Gawo 28
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Oliver Cowdery, ku Fayette, New York, Seputembara 1830. Hiram Page, membala wa Mpingo, adali ndi mwala wina ndipo adanena kuti akulandira mavumbulutso ndi chithandizo chake okhudzana ndi kumangidwa kwa Ziyoni ndi dongosolo la Mpingo. Mamembala angapo adanyengedwa ndi zonena izi, ndipo ngakhale Oliver Cowdery adanamizidwa mzimenezo. Kutangotsala pang’ono msonkhano waukulu kuchitika, Mneneri adafunsa moona mtima kwa Ambuye pa nkhaniyo, ndipo vumbulutsoli lidatsatira.
1–7, Joseph Smith ali ndi mafungulo a zinsinsi, ndipo iye yekhayo amalandira mavumbulutso a Mpingo; 8–10, Oliver Cowdery akuyenera kulalikira kwa Alamani; 11–16, Satana adanyenga Hiram Page ndipo adamupatsa iye mavumbulutso abodza.
1 Taona, ndikunena kwa iwe, Oliver, kuti kudzapatsidwa kwa iwe kuti udzamvedwa ndi mpingo muzinthu zonse zomwe udzawaphunzitse ndi Mtonthozi, zokhudzana ndi mavumbulutso ndi malamulo amene ndapereka.
2 Koma, taona, indetu, indetu, ndinena kwa iwe, palibe amene adzasankhidwe kulandira malamulo ndi mavumbulutso mu mpingo uno kupatula mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., pakuti amawalandira iwo ngakhale monga Mose.
3 Ndipo udzakhala womvera ku zinthu zimene ndidzapereka kwa iye, ngakhale monga Aroni, kulengeza mokhulupirika malamulo ndi mavumbulutso, ndi mphamvu ndi ulamuliro kwa mpingo.
4 Ndipo ngati iwe utsogozedwa ndi Mtonthozi pa nthawi iliyonse poyankhula kapena kuphunzitsa, kapena nthawi zonse mwa lamulo kwa mpingo, ukhonza kuchita.
5 Koma iwe sudzalemba mwa lamulo, koma mwa nzeru;
6 Ndipo iwe sudzamulamula iye amene ali pamutu wako, ndi pamutu wa Mpingo;
7 Pakuti ine ndampatsa iye mafungulo a zinsinsi, ndi mavumbulutso amene asindikizidwa, mpaka ine ndidzaike kwa iwo wina m’malo mwake.
8 Ndipo tsopano, taona, ndikunena kwa iwe kuti udzapita kwa Alamani ndi kukalalikira uthenga wanga kwa iwo; ndipo pamene iwo adzalandira ziphunzitso zako udzapangitsa mpingo wanga kukhazikika pakati pawo; ndipo udzakhala ndi mavumbulutso, koma usadzawalembe monga mwa lamulo.
9 Ndipo tsopano, taona, ndinena kwa iwe kuti sikudaululidwe, ndipo palibe munthu akudziwa kumene mzinda wa Ziyoni udzamangidwa, koma kudzaperekedwa pambuyo pake. Taona, ndikunena kwa iwe kuti kudzakhala pa malire ndi Alamani.
10 Usachoke pamalo ano kufikira pambuyo pa msonkhano waukulu; ndipo mtumiki wanga Joseph adzasankhidwa kuti atsogolere msonkhano waukuluwu ndi mawu ake, ndipo chimene iye adzanene kwa iwe udzanena.
11 Ndiponso, udzatenga mbale wako, Hiram Page, pakati pa iye ndi iwe wekha, ndi kumuuza iye kuti zimene adalemba pa mwala umenewo sizili za ine, ndipo kuti Satana amunyenga iye;
12 Pakuti, taonani, zinthu izi sizidaikidwe kwa iye, ngakhale chilichonse sichidzaikidwa kwa aliyense wa mpingo uwu motsutsana ndi mapangano a mpingo.
13 Pakuti zinthu zonse zikuyenera kuchitidwa mwadongosolo, ndi kuvomereza kwa onse mu mpingo, mwa pemphero la chikhulupiliro.
14 Ndipo iwe udzathandiza kuthetsa zinthu zonsezi, molingana ndi mapangano a mpingo, usadayambe ulendo wako pakati pa Alamani.
15 Ndipo kudzapatsidwa kwa iwe kuyambira nthawi yomwe utadzapite, kufikira nthawi yodzabwelera, chimene utadzachite.
16 Ndipo ukuyenera kutsegula pakamwa pako nthawi zonse, kulengeza uthenga wanga ndi mawu a chisangalalo. Ameni.