Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 61


Gawo 61

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, m’mphepete mwa Mtsinje wa Missouri, McIlwaine’s Bend, Ogasiti 12, 1831. Pa ulendo wawo wobwelera ku Kirtland, Mneneri ndi akulu khumi adali atayenda kumusi kwa Mtsinje wa Missouri mu mabwato. Pa tsiku lachitatu la ulendowo, adakumana ndi zowopsya zambiri. Mkulu William W. Phelps, m’masomphenya a usana, adaona wowonongayo akukwera mu mphamvu pamadzi.

1–12, Ambuye walamulira chiwonongeko chambiri pamadzi; 13–22, Madzi adatembeleredwa ndi Yohane, ndipo wowonongayo akukwera pa nkhope zawo; 23–29, Ena ali ndi mphamvu yakulamulira madzi; 30–35, Akulu akuyenera kuyenda awiriawiri ndi kukalalikira uthenga wabwino; 36–39, Iwo akuyenera kukonzekera kudza kwa Mwana wa Munthu.

1 Taonani, ndipo mvetserani ku mawu a iye amene ali ndi mphamvu zonse, amene ali kuchokera kunthawi zosatha mpaka kunthawi zosatha, ngakhale Alefa ndi Omega, oyamba ndi otsiriza.

2 Taonani, indetu, akutero Ambuye kwa inu, O inu akulu a mpingo wanga, amene mwasonkhana pamalo ano, amene machimo tsopano akhululukidwa kwa inu, pakuti ine, Ambuye, ndimakhululukira machimo, ndipo ndine wachifundo kwa iwo amene amavomereza machimo awo ndi mitima yodzichepetsa;

3 Koma indetu ndinena kwa inu, kuti sikuli koyenera kuti gulu lonse ili la akulu anga ayende mofulumira pa madzi, pamene okhala ku mbali zonsezo akuwonongeka mu kusakhulupilira.

4 Komabe, ndidalolera kuti muchitire umboni; taonani, pali zoopsa zambiri pamadzi, ndipo makamaka pambuyo pake;

5 Pakuti ine, Ambuye, ndalamulira mu mkwiyo wanga ziwonongeko zambiri pa madzi; inde, ndipo makamaka pa madzi awa.

6 Komabe, zamoyo zonse zili m’dzanja langa, ndipo iye amene ali wokhulupirika mwa inu sadzawonongeka ndi madzi.

7 Kotero, ndi koyenera kuti mtumiki wanga Sidney Gilbert ndi mtumiki wanga William W. Phelps akhale mwachangu pa mayendedwe ndi ntchito yawo.

8 Komabe, sindidzalola kuti inu mulekane mpaka inu mutalangidwa chifukwa cha machimo anu onse, kuti mukakhale amodzi, kuti musakathe kuwonongeka mu zoipa;

9 Koma tsopano, indetu ndinena, kukuyenera kwa ine kuti mulekane. Kotero lolani atumiki anga Sidney Gilbert ndi William W. Phelps atenge gulu lawo lakale, ndipo asiyeni ayende ulendo wawo mwachangu kuti akakwaniritse ntchito yawo, ndipo kudzera mwa chikhulupiliro adzagonjetsa;

10 Ndipo pamene iwo ali okhulupirika adzatetezedwa, ndipo ine, Ambuye, ndidzakhala nawo.

11 Ndipo otsalawo atenge zomwe zili zofunika pa zovala.

12 Lolani mtumiki wanga Sidney Gilbert atenge zomwe zili zosafunikira ndi iye, monga inu mungavomereze.

13 Ndipo tsopano, taonani, chifukwa cha ubwino wanu ndidapereka kwa inu lamulo la zinthu izi; ndipo ine, Ambuye, ndidzakambilana ndi inu monga ndi anthu m’masiku akale.

14 Taonani, ine, Ambuye, poyamba ndidadalitsa madzi; koma m’masiku otsiriza, kudzera pakamwa pa mtumiki wanga Yohane, ndidatembelera madzi.

15 Kotero, masiku adzafika pamene palibe nyama idzakhale yotetezeka pamadzi.

16 Ndipo kudzanenedwa m’masiku akudzawo kuti palibe angathe kukwera ku dziko la Ziyoni pamadzi, koma iye amene ali woongoka mtima.

17 Ndipo, monga ine, Ambuye, pa chiyambi ndidatembelera dzikolo, ngakhale chomwecho mu masiku otsiriza ndidalidalitsa ilo, mu nthawi yake, chifukwa cha kugwiritsa ntchito kwa oyera mtima anga, kuti akathe kudya zonona zake.

18 Ndipo tsopano ndikukupatsani inu lamulo kuti chimene ine ndinena kwa m’modzi ndinena kwa onse, kuti inu mudzachenjezeratu abale anu zokhudzana ndi madzi awa, kuti iwo asabwere mu ulendo pa iwo, kuopa kuti chikhulupiliro chawo chidzalephera ndipo iwo adzakodwa m’misampha;

19 Ine, Ambuye ndalamula, ndipo owononga akwera pankhope pake, ndipo sindibwenza lamulolo.

20 Ine, Ambuye, ndidakwiya nanu dzulo, koma lero mkwiyo wanga wabwelera.

21 Kotero, lolani awo ponena za amene ndayankhula, kuti atenge ulendo wawo mofulumira—komanso ndinena kwa inu, asiyeni iwo atenge ulendo wawo mwa changu.

22 Ndipo kulibe kanthu kwa ine, pakapita kamphindi, ngati atatsiriza ntchito yawo, kaya ayenda pamadzi kapena pamtunda; izi zikhale monga zidzadziwike kwa iwo molingana ndi ziweruzo zawo pambuyo pake.

23 Ndipo tsopano, zokhudzana ndi atumiki anga, Sidney Rigdon, Joseph Smith, Jun., ndi Oliver Cowdery, aloleni iwo asabwerenso pamadzi, koma pa ngalande, pamene akuyenda ku nyumba zawo; kapena mwa kuyankhula kwina iwo sadzabwera pa madzi kuti ayende, koma pa ngalande.

24 Taonani, ine, Ambuye, ndakonzera njira ya ulendo wa oyera mtima anga; ndipo taonani, iyi nde njirayo—kuti atachoka ngalandeyo adzayenda pa nthaka, pamene iwo akulamulidwa kuyenda ndi kupita ku dziko la Ziyoni;

25 Ndipo adzachite monga ana a Israeli, akukhoma mahema awo munjira.

26 Ndipo, taonani, lamulo ili mudzapereka kwa abale anu onse.

27 Komabe, kwa amene kwapatsidwa mphamvu yakulamula madziwo, kwa iye kwapatsidwa ndi Mzimu kudziwa njira zake zonse;

28 Kotero, mloleni achite monga momwe Mzimu wa Mulungu wamoyo udamulamulira, kaya pamtunda kapena pamadzi, monga zakhala ndi ine kuchita pambuyo pake.

29 Ndipo kwa inu kwapatsidwa njira ya oyera mtima, kapena njira ya oyera mtima a msasa wa Ambuye, kuti ayende.

30 Ndiponso, inde ndinena kwa inu, atumiki anga, Sidney Rigdon, Joseph Smith, Jun., ndi Oliver Cowdery, sadzatsegula pakamwa pawo m’misonkhano ya oipa kufikira iwo atafika ku Cincinnati;

31 Ndipo m’malo amenewo iwo adzakwezera mawu awo kwa Mulungu motsutsana ndi anthu amenewo, inde, kwa iye amene mkwiyo wake wayatsidwa motsutsana ndi kuipa kwawo, anthu amene ali pafupi kucha kuti awonongedwe.

32 Ndipo kuchokera kumeneko aloleni iwo apite ku misonkhano ya abale awo, pakuti ntchito zawo ngakhale tsopano zikufunika mochuluka pakati pawo kuposa pakati pa misonkhano ya oipa.

33 Ndipo tsopano, zokhudzana ndi otsala, aloleni iwo ayende ndi kulengeza mawu pakati pa misonkhano ya oipa, monga momwe kwaperekedwera;

34 Ndipo pamene iwo adzachita izi iwo adzachotsa zovala zawo, ndipo iwo adzakhala opanda banga pamaso panga.

35 Ndipo aloleni iwo ayende pamodzi, kapena awiri-awiri, monga momwe iwo akufunira, koma mtumiki wanga Reynolds Cahoon, ndi mtumiki wanga Samuel H. Smith, amene ndimakondwera nawo, asasiyanitsidwe mpaka atabwelera kwawo, ndipo izi ndi cholinga chanzeru mwa ine.

36 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu, ndipo chimene ndinena kwa m’modzi ndinena kwa onse, khalani okondwa, ti ana tating’ono; pakuti ine ndili pakati panu, ndipo sindidakusiyeni inu;

37 Ndipo pamene mwadzichepetsa nokha pamaso panga, madalitso a ufumu ndi anu.

38 Mangani lamba m’chiuno mwanu, ndipo khalani atcheru, ndipo khalani ochangamuka, kuyang’anira kudza kwa Mwana wa munthu, pakuti adzabwera mu ola limene simukuliganizira.

39 Pempherani nthawi zonse kuti mungalowe m’mayesero, kuti mukathe kuyimabe pa tsiku la kudza kwake, kaya m’moyo kapena mu imfa. Ngakhale zili choncho. Ameni.