Gawo 3
Vumbulutso loperekedwa kwa Mneneri Joseph Smith, ku Harmony, Pennsylvania, Julaye 1828, zokhudza kutaika kwa masamba 116 a malembo apamanja omasulidwa kuchokera ku gawo loyamba la Buku la Mormoni, lomwe linkatchedwa buku la Lehi. Mneneriyo monyinyirika adalora masambawa kuchoka mu chisamaliro chake kupita kwa Martin Harris, amene adatumikira kwa nthawi yochepa ngati mlembi mu kumasulira kwa Buku la Mormoni. Vumbulutso lidaperekedwa kudzera mu Urimu ndi Tumimu. (Onani gawo 10.)
1–4, Njira ya Ambuye ndi kuzungulira kwamuyaya; 5–15 Joseph Smith akuyenera kulapa kapena kutaya mphatso kuti amasulire; 16–20, Buku la Mormoni likudza kudzapulumutsa mbewu ya Lehi.
1 Ntchito, ndi zopanga, ndi zolinga za Mulungu sizingathe kusokonezedwa, ngakhalenso izo sizingathe kukhala zapachabe.
2 Pakuti Mulungu sayenda m’njira zokhotakhota, ngakhalenso sapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere, kapena kusiyanitsa ndi zomwe wanena, kotero njira zake zili zowongoka, ndipo njira yake ndi yozungulira yamuyaya.
3 Kumbukirani, kumbukirani kuti si ntchito ya Mulungu yomwe imasokonezedwa, koma ntchito ya anthu;
4 Pakuti ngakhale munthu angakhale nawo mavumbulutso ambiri, ndi kukhala ndi mphamvu yakuchita zamphamvu zambiri, koma ngati adzitamandira mu mphamvu zake za iye yekha, ndi kupeputsa uphungu wa Mulungu, ndi kutsata zokhumba za iye mwini ndi zilakolako za thupi, akuyenera kudzagwa ndi kudzazibweletsera kubwenzera kwa Mulungu wolungama pa iye.
5 Taona, udapatsidwa udindo wa zinthu izi; koma malamulo ako adali okhwima bwanji; ndipo kumbukiranso malonjezo amene adalonjezedwa kwa iwe, ngati sudawalakwitse iwo
6 Ndipo taona, ndi kangati iwe walakwira malamulo a Mulungu, ndipo wapitilirabe mu zokopa za anthu.
7 Pakuti, taona, siwudayenera kuopa munthu koposa Mulungu. Ngakhale anthu amapeputsa uphungu wa Mulungu, ndi kunyoza mawu ake—
8 Koma ukadakhalabe wokhulupirika; ndipo akadatambasula mkono wake ndi kukuthandiza potsutsa mivi yonse yoyaka moto ya m’daniyo; ndipo akadakhala nawe munthawi za masautso onse.
9 Taona, ndiwe Joseph ndipo udasankhidwa kuchita ntchito ya Ambuye, koma chifukwa cha kulakwa, ngati sukudziwa udzagwa.
10 Koma kumbukira, Mulungu ndiwachifundo; kotero, lapa pa icho chimene wachita chimene chili chosemphana ndi lamulo limene ine ndidakupatsa iwe, ndipo iwe ukadali wosankhidwa, ndipo waitanidwanso ku ntchito;
11 Pokhapokha utachita izi, udzaperekedwa ndi kukhala ngati anthu ena, ndikukhala wopanda mphatso.
12 Ndipo pamene udapereka chimene Mulungu adakupatsa kupenya ndi mphamvu yakumasulira, udapereka icho chimene chidali chopatulika m’manja mwa munthu woipa.
13 Amene wapeputsa uphungu wa Mulungu, ndipo waphwanya malonjezo opatulika kwambiri amene adaperekedwa pamaso pa Mulungu, ndipo wadalira pa chiweruzo chake chomwe ndikudzitamandira mu nzeru zake zomwe.
14 Ndipo ichi ndi chifukwa chake chomwe wataya mwayi wako kwa kanthawi—
15 Pakuti walora uphungu wa wotsogolera wako kuponderezedwa kuyambira pachiyambi.
16 Komabe, ntchito yanga idzapita patsogolo, pakuti monga momwe chidziwitso cha Mpulumutsi chidadza ku dziko lapansi, kudzera mu umboni wa Ayuda, momwemonso chidziwitso cha Mpulumutsi chidzafika kwa anthu anga—
17 Ndipo kwa Anefi, ndi Ayakobo, ndi Ayosefe ndi Azoramu, kudzera mu umboni wa makolo awo—
18 Ndipo umboni uwu udzafika ku chidziwitso cha Alamani, ndi Alemueli, ndi Aismaeli, amene adacheperachepera m’kusakhulupilira chifukwa cha kusaweruzika kwa makolo awo, amene Ambuye adawalora kuti awononge abale awo Anefi, chifukwa cha mphulupulu zawo ndi zonyansa zawo.
19 Ndipo chifukwa cha cholinga ichi mapale awa asungidwa omwe ali ndi zolemba izi—kuti malonjezo a Ambuye akwaniritsidwe, amene adapanga kwa anthu ake;
20 Ndipo kuti Alamani akathe kubwera ku chidziwitso cha makolo awo, ndipo kuti akathe kudziwa malonjezano a Ambuye; ndipo kuti akathe kukhulupilira uthenga wabwino ndi kudalira pa ubwino wa Yesu Khristu, ndipo kuti akalemekezedwe kudzera m’chikhulupiliro m’dzina lake, ndipo kuti kudzera mu kulapa kwawo iwo akathe kupulumutsidwa. Ameni.