Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 41


Gawo 41

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Mpingo, ku Kirtland, Ohio, Febuluwale 4, 1831. Vumbulutso ili likulangiza Mneneri ndi akulu a Mpingo kupemphera kuti alandire “lamulo” la Mulungu (onani gawo 42). Joseph Smith adali atangofika kumene mu Kirtland kuchokera ku New York, ndipo Leman Copley, membala wa Mpingo pafupi ndi Thompson, Ohio, “adapempha M’bale Joseph ndi Sidney [Rigdon] …akhale naye ndipo awapatsa nyumba ndi zakudya.” Vumbulutso lotsatirali likutambasula bwino kumene Joseph ndi Sidney akuyenera kukhala komanso laitana Edward Partridge kukhala bishopu woyamba wa Mpingo.

1–3, Akulu adzatsogolera Mpingo ndi mzimu wa vumbulutso; 4–6, Ophunzira oona adzalandira ndi kusunga chilamulo cha Ambuye; 7–12, Edward Partridge atchulidwa ngati bishopu ku Mpingo.

1 Mvetserani ndi kumva, O inu anthu anga, atero Ambuye ndi Mulungu wanu, inu amene ndikondwera kukudalitsani ndi madalitso aakulu koposa onse, inu amene mumandimva; ndipo inu amene simumandimvera ndidzatembelera, amene mwatchula dzina langa ndi matembelero aakulu koposa onse.

2 Mvetserani, O inu akulu a mpingo wanga amene ndaitana, taonani ndikupereka kwa inu lamulo, kuti mudzadzisonkhanitsa nokha pamodzi kuti mugwirizane pa mawu anga;

3 Ndipo ndi pemphero la chikhulupiliro chanu mudzalandira lamulo langa; kuti muthe kudziwa kutsogolera mpingo wanga, ndi kukhala nazo zonse pamaso panga.

4 Ndipo ndidzakhala wolamulira wanu ndikadzabwera; ndipo onani, ndidza msanga, ndipo mudzaona kuti lamulo langa likusungidwa.

5 Iye amene walandira chilamulo changa ndi kuchichita, yemweyo ndiye wophunzira wanga; ndipo yemwe anena kuti walandira ndi kusachichita, yemweyo sali wopunzira wanga, ndipo adzachotsedwa kuchokera pakati panu;

6 Pakuti sikoyenera kuti zinthu za ana a ufumu ziperekedwe kwa iwo amene sioyenelera, kapena kwa agalu, kapena ngale kuponyedwa pamaso pa nkhumba.

7 Ndiponso, ndikoyenera kuti mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., akhale ndi nyumba yomangidwa, momwe angakhale ndi kumasulira.

8 Ndiponso, ndikoyenera kuti mtumiki wanga Sidney Rigdon akuyenera akakhale monga momwe iye akufunira, pamene iye akusunga malamulo anga.

9 Ndiponso, ndaitana mtumiki wanga Edward Partridge; ndipo ndikupereka lamulo, kuti iye asankhidwe ndi mawu a mpingo, ndi kudzodzedwa bishopu ku mpingo; kusiya malonda ake ndi kuthera nthawi yake yonse mu ntchito za mpingo;

10 Kuona zinthu zonse monga zidzaikidwa kwa iye mu malamulo anga mu tsiku limene ndidzawapereka iwo.

11 Ndipo ichi chifukwa mtima wake ndi woyera pamaso panga, pakuti ali ngati Natanayeli wakale, amene mulibe chinyengo.

12 Mawu awa apatsidwa kwa inu, ndipo iwo ndi oyera pamaso panga; kotero, chenjerani momwe inu mukuzigwilira izo, pakuti zidzayankhidwa pa miyoyo yanu m’tsiku la chiweruzo. Ngakhale zili choncho. Ameni.