Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 56


Gawo 56

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Juni 15, 1831. Vumbulutso ili likudzudzula Ezra Thayre pakusamvera vumbulutso lakale (“lamuloli” lotchulidwa mu ndime 8), limene Joseph Smith adalandira kwa iye, kulangiza Thayre zokhudzana ndi ntchito zake pamunda wa Frederick G. Williams, kumene iye ankakhala. Vumbulutso lotsatirali likuletsanso kuitanidwa kwa Thayre kuti apite ku Missouri ndi Thomas B. Marsh (onani gawo 52:22).

1–2, Oyera Mtima akuyenera kunyamula mtanda wawo ndi kutsata Ambuye kuti apeze chipulumutso; 3–13, Ambuye amalamula ndi kuletsa, ndipo osamvera amachotaidwa; 14–17, Tsoka kwa olemera amene samathandiza osauka, ndipo tsoka kwa osauka amene mitima yawo siyosweka; 18–20, Odala ali osauka amene ali oyera mtima, pakuti adzalandira dziko lapansi,

1 Mvetserani, O inu anthu amene mumatchula dzina langa, atero Ambuye Mulungu wanu; pakuti taonani, mkwiyo wanga wayaka motsutsana ndi wopanduka, ndipo iwo adzadziwa mkono wanga ndi ukal wanga, mu tsiku la kuyenderedwa ndi la mkwiyo pa maiko.

2 Ndipo iye amene sadzanyamula mtanda wake ndi kunditsata ine, ndi kusunga malamulo anga, yemweyo sadzapulumutsidwa.

3 Taonani, ine, Ambuye, ndikulamula; ndipo iye amene sadzamvera adzadulidwa mu nthawi yanga yoikika, ine nditalamula ndipo lamulolo laphwanyidwa.

4 Kotero ine, Ambuye, ndimalamula ndi kuchotsa, momwe ine ndakondera; ndipo zonsezi zidzayankhidwa pa mitu ya wopanduka, atero Ambuye.

5 Kotero, ine ndikuchotsa lamulo limene ndidapereka kwa atumiki anga Thomas B. Marsh ndi Ezra Thayre, ndikupereka lamulo latsopano kwa mtumiki wanga Thomas, kuti iye ayambe ulendo wake mwachangu kupita ku dziko la Missouri, ndipo mtumiki wanga Selah J. Griffin adzapitanso naye.

6 Pakuti taonani, ndikuchotsa lamulo limene lidaperekedwa kwa atumiki anga Selah J. Griffin ndi Newel Knight, potsatira kwa kusamvera kwa anthu anga amene ali ku Thompson, ndi kupanduka kwawo.

7 Kotero, lolani mtumiki wanga Newel Knight akhale ndi iwo; ndipo pamene ambiri amene akufuna angathe kupita, amene ali olapa pamaso panga, ndi kutsogoleledwe ndi iye ku dziko limene ine ndalisankha.

8 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, kuti mtumiki wanga Ezra Thayre akuyenera kulapa pa kunyada kwake, ndi kudzikonda kwake, ndi kumvera lamulo lakale limene ndidapereka kwa iye lokhudzana ndi malo amene iye akukhala.

9 Ndipo ngati iye achita ichi, pamene sipadzakhala migawaniko yopangidwa pa dzikolo, iye adzasankhidwa kuti apitebe ku dziko la Missouri;

10 Apo ayi iye adzalandira ndalama zimene iye adapereka, ndipo adzachoka kumalowo, ndipo adzachotsedwa mu mpingo wanga, atero Ambuye Mulungu wamakamu;

11 Ndipo ngakhale kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, mawu awa sadzatha, koma adzakwaniritsidwa.

12 Ndipo ngati mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., akufunikira kupereka ndalamazo, taonani, ine, Ambuye, ndidzaperekanso kwa iye mu dziko la Missouri, kuti iwo amene iye adzawalandire adzalipidwanso molingana ndi icho chimene iwo achita;

13 Pakuti molingana ndi icho chimene iwo amachita iwo adzalandira, ngakhale mu dziko la cholowa chawo.

14 Taonani, akutero Ambuye kwa anthu anga—muli ndi zinthu zambiri zochita ndi zoti mulape; pakuti taonani, machimo anu afika kwa ine, ndipo simudakhulukidwe, chifukwa mumafunafuna uphungu mu njira zanu zomwe.

15 Ndipo mitima yanu ndiyosakhutitsidwa. Ndipo simumvera choonadi, koma mukondwera mu kusalungama.

16 Tsoka kwa inu anthu olemera, amene simupereka chuma chanu kwa osauka, pakuti chuma chanu chidzaumitsa miyoyo yanu; ndipo ichi chidzakhala cholilitsa chanu mu tsiku la kuyenderedwa, ndi la chiweruzo ndi la ukali: Kukolola kwatha, chilimwe chatha, ndipo moyo wanga sudapulumutsidwe!

17 Tsoka kwa inu anthu osauka, amene mitima yanu siyosweka, amene mizimu yanu siyolapa, ndi amene mimba zanu sizokhutitsidwa, ndi amene manja anu saletsedwa kuikidwa pa zinthu za anthu ena, amene maso anu ndi odzadza ndi dyera, ndi amene simugwira ntchito ndi manja anu!

18 Koma odala ndi osauka amene mitima yawo ndi yoyera, amene mitima yawo ndi yosweka, ndi amene mizimu yawo ndi yolapa, pakuti iwo adzaona ufumu wa Mulungu ukubwera mu mphamvu ndi ulemelero waukulu kwa chipulumutso chawo; pakuti zonenepetsa za dziko lapansi zidzakhala zawo.

19 Pakuti taonani, Ambuye adzabwera, ndipo malipilo yake idzakhala ndi iye, ndipo iye adzalipira kwa munthu aliyense, ndipo osauka adzakondwera;

20 Ndipo mibadwo yawo idzalandira dziko lapansi kuchokera ku m’badwo ndi m’bawo, kunthawi za nthawi zosatha. Ndipo tsopano ine ndikumaliza kuyankhula kwa inu. Ngakhale choncho. Ameni.