Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 67


Gawo 67

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, kumayambiliro kwa Novembala 1831. Chochitika chake chidali chokuti msonkhano wapedera, ndi kutsindikizidwa kwa mavumbulutso olandiridwa kale kuchokera kwa Ambuye kudzera mwa Mneneri adaganiziridwapo ndi kuchitidwapo (onani mutu wa gawo 1). William W. Phelps adali atangokhazikitsa kumene malo a Mpingo otsindikizira mu Independence, Missouri. Msonkhanowo udaganiza zotsindikiza mavumbulutsowo mu Book of Commandments ndi kutsindikiza makope 10,000 (amene pambuyo pake chifukwa cha zovuta zosayembekezereka adachepetsedwa kufika pa makope 3,000). Ambiri mwa abale adachitira umboni wotsimikiza kuti mavumbulutso amene adaphatikizidwa kuti atsindikizidwe adali oona ndithu, monga zidachitidwira umboni ndi Mzimu Woyera wotsanulidwa pa iwo. Mbiri ya Joseph Smith imalemba kuti potsatira vumbulutso lodziwika kuti gawo 1 litalandiridwa, zokambirana zina zidakhalapo zokhudzana ndi chiyankhulo chomwe chidagwiritsidwa ntchito mu mavumbulutsowo. Vumbulutsoli lapano lidatsatira.

1–3, Ambuye amamva mapemphero ndi kuyang’anira akulu Ake; 4–9, Iye amaitana munthu wanzeru koposa kuti abwerenze mocheperako mwa mavumbulutso Ake; 10–14, Akulu okhulupirika adzakwatulidwa ndi Mzimu ndi kuona nkhope ya Mulungu.

1 Taonani, ndipo mvetserani, O inu akulu ampingo wanga, amene mwadzisonkhanitsa nokha pamodzi, amene mapemphero anu ndawamva, amene mitima yanu ndikuidziwa, ndipo amene zokhumba zanu zafika pamaso panga.

2 Taonani ndipo onani, maso anga ali pa inu, ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwanga ndipo chuma cha muyaya ndichaine kuchipereka.

3 Inu mwayesetsa kukhulupilira kuti mukathe kulandira madalitso amene adaperekedwa kwa inu; koma taonani, indetu ndikunena kwa inu mudali mantha mu mitima yanu, ndipo indetu ichi ndi chifukwa chomwe inu simudalandire.

4 Ndipo tsopano ine, Ambuye, ndikupereka kwa inu umboni wa choonadi cha malamulo awa amene ayalidwa pamaso panu.

5 Maso anu akhala pa mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndipo chiyankhulo chake mwachidziwa, ndipo zofooka zake mwazidziwa; ndipo inu mwafuna mu mitima yanu chidziwitso choti muthe kuonetsa kuposera chiyankhulo chake; izi mukuzidziwanso.

6 Tsopano, funafunani kuchokera mu Buku la Malamulo, ngakhale wamn’gono pakati pawo, ndipo mumusankhe iye amene ali wanzeru kwambiri pakati panu;

7 Kapena, ngati pali wina pakati panu amene angapange limodzi lofanana nalo, pamenepo inu mwalungamitsidwa pakunena kuti inu simukudziwa kuti ndi oona;

8 Koma ngati simungapange lina lofanana nalo, muli pansi pa chidzudzulo ngati simuchitira umboni kuti ndi oona

9 Pakuti inu mukudziwa kuti palibe kusalungama mwa iwo, ndipo chimene chili cholungama chimabwera kuchokera kumwamba, kuchokera kwa Atate wa kuwala.

10 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, kuti ndi mwayi wanu, ndipo lonjezo ndikupereka kwa inu amene mwadzodzedwa ku utumiki uwu, kuti pamene inu mudzichotsera nokha ku nsanje ndi mantha, ndi kudzichepetsa nokha pamaso panga, pakuti inu sumuli odzichepetsa mokwanira, chinsalu chophimba chidzang’ambidwa ndipo inu mudzandiona ine, ndi kudziwa kuti ine ndine—osati ndi maganizo a thupi, kapena a chibadwidwe, koma ndi mzimu.

11 Pakuti palibe munthu adaona Mulungu pa nthawi iliyonse mu thupi, kupatula atakwatulidwa ndi Mzimu wa Ambuye.

12 Ngakhalenso munthu aliyense wachilengedwe sangakhale pamaso pa Mulungu, kapena kutsatira lingaliro la chithupithupi.

13 Inu simungathe kukhala pamaso pa Mulungu tsopano, ngakhale angelo otumikira; kotero, pitilizani mu chipiliro kufikira mutalungamitsidwa.

14 Musalore malingaliro anu abwelere m’mbuyo; ndipo pamene muli oyenera, mu nthawi yanga yoikika, mudzaona ndi kudziwa icho chimene chidaperekedwa pa inu kudzera mu manja a mtumiki wanga Joseph Smith. Jun. Ameni.