Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 10


Gawo 10

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Harmony, Pennsylvania, mwina chakumapeto kwa Epulo 1829, ngakhale magawo ena adali atalandiridwa kale m’chilimwe cha 1828. M’menemu Ambuye akudziwitsa Joseph za kusintha kopangidwa ndi anthu oipa m’masamba 116 a malembo a pamanja kuchokera mu kumasulira kwa buku la Lehi, mu Buku la Mormoni. Masamba olembedwa pamanja awa adali atataika m’manja mwa a Martin Harris, yemwe mapepalawo adamuikizira kwa kanthawi. (Onani mutu wa gawo 3.) Dongosolo loipa lidali kuyembekezera kumasuliridwansokwa nkhani yomwe yalembedwa ndi masamba obedwa ndipo kenako kunyozetsa womasulirayo posonyeza kusagwirizana komwe kudapangidwa ndi zosinthazo. Kuti cholinga choipa ichi chidakhazikitsidwa ndi oipayo ndipo chidadziwika kwa Ambuye ngakhale pamene Mormoni, wolemba mbiri yakale wachinefi, adali kupanga chidule chake cha mapale osonkhanitsidwa, chikusonyezedwa mu Buku la Mormoni.(onani Mawu a Mormoni 1:3–7).

1–26, Satana awutsa anthu oipa kuti atsutse ntchito ya Ambuye;27–33, Iye afunafuna kuwononga miyoyo ya anthu; 34–52, Uthenga wabwino ndi wopita kwa Alamani ndi mafuko onse kudzera mu Buku la Mormoni; 53–63, Ambuye adzakhazikitsa Mpingo Wake ndi uthenga Wake pakati pa anthu; 64–70, Iye adzasonkhanitsa olapa mu Mpingo Wake ndipo adzapulumutsa omvera.

1 Tsopano, taona, ndinena kwa iwe, kuti chifukwa udapereka zolembazo zimene udali nazo mphamvu zopatsidwa kwa iwe za kumasulira ndi njira ya Urimu ndi Tumimu, m’manja mwa munthu woipa, iwe wataya izo.

2 Ndipo iwenso udataya mphatso yako pa nthawi yomweyo, ndipo malingaliro ako adakhala odetsedwa.

3 Komabe, tsopano yabwezeretsedwanso kwa iwe; kotero ona kuti ndiwe okhulupirika, ndipo pitiriza kufikira kutha kwa ntchito yotsala ya kumasulira monga wayambira.

4 Osathamanga kwambiri kapena kugwira ntchito kuposa momwe ulili ndi mphamvu ndi njira zomwe zaperekedwa kuti uthe kumasulira; koma khala olimbika kufikira chimaliziro.

5 Pemphera nthawi zonse, kuti iwe ukathe kupezeka wogonjetsa; inde, kuti ukathe kumugonjetsa Satana, ndipo kuti ukapulumuke m’manja mwa atumiki a Satana amene akugwira ntchito yake.

6 Taona, akufuna kukuwononga; inde, ngakhale munthu amene umamukhulupilira wafuna kukuwononga.

7 Ndipo pachifukwa cha ichi ine ndidanena kuti iye ndi munthu woipa, pakuti iye adafuna kutenga zinthu zimene iwe udaikiziridwa; ndipo wafunanso kuwononga mphatso yako.

8 Ndipo chifukwa wapereka zolemba m’manja mwake, taona, anthu oipa adazitenga kwa iwe.

9 Chotero, iwe udazipereka izo, inde, zimene zidali zopatulika, kwa zoipa.

10 Ndipo taona, Satana waika izo m’mitima yawo kuti asinthe mawu amene waapangitsa kuti alembedwe, kapena amene waamasulira, amene atuluka m’manja mwako.

11 Ndipo taona, ndinena kwa iwe, kuti chifukwa iwo adasintha mawu, iwo adawerenga mosiyana ndi zimene iwe udamasulira ndi kupangitsa kuti zilembedwe;

12 Ndipo, mwa njira yotere, mdyerekezi wafuna kuika chiwembu chonyenga, kuti athe kuwononga ntchito iyi;

13 Pakuti iye waika mu mitima yawo kuti achite izi, kuti mwa kunama iwo akathe kunena kuti adakugwira iwe m’mawu amene iwe udanamizira kumasulira.

14 Indetu, ndinena kwa iwe, kuti sindidzalola kuti Satana akwaniritse dongosolo lake loipa mu chinthu ichi.

15 Pakuti taona, waika m’mitima mwawo kuti uyese Ambuye Mulungu wako, mu kupempha kuti ulimasulirenso.

16 Ndipo kenako, taona, akunena ndi kuganiza m’mitima mwawo—Tiona ngati Mulungu wampatsa mphamvu yomasulira; ngati watero, adzamupatsanso iye mphamvu;

17 Ndipo ngati Mulungu wamupatsanso iye mphamvu, kapena ngati iye atamasulirenso, kapena, m’mawu ena, ngati iye atabweretse mawu omwewo, taonani, tili nawo omwewo ndi ife, ndipo tawasintha;

18 Kotero sadzagwirizana, ndipo tidzanena kuti iye wanama m’mawu ake, ndipo kuti iye alibe mphatso, ndipo kuti iye alibe mphamvu;

19 Kotero tidzamuwononga iye, ndiponso ntchitoyo; ndipo tidzachita izi kuti tisadzachite manyazi pamapeto pake, ndi kuti tikathe kulandira ulemelero wa dziko lapansi.

20 Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, kuti Satana ali nacho chogwira chachikulu pa mitima yawo; iye wautsa iwo kuchita mphulupulu motsutsana ndi izo zimene zili zabwino;

21 Ndipo mitima yawo ili yovunda, ndi yodzadza ndi zoipa ndi zonyansa; ndipo amakonda mdima koposa kuwala, pakuti ntchito zawo ndi zoipa; kotero sadzandipempha ine.

22 Satana amawautsa iwo, kuti akathe kutsogolera miyoyo yawo ku chiwonongeko.

23 Ndipo kotero iye waika dongosolo lachinyengo, kuganiza kuti awononge ntchito ya Mulungu; koma ndidzafuna ichi m’manja mwawo, ndipo chidzatembenuka ku manyazi awo ndi chitsutso pa tsiku la chiweruzo.

24 Inde, amautsa mitima yawo kuti akwiyire ntchito imeneyi.

25 Inde, amanena kwa iwo: Chinyengo ndi kunama pakubisalira kuti mugwire, kuti mukathe kuwononga; taonani, ichi sichili choipa. Ndipo kotero iye amawanyengeza iwo, ndi kuwauza iwo kuti si tchimo kunama kuti akathe kugwira munthu mu bodza, kuti akathe kumuwononga.

26 Ndipo motero iye amawanyengeza iwo, ndikuwatsogolera mpaka ataikokera miyoyo yawo ku gahena; ndipo motero amawapangitsa iwo kudzikola okha mu msampha wawo womwe.

27 Ndipo kotero iye amakwera ndi kutsika, uku ndi uko padziko lapansi, kufunafuna kuwononga miyoyo ya anthu.

28 Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, tsoka likhale kwa iye amene amanama kuti apusitse chifukwa iye amayesa kuti wina amanama kuti apusitse, pakuti otere sali okhululukidwa ku chilungamo cha Mulungu.

29 Tsopano, taona, iwo asintha mawu awa, chifukwa Satana amanena kwa iwo: Iye wakupusitsani inu—ndipo motero iye amawakopa iwo kuti achite mphulupulu, kuti akupangitse iwe kuti uyese Ambuye Mulungu wako.

30 Taona, ndinena kwa iwe, kuti sudzamasuliranso mawu amenewo amene apita kuchokera m’manja mwako;

31 Pakuti, taona, iwo sadzakwaniritsa zolinga zawo zoipa mu kunama motsutsa mawu amenewo. Pakuti, taona, ngati utatulutse mawu omwewo iwo adzanena kuti wanama ndi kuti wanamizira kumasulira, koma kuti wadzitsutsa wekha.

32 Ndipo, taona, iwo adzafalitsa izi, ndipo Satana adzaumitsa mitima ya anthu kuti awautse iwo kutsutsana nawe, kuti asadzakhulupilire mawu anga.

33 Motere Satana akuganiza kugonjetsa umboni wako mu m’badwo uno, kuti ntchitoyi isathe kubwera mu m’badwo uno.

34 Koma taona, pano pali nzeru, ndipo chifukwa ine ndikuonetsa kwa iwe nzeru, ndi kukupatsa iwe malamulo okhudzana ndi zinthu izi, zimene iwe udzachite, usadzaonetse izo kwa dziko mpaka iwe utakwaniritsa ntchito yomasulira.

35 Usadabwe kuti ndidanena kwa iwe: Pano pali nzeru, usadzazionetse kwa dziko—pakuti ndidanena, usadzazionetse ku dziko, kuti upulumuke.

36 Taona, sindikunena kuti sudzazionetsa kwa olungama;

37 Koma monga sungathe kudziwa olungama nthawi zonse, kapena monga sungathe kudzadziwa nthawi zonse kusiyanitsa oipa kuchokera kwa olungama, kotero ine ndinena kwa iwe, khala kaye mpaka ine ndidzaone koyenera kuti zinthu zonse zidziwike kwa dziko zokhudza nkhaniyi.

38 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa iwe, kuti nkhani ya zinthu zimenezo zimene iwe walemba, zimene zapita kuchokera m’manja mwako, ndi zozokotedwa pa mapale a Nefi;

39 Inde, ndipo ukukumbukira kuti zidanenedwa mu zolembedwa zimenezo kuti nkhani yodziwika kwambiri idaperekedwa ya zinthu izi pa mapale a Nefi.

40 Ndipo tsopano, chifukwa zolembedwa zimene zidazokotedwa pamapale a Nefi ndi zodziwika kwambiri zokhudza zinthu zimene, mu nzeru zanga, ndidzabweretsa ku chidziwitso cha anthu munkhani izi—

41 Kotero, udzamasulira zozokotedwa zimene zili pa mapale a Nefi, kutsika ngakhale mpaka iwe udzafika ku ufumu wa mfumu Benjamini, kapena mpaka iwe utabwera kwa izo zimene iwe wamasulira, zimene iwe wabwenzeredwa;

42 Ndipo taona, udzazitsindikiza monga zolemba za Nefi; ndipo motero ndidzasokoneza iwo amene asintha mawu anga.

43 Sindidzalola kuti iwo awononge ntchito yanga; inde, ine ndidzaonetsa kwa iwo kuti nzeru zanga ndi zazikulu kuposa chinyengo cha mdyerekezi.

44 Taona, iwo ali ndi kagawo kokha, kapena chidule cha nkhani ya Nefi.

45 Taona, pali zinthu zambiri zozokotedwa pa mapale a Nefi zomwe zimaponya mawonedwe okulirapo pa uthenga wanga; kotero, ndi nzeru mwa ine kuti umasulire gawo loyambali la zozokota za Nefi, ndi kutumiza mu ntchito iyi.

46 Ndipo taona, yotsala yonse ya ntchito iyi ili ndi zigawo zonse izo za uthenga wanga zimene aneneri anga oyera, inde, ndiponso ophunzira anga, adakhumba m’mapemphero awo kuti ibwere kwa anthu awa.

47 Ndipo ine ndidati kwa iwo, kuti zikuyenera kuperekedwa kwa iwo molingana ndi chikhulupiliro chawo m’mapemphero awo;

48 Inde, ndipo ichi chidali chikhulupiliro chawo—kuti uthenga wanga, umene ndidapereka kwa iwo kuti akalalikire m’masiku awo, ukafike kwa abale awo Alamani, ndiponso onse amene adakhala Alamani chifukwa cha kugawanikana kwawo.

49 Tsopano, izi sizokhazi—chikhulupiliro chawo m’mapemphero awo chidali chakuti uthenga uwu udziwikenso, ngati kukadakhala kotheka kuti mitundu ina itenge dziko ili;

50 Ndipo kotero adasiya mdalitso pa dziko ili m’mapemphero awo, kuti aliyense amene angakhulupilire uthenga uwu m’dziko lino akathe kukhala ndi moyo wosatha;

51 Inde, kuti likathe kukhala laufulu kwa onse a dziko lililonse, fuko, lilime, kapena anthu omwe angakhale.

52 Ndipo tsopano, taona, molingana ndi chikhulupiliro chawo m’mapemphelo awo ndidzabweretsa gawo ili la uthenga wanga ku chidziwitso cha anthu anga. Taona, sindidzaubweretsa kuti ndidzawononge izo zomwe adalandira, koma kudzazimangilira.

53 Ndipo pachifukwa cha ichi ndati: Ngati m’badwo uwu suumitsa mitima yawo, ndidzakhazikitsa mpingo wanga pakati pawo.

54 Tsopano ine sindikunena izi kuti ndiwononge mpingo wanga, koma ine ndikunena izi kuti ndimange mpingo wanga;

55 Kotero, aliyense amene ali wa mpingo wanga sakuyenera kuopa, pakuti oterowo adzalandira ufumu wa kumwamba.

56 Koma ali iwo amene samandiwopa ine, kapena kusunga malamulo anga koma amamanga mipingo kwa iwo eni kuti apeze phindu, inde, ndi onse amene amachita zoipa ndi kumanga ufumu wa mdyerekezi—inde, indetu, indetu, ndinena kwa iwe, kuti ndi iwo amene ndidzasokoneza, ndi kuchititsa kunjenjemela ndi kugwedezeka pakati.

57 Taona, ine ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Ndidadza kwa anga, ndipo anga omwe sadandilandire.

58 Ine ndine kuunika kumene kumawala mumdima, ndipo mdima siumakuzindikira.

59 Ndine amene ndidati—Nkhosa zina ndili nazo zomwe sizili za khola ili—kwa ophunzira anga, ndipo ambiri adalipo amene sadandimvetse.

60 Ndipo ndidzaonetsa kwa anthu awa kuti ndidali nazo nkhosa zina, ndi kuti zidali nthambi ya nyumba ya Yakobo;

61 Ndipo ndidzabweletsa poyera zodabwitsa zawo, zimene adazichita mu dzina langa;

62 Inde, ndipo ndidzabweretsanso poyera uthenga wanga wabwino umene udatumikiridwa kwa iwo, ndipo, taona, iwo sadzakana chimene iwe walandira, koma adzachimanga, ndipo adzabweretsa poyera mfundo zoona za chiphunzitso changa, inde; ndi chiphunzitso chokhacho chimene chili mwa ine.

63 Ndipo izi ndimachita kuti ine ndithe kukhazikitsa uthenga wanga, kuti pasakathe kukhala mikangano yochuluka; inde, Satana amautsa mitima ya anthu ku kukangana zokhudzana ndi mfundo za chiphunzitso changa; ndipo mu zimenezi amalakwitsa, pakuti iwowa amapotoza malembo ndipo samawamvetsa.

64 Kotero, ine ndidzatambasula kwa iwo chinsinsi chachikulu ichi;

65 Pakuti, taona, ndidzawasonkhanitsa monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake pansi pa mapiko ake, ngati sadzaumitsa mitima yawo;

66 Inde, ngati akufuna kudza, akhonza, ndi kudzamwako madzi a moyo kwaulere.

67 Taona, ichi ndi chiphunzitso changa—aliyense amene walapa ndi kudza kwa ine, yemweyo ali mpingo wanga.

68 Aliyense amene alengeza mochuluka kapena mochepera kuposa izi, yemweyo sali wa ine, koma ali wotsutsana ndi ine; kotero iye sali wa mpingo wanga.

69 Ndipo tsopano, taona, aliyense amene ali wa mpingo wanga, ndipo adzapilira mu mpingo wanga mpaka kumapeto, iye ndidzamukhazikitsa pa thanthwe langa, ndipo zipata za gahena sizidzawagonjetsa iwo.

70 Ndipo tsopano, kumbukira mawu a iye amene ali moyo ndi kuunika kwa dziko lapansi, Muwomboli wako, Ambuye wako ndi Mulungu wako. Ameni.