikoli kapena mu dziko lilinkudza.
42Â Ndipo tsoka kwa onse amene sabwera ku unsembe uwu umene inu mwaulandira, umene ine tsopano ndikuutsimikizira pa inu amene mwapezeka lero lino, mwa mawu anga kuchoka kumwamba; ndipo ngakhale ndapereka kwa makamu akumwamba ndi angelo anga udindo wokhudza inu.
43Â Ndipo tsopano ndikupatsani inu lamulo kuti muchenjere zokhudza inu eni, kuti mutchere khutu ku mawu a moyo wosatha.
44Â Pakuti mudzakhala moyo ndi liwu lililonse lochokera pakamwa pa Mulungu.
45Â Pakuti mawu a Ambuye ali choonadi, ndipo chilichonse chimene chili choonadi chili kuumika, ndipo chilichonse chimene chili kuunika chili Mzimu, ngakhale Mzimu wa Yesu Khristu.
46Â Ndipo Mzimu umapereka kuunika kwa munthu aliyense amene amabwera kudziko; ndipo Mzimu umazindikilitsa munthu aliyense wapadziko, amene amamvetsera ku mawu a Mzimu.
47Â Ndipo aliyense amene amamvetsera ku mawu a Mzimu amabwera kwa Mulungu, ngakhale Atate.
48Â Ndipo atate amaphunzitsa iye za pangano limene iye walikonzanso ndi kulitsimikizira pa inu, limene latsimikiziridwa pa inu pa ubwino wanu, ndipo osati pa ubwino wanu okha, koma pa ubwino wa dziko lonse.
49Â Ndipo dziko lonse lagona mu uchimo, ndipo likubuula pansi pa mdima ndi pansi pa nsinga za uchimo.
50Â Ndipo mwa ichi inu mungathe kudziwa ali pansi pa nsinga za uchimo, chifukwa iwo sabwera kwa ine.
51Â Pakuti aliyense osabwera kwa ine ali pansi pa nsinga za uchimo.
52Â Ndipo amene salandira mawu anga samawadziwa mawu anga, ndipo sali wa ine.
53Â Ndipo mwa ichi mungathe kudziwa olungama kuchokera kwa oipa, ndipo kuti dziko lonse libuula pansi pa tchimo ndi mdima ngakhale tsopano.
54 Ndipo mu malingaliro anu mu nthawi yapitayo adali odetsedwa chifukwa cha kusakhulupilira, ndipo chifukwa mwapeputsa zinthu zimene mwazilandira—
55Â Zimene zachabechabe ndi kusakhulupilira zabweretsa mpingo wonse pansi pa chiweruzo.
56Â Ndipo chiweruzo chimenechi chakhala pa ana a Ziyoni, ngakhale onse.
57 Ndipo iwo adzakhalabe pansi pa chiweruzochi kufikira iwo atalapa ndi kukumbukira pangano latsopano, ngakhale Buku la Mormoni, ndi malamulo akale amene ine ndawapatsa, osati kungonena, koma kuwachita molingana ndi chimene ndachilemba—
58Â Kuti iwo akathe kubweretsa chipatso choyenera ku ufumu wa Atate awo; apo ayi kudzakhalabe mliri ndi chiweruzo chotsanulidwa pa ana a Ziyoni.
59Â Pakuti kodi ana a ufumu adzaipitsa dziko langa loyera? Indetu, ndikunena kwa inu, Ayi.
60Â Indetu, indetu, ndinena kwa inu amene tsopano mukumva mawu anga, amene ali mawu anga, odala ndinu pamene mukulandira zinthu izi;
61 Pakuti ndidzakhululukira inu machimo anu ndi lamulo ili—kuti mukhale okhazikika mu malingaliro anu mwa ulemu ndi mzimu wa pemphero, mu kuchitira umboni ku dziko lonse wa zinthu zimene zayankhulidwa kwa inu.
62Â Kotero, pitani ku dziko lonse; ndi ku malo aliwonse amene simungapite mudzatumiza, kuti umboniwu ukathe kupita kuchokera kwa inu kufika kudziko lonse kwa cholengedwa chilichonse.
63Â Ndipo monga ndanena kwa atumwi anga, momwemonso ndikunena kwa inu, pakuti inu ndinu atumwi anga, ngakhale ansembe aakulu a Mulungu; ndinu amene Atate anga andipatsa; ndinu abwenzi anga;
64Â Kotero, monga ndanena kwa atumwi anga ndikunenanso kwa inu, kuti moyo uliwonse umene udzakhulupilira pa mawu anu, ndi kubatizidwa ndi madzi pakuchotsa machimo, udzalandira Mzimu Woyera.
65 Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupilira—
66Â Mu dzina langa iwo adzachita ntchito zambiri zodabwitsa;
67Â Mu dzina langa iwo adzatulutsa ziwanda;
68Â Mu dzina langa iwo adzachilitsa odwala;
69Â Mu dzina langa iwo adzatsegula maso a wakhungu, ndipo kutsegula makutu a wosamva;
70Â Ndipo lilime la wosalankhula lidzayankhula;
71Â Ndipo ngati munthu aliyense adzawapatsa iwo chiphe sichidzawapweteka iwo;
72Â Ndipo njoka za chiphe sizidzakhala ndi mphamvu yowavulaza iwo.
73Â Koma lamulo ndikupereka kwa iwo, kuti iwo asadzitamandire mwa iwo wokha pa zinthu izi, kapena kuziyankhula pamaso pa dziko; pakuti zinthu izi zaperekedwa kwa inu pa phindu lanu ndi chipulumutso.
74Â Indetu, indetu, ndinena kwa inu, iwo amene sakhulupilira pa mawu anu, ndipo sadabatizidwe mu madzi mu dzina langa, ku chikhululukiro cha machimo awo, kuti akathe kulandira Mzimu Woyera, adzawonongedwa, ndipo sadzabwera ku ufumu wa Atate anga kumene Atate anga ndi ine ndili.
75Â Ndipo vumbulutso ili kwa inu, ndi lamulo, zikugwira ntchito kuyambira ola lino pa dziko lonse lapansi, ndipo uthenga wabwino uli kwa onse amene sadaulandire.
76 Koma, indetu ndikunena kwa onse amene ufumu wapatsidwa—kuchokera kwa inu zikuyenera kulalikidwa kwa iwo, kuti iwo adzalape ku ntchito zawo zoipa zakale; pakuti iwo akuyenera kudzudzulidwa pa mitima yawo yoipa ya kusakhulupilira, ndipo abale anu mu Ziyoni chifukwa cha kupandukira kwawo motsutsana nanu pa nthawi yomwe ndidakutumani.
77Â Ndiponso ndikunena kwa inu, abwenzi anga, pakuti kuchokera pano ndidzakutchani abwenzi, ndikofunikira kuti ndikupatseni inu lamulo, kuti inu mukhale monga abwenzi anga mu masiku amene ine ndidali nawo, kuyenda kokalalikira uthenga wabwino mu mphamvu yanga;
78Â Pakuti sindidalore kuti iwo akhale ndi chikwama kapena thumba, ngakhale mayala awiri.
79Â Taonani, ndakutumizani inu kuti mukayese dziko, ndipo wogwira ntchito ndi woyenera kulandira malipiro ake.
80 Ndipo munthu aliyense amene adzapita ndi kukalalikira uthenga wabwino uwu wa ufumu, ndi wosalephera kupitiriza kukhulupirika mu zinthu zonse, sadzatopa mu maganizo, kapena kudetsedwa, kapena mu nthupi, mchiwalo, kapena mmafupa; ndipo tsitsi la m’mutu mwake silidzathothokera pansi osadziwika, Ndipo iwo sadzapita ndi njara, kapena ludzu.
81Â Kotero musadere nkhawa kuti mawa, tidzadya chiyani kapena tidzamwa chiyani, kapena, tidzavala chiyani.
82 Pakuti, talingalirani maluwa akuthengo, m’mene iwo amakulira, iwo sagwira ntchito, kapena kupota; ndipo maufumu a dziko lapansi, mu ulemelero wawo wonse, sadavalepo zokongola zofanana ndi limodzi mwa awa?
83Â Pakuti Atate anu, amene ali kumwamba, akudziwa kuti mukusowekera zinthu zonsezi.
84Â Kotero, lolani mawa lidzidera nkhawa za zinthu za ilo lokha.
85 Kapena musadere nkhawa musadapite zimene mudzakanene; koma sungani m’malingaliro anu mawu a moyo mosalekeza, ndipo chidzapatsidwa kwa inu mu nthawi yomweyo gawo limene lidzakhala loyenera kwa munthu aliyense.
86Â Kotero, musalore munthu pakati panu, pakuti lamulo ili ndi la onse okhulupirika amene aitanidwa ndi Mulungu mu mpingo ku utumiki, kuyambira ola lino musatenge chikwama kapena thumba, amene mukupita kukalengeza uthenga wabwino uwu wa ufumu.
87Â Taonani, ndakutumizani kuti mukadzudzule dziko zantchito zawo zonse zosalungama, ndi kuwaphunzitsa iwo za chiweruzo chimene chilinkudza.
88 Ndipo aliyense okulandirani inu, kumeneko inenso ndidzakhalako, pakuti ndidzapita pamaso panu. Ndidzakhala ku manja kwanu ndi kumanzere kwanu, ndipo Mzimu wanga udzakhala m’mitima yanu, ndipo angelo anga adzakuzingani, ndikukunyamulani.
89Â Aliyense okulandirani inu walandira ine; ndipo yemweyo adzakudyetsani inu, ndi kukuvekani, ndikukupatsani ndalama.
90Â Ndipo iye amene akudyetsani inu, kapena kukuvekani inu, kapena kukupatsani ndalama, sadzataya mphotho yake konse.
91Â Ndipo iye amene sachita zinthu izi si wophunzira wanga; mwa ichi mungathe kudziwa ophunzira anga.
92Â Iye amene sakulandirani inu, muchokereni mwanokha, ndi kutsuka mapazi anu ngakhale ndi madzi, madzi oyera, kaya kotentha kapena kozizira, ndipo chitirani umboni wa izo kwa Atate anu amene ali kumwamba, ndipo musabwelerenso kwa munthu ameneyo.
93 Ndipo m’mudzi wina uliwonse kapena mzinda omwe mwalowa, chitani chimodzimodzi.
94Â Komabe, funafunani mwakhama ndipo osasiya; ndipo tsoka kwa nyumba imeneyo, kapena mudziwo kapena mzinda umene wakukanani inu, kapena mawu anu, kapena umboni wokhudzana ndi ine.
95Â Tsoka, ndikunenanso, kwa nyumba imeneyo, kapena mudziwo kapena mzinda umene wakukanani inu, kapena mawu anu, kapena umboni wa ine;
96Â Pakuti, ine, Wamphamvu zonse, ndaika manja anga pa maiko, kuwalanga iwo chifukwa cha kuipa kwawo.
97 Ndipo milili idzatsogola, ndipo iwo sadzatengedwa kuchotsedwa ku dziko lapansi kufikira ine nditamaliza ntchito yanga, imene idzafupikitsidwa mu chilungamo—
98 Kufikira onse atandidziwa, amene atsalira, ngakhale kuyambira kwa wamng’ono mpaka wamkulu, ndipo adzadzadzidwa ndi chidziwitso cha Ambuye, ndipo adzaona maso ndi maso, ndipo adzakweza mawu awo, ndi mawu pamodzi kuimba nyimbo iyi yatsopano, nati:
99Â Ambuye wabweretsanso Ziyoni;Ambuye wawombola anthu ake, Israeli.Molingana ndi chisankho cha chisomo,Chimene chidabwera mwa chikhulupiliro.Ndi pangano la makolo awo.
100Â Ambuye wawombola anthu ake;Ndipo Satana wamangidwa ndipo nthawi kulibenso.Ambuye wasonkhanitsa zinthu zonse mu chimodzi.Ambuye watsitsa Ziyoni kuchokera kumwamba.Ambuye wakweza Ziyoni kuchokera pansi.
101Â Dziko lamva zowawa ndipo labweretsa mphamvu yake;Ndipo choonadi chakhazikitsidwa mu matumbo ake;Ndipo kumwamba kwalisekelera;Ndipo lavekedwa ndi ulemelero wa Mulungu wake;Pakuti iye waima pakati pa anthu ake.
102Â Ulemelero, ndi ulemu, ndi mphamvu, ndi nyonga,Zikhale kwa Mulungu wathu; pakuti iye ndi wodzadza ndi chifundo,Chilungamo, chisomo ndi choona, ndi mtendere,Kunthawi za nthawi, Ameni.
103Â Ndiponso, indetu, indetu, ndinena kwa inu, ndikofunikira kuti munthu aliyense amene apite kukalengeza uthenga wanga wabwino wosatha, kuti ngati iwo ali ndi mabanja, ndipo alandira ndalama mwa mphatso, kuti azitumize kwa iwo kapena kuzigwiritsa ntchito pa zowapindulira, monga Ambuye awatsogozera iwo, pakuti ndi momwe ndafunira.
104Â Ndipo lolani iwo amene alibe mabanja, amene alandira ndalama, azitumize kwa bishopu ku Ziyoni, kapena kwa bishopu ku Ohio, kuti zikathe kupatulidwa kuti zikabweretse mavumbulutso ndi zosindikiza zake, ndi kukhazikitsira Ziyoni.
105Â Ndipo ngati munthu aliyense adzapereka kwa inu mayala, kapena suti, tengani yakaleyo ndi kuponyera osauka, ndipo pitani njira yanu mokondwera.
106Â Ndipo ngati munthu wina pakati panu ali ndi mphamvu mu Mzimu, mloleni atengeko iye amene ali ofooka, kuti iye alimbikitsidwe mu chifatso chonse, kuti akathe kukhalanso wamphamvu.
107 Kotero, tenganani ndi iwo amene ali odzodzedwa kwa unsembe waung’ono, ndi kuwatumiza patsogolo panu kuti akapange dongosolo lokumana, ndi kukonzera njira, ndi kukhala pamene inu simunakwanitse kufika.
108Â Taonani, iyi ndi njira imene atumwi anga, mu masiku akale, adamangira mpingo wanga kwa ine.
109Â Kotero, lolani munthu aliyense aime mu udindo wake, ndi kugwira ntchito mu maitanidwe ake; ndipo musalole mutu unene kwa mapazi kuti siwofunikira mapaziwo; pakuti popanda mapazi thupi lidzakwanitsa bwanji kuima?
110Â Ndiponso thupi likufunikira chiwalo chilichonse, kuti zonse zilimbikitsidwe pamodzi, kuti dongosolo likhale la mngwiro.
111 Ndipo taonani, ansembe aakulu apite, ndiponso akulu, ndiponso ansembe aang’ono; koma madikoni ndi aphunzitsi asankhidwe kuyang’anira pa mpingo, kukhala atumiki oimilira pa mpingo.
112 Ndipo bishopu, Newel K. Whitney, nayenso apite mozungulira ndi pakati pa mipingo yonse, kufunafuna osauka kuti atumikire ku zosowa zawo potsitsa olemera ndi onyada.
113Â Iye alembenso mtumiki wotsogolera ndi kuchita malonda ake ena monga iye adzanenere.
114 Komabe, lolani bishopu apite ku mzinda wa New York, apitenso ku mzinda wa Albany, ndipo apitenso ku mzinda wa Boston, ndi kuchenjeza anthu a m’mizinda imeneyo ndi phokoso la uthenga wabwino, ndi mawu amfuu, za chipululutso ndi kuthetseratu chimene chikuwayembekezera ngati iwo angakane zinthu zimenezi.
115Â Pakuti ngati iwo akana zinthu zimenezi ola la chiweruzo chawo ili pafupi, ndipo nyumba zawo zidzasiidwa kukhala bwinja.
116 Muloleni iye andikhulupilire ine, ndipo sadzachita manyazi; ndipo tsitsi la m’mutu mwake silidzagwa pansi osadziwa.
117Â Ndipo indetu ndikunena kwa inu, atumiki anga otsalanu, pitani momwe nyengo zanu zingakuloleni, mu maitanidwe anu osiyanasiyana, ku mizinda yaikulu ndi yodziwika ndi midzi, kudzudzula dziko mu chilungamo za kusalungama kwawo konse ndi ntchito zoipa, kuwaunikira bwino ndi momveka bwino za chipululutso cha zonyansa mu masiku omaliza.
118 Pakuti, ndi inu atero Ambuye Wamphamvu zonse, ndidzang’amba maufumu awo; sindidzangogwedeza dziko lapansi lokha, komanso thambo lodzaza ndi nyenyezi lidzagwedezeka.
119Â Pakuti ine, Ambuye, ndatambasula dzanja langa kupereka mphamvu za kumwamba; simungalione tsopano, koma kanthawi kochepa ndipo mudzaliona, ndi kudziwa kuti ine ndine, ndipo kuti ndidzabwera ndi kulamulira ndi anthu anga.
120Â Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza. Ameni.