Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 36


Gawo 36

Vumbulutso loperekedwa kudzera kwa Joseph Smith Mneneri kwa Edward Partridge, kufupi ndi Fayette, New York, 9 Disembara 1830 (onani mutu wa gawo 35). Mbiri ya Joseph Smith imanena kuti Edward Partridge “adali chitsanzo cha umulungu, ndipo adali m’modzi wa anthu opambana a Ambuye.”

1–3, Ambuye asanjika dzanja Lawo pa Edward Partridge ndi dzanja la Sidney Rigdon; 4–8, Munthu aliyense amene walandira uthenga wabwino ndi unsembe ndiwoitanidwa kuti apite ndi kukalalikira.

1 Atero Ambuye Mulungu, Wamphamvu wa Israeli: Taona, ndikunena kwa iwe, mtumiki wanga Edward, kuti ndiwe odala, ndipo machimo ako akhululukidwa, ndipo iwe waitanidwa kukalalikira uthenga wanga monga ndi mawu a lipenga;

2 Ndipo ndidzasanjika dzanja langa pa iwe ndi dzanja la mtumiki wanga Sidney Rigdon, ndipo iwe udzalandira Mzimu wanga, Mzimu Woyera, ngakhale Mtonthozi, amene adzakuphunzitsa iwe zinthu za mtendere wakumwamba;

3 Ndipo iwe udzalengeza ichi ndi mawu okweza, nati: Hosana, lodala likhale dzina la Mulungu wam’mwambamwamba.

4 Ndipo tsopano, maitanidwe awa ndi lamulo ndikupereka kwa iwe zokhudzana anthu onse—

5 Kuti monga momwe ambiri adzabwera pamaso pa atumiki anga Sidney Rigdon ndi Joseph Smith, Jun., kuvomera maitananidwe awa ndi lamulo, adzadzodzedwa ndi kutumizidwa kukalalikira uthenga wosatha pakati pa maiko—

6 Kufuula kulapa, nati: Dzipulumutseni nokha kuchokera ku m’badwo wokhotakhotawu, ndi kutuluka ku moto, kudana ngakhale chovala chodetsedwa ndi mnofu.

7 Ndipo lamulo ili lidzaperekedwa kwa akulu a mpingo wanga, kuti munthu aliyense amene alivomeleze ndi mtima umodzi angathe kudzodzedwa ndi kutumizidwa, ngakhale monga momwe ndayankhulira.

8 Ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu; kotero, mangani malamba mchiuno mwanu ndipo ndidzabwera modzidzimutsa ku kachisi wanga. Ngakhale zili choncho. Ameni.