Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 54


Gawo 54

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Newel Knight, ku Kirtland, Ohio, Juni 10, 1831. Mamembala a Mpingo okhala ku Thompson, Ohio, adali ogawanikana pa mafunso okhudzana ndi kupatulidwa kwa katundu. Kudzikonda ndi umbombo kudaonekera. Kutsatira utumiki wake kwa a Shakers (onani mutu wa gawo 49), Leman Copley adaphwanya pangano lake kuti apatule munda wake waukulu ngati malo a cholowa cha Oyera Mtima ofika kuchokera ku Colesville, New York. Ngati zotsatira, Newek Knight (mtsogoleri wa mamembala okhala ku Thompson) ndi akulu ena adabwera kwa Mneneri kufunsa m’mene angapitile chitsogolo. Mneneri adafunsa kwa Ambuye, ndipo adalandira vumbulutso ili, limene likulamula mamembala ku Thompson kuti achoke ku munda wa Leman Copley ndi kupita ku Missouri.

1–6, Oyera Mtima akuyenera kusunga pangano la uthenga wabwino kuti akalandire chisomo; 7–10, Iwo akuyenera kupilira mu m’masautso.

1 Taonani, akutero Ambuye, ngakhale Alefa ndi Omega, oyamba ndi otsiriza, ngakhale iye amene adapachikidwa chifukwa cha machimo adziko—

2 Taona, indetu, indetu, ndinena kwa iwe, mtumiki wanga Newel Knight, iwe udzaima nji mu udindo umene ine ndakusankhira iwe.

3 Ndipo ngati abale ako akufuna kuthawa adani awo, alole iwo alape machimo awo wonse, ndi kukhala wodzichipetsa moona pamaso panga ndi wolapa.

4 Ndipo ngati pangano limene iwo adapanga kwa ine laphwanyidwa, ngakhale choncho lakhala lopanda kanthu komanso lilibe mphamvu.

5 Ndipo tsoka kwa iye amene chokhumudwitsa ichi chingadze, pakuti kukadakhala kwabwino kwa iye kuti adamizidwa mkuya kwa nyanja.

6 Koma odala ndi iwo amene asunga pangano ndi kusunga malamulo, pakuti adzapeza chifundo.

7 Kotero, pitani tsopano ndi kuthawa dzikoli, kuopa kuti adani anu abwera pa inu; ndipo yambani ulendo wanu, ndipo sankhani amene mukufuna adzakhale mtsogoleri wanu, ndi kukulipilirani ndalama

8 Ndipo motero mudzayamba ulendo wanu ku madera amadzulo, ku dziko la Missouri, ku malire a Alamani.

9 Ndipo mukatha ulendowo, taonani, ndikunena kwa inu, funafunani kukhala monga kwa anthu, kufikira nditakukonzerani malo anu.

10 Ndiponso, khalani opilira mu masautso kufikira nditabwera; ndipo, taonani, ndikudza msanga, ndipo mphotho yanga ili ndi ine, ndipo iwo amene andifunafuna ine molawira adzapeza mpumulo ku miyoyo yawo. Ngakhale choncho. Ameni.