Gawo 63
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Ogasiti 30, 1831. Mneneri, Sidney Rigdon, ndi Oliver Cowdery adafika mu Kirtland pa Ogasiti 27 kuchokera ku ulendo wawo ku Missouri. Mbiri ya Joseph Smith ikufotokozera vumbulutso ili: “Mu masiku aubwana wa Mpingo, kudali nkhawa yaikulu kupeza mawu a Ambuye pa nkhani iliyonse imene munjira ina imakhudza za chipulumutso chathu; ndipo pamene dziko la Ziyoni lidali tsopano nkhani yofunikira kwambiri ya chinthu chowonekera kuthupi, ndidafunsa kwa Ambuye pa uthenga wapadera pa kusonkhana kwa Oyera Mtima, ndi kugula kwa malo, ndi nkhani zina.”
1–6, Tsiku la mkwiyo lidzafika pa woipa; 7–12, Zizindikilo zimabwera ndi chikhulupiliro; 13–19, Achigololo mumtima adzakana chikhulupiliro ndipo adzaponyedwa mu nyanja ya moto; 20, Okhulupirika adzalandira cholowa pa dziko lapansi losandulika; 21, Nkhani yonse ya zochitika pa Phiri la kusandulika siinavumbulutsidwebe; 22–23, Omvera amalandira zinsisi za ufumu; 24–31, Cholowa cha mu Ziyoni chikuyenera kugulidwa; 32–35, Ambuye alengeza nkhondo, ndipo oipa apha oipa; 36–48, Oyera Mtima akuyenera kusonkhana ku Ziyoni ndi kupereka ndalama zomumangira; 49–54, Madalitso atsimikiziridwa kwa okhulupirika pa Kubwera Kwachiwiri, mu chiukitso, ndi munthawi ya Zakachikwi; 55–58Ili ndi tsiku la chenjezo; 59–66, Dzina la Ambuye limatengedwa pachabe ndi iwo amene amaligwiritsa popanda ulamuliro.
1 Mvetserani, O inu anthu, ndi kutsegula mitima yanu ndi kutchera khutu kuchokera patali, ndipo mverani, inu amene mumadzitcha nokha anthu a Ambuye, ndipo mverani mawu a Ambuye ndi chifuniro chake chokhudzana ndi inu.
2 Inde, indetu, ndikunena, mverani mawu a iye amene mkwiyo wake wayaka motsutsana ndi woipa komanso wapandukila;
3 Amene amafuna kutenga ngakhale iwo amene angafune kuwatenga, ndipo amasunga mu moyo iwo amene angafune kuwasunga;
4 Amene amamanga pa chifuniro ndi kukondweretsedwa kwake; ndipo amawononga m’mene wakondera, ndipo ndi wokutha kuponya moyo ku gahena.
5 Taonani, ine, Ambuye, ndayankhula mawu anga, ndipo adzamveredwa.
6 Kotero, indetu ndikunena, lolani oipayo asamale, ndipo lolani wopandukirawo achite mantha ndi kunjenjemera; ndipo lolani wosakhulupilira agwire milomo yawo, pakuti tsiku la mkwiyo lidzafika pa iwo ngati kamvuluvulu, ndipo anthu onse azadziwa kuti ndine Mulungu wawo.
7 Ndipo iye amene afunafuna zizindikiro adzaona zizindikiro, koma osati za kuchipulumutso.
8 Indetu, ndikunena kwa inu, pali ena pakati panu amene akufuna zizindikiro, ndipo akhalapo oterowo ngakhale kuchokera pachiyambi;
9 Koma, taonani, chikhulupiliro sichimabwera mwa zizindikiro, koma zizindikiro zimatsatira iwo amene akhulupilira.
10 Inde, zizindikiro zimadza mwa chikhulupiliro, osati mwa chifuniro cha anthu, kapena momwe iwo akondera, koma kudzera mu chifuniro cha Mulungu.
11 Inde, zizindikiro zimadza mwa chikhulupiliro, kwa ntchito zamphamvu, pakuti popanda chikhulupiliro palibe munthu angakondweretse Mulungu; ndipo yemwe Mulungu wakwiya naye, iye sakondwera naye; kotero, kwa oterowo iye saonetsa zizindikiro, mkwiyo wokha ku chiweruzo chawo.
12 Kotero, ine, Ambuye, sindikondwera ndi iwo pakati panu amene amafunitsitsa zizindikiro ndi zodabwitsa pa chikhulupiliro, koma osati pa ubwino wa anthu ku ulemelero wanga.
13 Komabe, ndimapereka malamulo, ndipo ambiri atembenukira kumbali kwa malamulo anga ndipo sadawasunge.
14 Adalipo pakati panu achigololo; ena mwa iwo atembenukira kumbali kwanu, ndipo ena atsalira ndi inu amene pambuyo pake adzaululidwa.
15 Lolani oterowo achenjere ndi kulapa mwachangu, kuopa chiweruzo chidzabwera pa iwo ngati msampha, ndi zonyansa zawo zidzaonetsedwa, ndi ntchito zawo zidzawatsatira m’maso mwa anthu.
16 Ndipo indetu ndikunena kwa inu, monga ndidanena kale, iye amene ayang’ana kwa mzimayi ndi kumusilira, kapena ngati wina adzachita chigololo m’mitima mwawo, sadzakhala ndi Mzimu, koma adzakana chikhulupiliro ndipo adzaopa.
17 Kotero, ine, Ambuye, ndanena kuti amantha, ndi osakhulupilira, ndi onse abodza, ndi aliyense wokonda ndi kuchita bodza, ndi achigololo, ndi anyanga, adzakhala ndi gawo lawo mu nyanja imene amayaka ndi moto ndi sulufure, imene ndi imfa yachiwiri.
18 Indetu ndikunena, kuti iwo sadzakhala ndi gawo mu chiukitso choyamba.
19 Ndipo tsopano taonani, ine, Ambuye, ndikunena kwa inu kuti inu simunalungamitsidwe, chifukwa zinthu izi zili pakati panu.
20 Komabe, iye amene apilira mu chikhulupiliro ndi kuchita chifuniro changa, yemweyo adzapambana, ndipo adzalandira cholowa pa dziko lapansi pamene tsiku la kusandulika lidzafika;
21 Pamene dziko lapansi lidzasandulika, ngakhale molingana ndi njira imene idawonetseredwa kwa atumwi anga pa phiri; zimene chidzalo chake inu simudachilandirebe.
22 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa inu, kuti monga ndanena kuti ndidzadziwitsa chifuniro changa kwa inu, taonani ndidzachidziwitsa kwa inu, osati munjira ya lamulo, pakuti alipo ambiri amene sasunga malamulo anga.
23 Koma kwa iye amene amasunga malamulo anga ndidzampatsa zinsisi za ufumu wanga, ndipo omwewo adzakhala chitsime cha madzi amoyo, kutumphukira ku moyo wasatha.
24 Ndipo tsopano, taonani, ichi ndicho chifuniro cha Ambuye Mulungu wanu chokhudzana oyera mtima ake, kuti iwo akadzisonkhanitse wokha limodzi ku dziko la Ziyoni, osati mwachangu, kuopa kungakhale chisokonezo, chimene chimabweretsa mliri.
25 Taonani, dziko la Ziyoni—ine, Ambuye, ndalinyamula m’manja mwanga;
26 Komabe, ine, Ambuye, ndimapereka kwa Kaesara zinthu zimene zili za Kaesara.
27 Kotero, ine Ambuye ndikufuna kuti inu mugule malo, kuti mukakhale ndi mwayi ku dziko, kuti mukathe kukhala ndi chonena pa dziko, kuti iwo asakautsidwe ku mkwiyo.
28 Pakuti Satana amaika ichi mu mitima yawo kuti akwiye nanu, ndipo mpaka kukhetsa kwa mwazi.
29 Kotero, dziko la Ziyoni silidzatengedwa koma mwa kugula kapena mwa mwazi, kupanda apo kulibe cholowa chanu.
30 Ndipo ngati mwakugula, taonani ndinu odala;
31 Ndipo ngati mwa mwazi, monga inu mwaletsedwa kukhetsa mwazi, onani, adani anu ali pa inu, ndipo inu mudzakwapulidwa kuchokera ku mzinda ndi mzinda, ndipo kuchokera ku sunagoge ndi sunagoge, ndipo koma ochepa adzaima kukalandira cholowa chawo.
32 Ine, Ambuye, ndili wokwiya ndi oipawo; Ndaletsa Mzimu wanga kwa okhala pa dziko lapansi.
33 Ndalumbira mu mkwiyo wanga, ndipo ndalengeza nkhondo pamaso pa dziko lapansi, ndipo woipa adzapha woipa, ndipo mantha adzafika pa munthu aliyense;
34 Ndipo oyera mtima sadzatha kuthawa; komabe, ine, Ambuye, ndili nawo, ndipo ndidzatsika kuchoka kumwamba kuchokera pamaso pa Atate anga, ndi kuyatsa woipa ndi moto wosazimitsika.
35 Ndipo taonani, izi sizidachitikebe, koma pang’ono ndi pang’ono.
36 Kotero, poona kuti ine, Ambuye, ndalengeza zinthu zonsezi pamaso pa dziko lapansi, ndikufuna kuti oyera mtima anga asonkhane pa dziko la Ziyoni;
37 Ndipo kuti munthu aliyense atenge chilungamo mu manja ake ndi kukhulupirika mchiuno mwake, ndi kukweza liwu la chenjezezo kwa okhala mu dziko lapansi; ndi kulengeza ndi zonse mawu ndi kuthawa kuti chipululuko chidzabwera kwa woipa.
38 Kotero, lolani ophunzira anga mu Kirtland akonze nkhawa zawo zakuthupi, womwe akukhala pa munda uwu.
39 Mulekeni mtumiki wanga Titus Billings, amene akuyang’anirapo, agulitse malowo, kuti iye akadzikonzekeretse mu nyengo yamasika ikubwerayi kuyamba ulendo wake kupita ku dziko la Ziyoni, ndi iwo amene akukhala pa malopo, kupatula iwo amene ine ndidzawasunga kwa inemwini, amene sadzapita kufikira nditawalamula.
40 Ndipo lolani ndalama zonse zomwe zingathe kusungidwa, zilibe kanthu kwa ine kuti ndizochepa kapena zochuluka, zitumizidwe ku dziko la Ziyoni, kwa iwo amene ndawasankha kuti alandire.
41 Taonani, ine, Ambuye, ndidzapereka kwa mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., mphamvu kuti iye adzakwanitse kuzindikira mwa Mzimu iwo amene adzapita ku dziko la Ziyoni, ndi iwo mwa ophunzira anga amane adzatsale.
42 Mulekeni mtumiki wanga Newel K. Whitney akhale ndi sitolo yake, kapena mu mawu ena, sitoloyo, kwa kanthawi kochepa.
43 Komabe, mulekeni iye agawe ndalama zonse zimene angathe kugawa, kuti zitumizidwe ku dziko la Ziyoni.
44 Taonani, zinthu izi zili m’manja mwake, muloleni achite molingana ndi nzeru zake.
45 Indetu ndikunena, mulekeni iye adzodzedwe ngati nthumwi kwa ophunzira amene adzatsalire, ndipo muloleni iye adzodzedwe ku mphamvu imeneyi;
46 Ndipo tsopano mwachangu yenderani mipingo, kufotokozera zinthu izi kwa iwo, ndi mtumiki wanga Oliver Cowdery. Taonani, ichi ndi chifuniro changa kupeza ndalama ngakhale momwe ine ndalangizira.
47 Iye amene ali okhulupirika ndi kupilira adzapambana dziko.
48 Iye amene atumiza chuma mu dziko la Ziyoni adzalandira cholowa mu dziko lino, ndipo ntchito zake zidzamutsatira, ndiponso mphotho mu dziko lilinkudza.
49 Inde, ndipo odala ndi okufa amene amafa mwa ambuye, kuchokera tsopanolino, pamene Ambuye adzabwera, ndipo zinthu zakale zidzatha, ndipo zinthu zonse zidzakhala zatsopano, iwo adzauka kwa akufa ndipo sadzafanso, ndipo adzalandira cholowa pamaso pa Ambuye, mu mzinda woyerawo.
50 Ndipo iye amene alimoyo pamene Ambuye adzabwera, ndipo wasunga chikhulupiliro, odala ndi iye; komabe, kwaikidwa kwa iye kufa pa dzaka za munthu.
51 Kotero, ana adzakula kufikira iwo atakalamba; okalamba adzafa; koma iwo sadzagona mu nthaka, koma adzasandulika mu kuphethira kwa diso.
52 Kotero, pachifukwa ichi adalalika atumwi kwa dziko lapansi chiukitso cha akufa.
53 Zinthu izi ndi zinthu zimene inu mukuyenera kuziyang’anira; ndi, kuziyankhura potsatira njira ya Ambuye, zayandikira tsopano, ndipo munthawi ikudza, ngakhale mu tsiku la kudza kwa Mwana wa Munthu.
54 Ndipo kufikira ola limenelo kudzakhala anamwali opusa pakati pa anzeru; ndipo pa ola limenelo kudzabwera kusiyanitsa konse kwa olungama ndi oipa; ndipo mu tsiku limenelo ndidzatumiza angelo anga kuchotsa oipa ndi kuwaponya iwo mu moto wosazimitsika.
55 Ndipo tsopano taonani, indetu ndikunena kwa inu, ine, Ambuye, sindikukondwera ndi mtumiki wanga Sidney Rigdon; iye adadzikweza yekha mumtima mwake, ndipo sadalandire uphungu, koma adamvetsa chisoni Mzimu;
56 Kotero zolemba zake ndizosavomelezeka kwa Ambuye, ndipo iye adzalemba zina; ndipo ngati Ambuye sazilandira, taonani iye sadzaimanso mu udindo umene ine ndidamuikiza iye.
57 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, iwo amene akufuna m’mitima yawo, mofatsa, kuti achenjeze ochimwa ku kulapa, aloleni iwo adzodzedwe ku mphamvu imeneyi.
58 Pakuti ili ndi tsiku la chenjezo, ndipo osati tsiku la mawu ochuluka. Pakuti ine, Ambuye, sindidzanyozedwa mu masiku omaliza.
59 Taonani, ndine wochokera kumwamba, ndipo mphamvu yanga ili pansi. Ndili ponsoponse, ndi mu zonse, ndi mwa zonse, ndipo ndimafufuza zonse, ndipo tsiku likudza limene zinthu zonse zidzagwadira kwa ine.
60 Taonani, ndine Alefa ndi Omega, ngakhale Yesu Khristu.
61 Kotero, anthu onse achenjere m’mene iwo amatengera dzina langa pakamwa pawo—
62 Pakuti taonani, indetu ndikunena, kuti ambiri alipo amene ali pansi pa kutsutsidwa, amene amagwiritsa dzina la Ambuye, ndi kuligwiritsa ilo pachabe, opanda ulamuliro.
63 Kotero, lolani mpingo ulape pa machimo awo, ndipo ine Ambuye, ndidzawavomera iwo; apo ayi iwo adzadulidwa.
64 Kumbukirani kuti icho chimene chilinkudza kuchokera kumwamba ndi chopatulika, ndipo chikuyenera kuyankhulidwa mosamala, ndi moletsedwa ndi Mzimu; ndipo mu ichi mulibe kutsutsidwa, ndipo inu mumalandira Mzimu kudzera mu pemphero; kotero, popanda ichi kutsutsidwa kukadalipobe.
65 Mulekeni mtumiki wanga, Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon, afune nyumba, monga momwe aphunzitsidwira kudzera mu pemphero ndi Mzimu.
66 Zinthu izi zatsala kuti zigonjetsedwe kudzera ku chipiliro, kuti otero akathe kulandira ulemelero wopambanitsa komanso wamuyaya, apo ayi, kutsutsidwa kwakukulu. Ameni.