Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 90


Gawo 90

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Malitchi 8, 1833 Vumbulutso ili ndi kupitiriza pang’onopang’ono kukhazikitsa kwa Atsogoleri Oyamba (onani mutu wa gawo 81); ngati zotsatira zake, alangizi otchulidwawo adadzodzedwa pa Malitchi 18, 1833.

1–5, Mafungulo a ufumu aperekedwa kwa Joseph Smith ndipo kudzera mwa iyeyo kupita ku mpingo; 6–7, Sidney Rigdon ndi Frederick G. Williams akuyenera kutumikira mu Utsogoleri Woyamba; 8–11, Uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa ku maiko a Israeli, kwa Amitundu, ndi kwa Ayuda, munthu aliyense kumvera mu chiyankhulo chake; 12–18, Joseph Smith ndi aphungu ake akuyenera kukhazikitsa Mpingo mu dongosolo; 19–37, Anthu osiyanasiyana alangizidwa ndi Ambuye kuti ayende mowongoka ndi kutumikira mu ufumu Wake.

1 Akutero Ambuye, indetu, indetu ndikunena kwa iwe mwana wanga, machimo ako akhululukidwa, molingana ndi pempho lako, pakuti mapemphero ako ndi mapemphero a abale ako afika m’makutu mwanga.

2 Kotero, ndiwe odala kuyambira pano kupita mtsogolo amene wanyamula mafungulo a ufumu operekedwa kwa iwe; umene ufumu wake ukudza kwa nthawi yomaliza.

3 Indetu ndikunena kwa iwe, mafungulo a ufumu uwu sadzatengedwa kwa iwe, pamene iwe udakali mu dziko, ngakhale mu dziko lilinkudza;

4 Komabe, kudzera mwa iwe masomphenyawa adzaperekedwa kwa ena, inde ngakhale kwa mpingo.

5 Ndipo onse amene alandira masomphenya a Mulunguwa, achenjere momwe amawagwirizira kuopa angawatenge ngati chinthu chopepuka, ndi kubweretsedwa pansi pa chiweruzo potero, ndi kuphunthwa ndi kugwa pamene anamondwe atsika, ndi mphepo ziwomba, ndi mvula itsika, ndi kuwomba nyumba zawo.

6 Ndiponso, ndinena kwa abale ako, Sidney Rigdon ndi Frederick G. Williams, machimo awo akhululukidwanso, ndipo akutengedwa monga chimodzimodzi ndi iwe mu kusunga mafungulo a ufumu omalizawu;

7 Monganso kudzera mu utumiki wako mafungulo a sukulu ya aneneri, imene ndakulamula kuti ukhazikitse;

8 Kuti potero iwo akathe kukhala angwiro mu utumiki wawo ku chipulumutso cha Ziyoni, ndi cha maiko a Israeli, ndi cha Amitundu, pamene ambiri adzakhulupilira;

9 Kuti kudzera mu utumiki wako iwo akathe kulandira mawu, ndi kudzera mu utumiki wawo mawu akathe kupita ku malekezero a dziko lapansi, kwa Amitundu koyamba, ndipo kenako, taonani, ndipo onani, iwo adzatembenukira kwa Ayuda.

10 Ndipo kenako likudza tsiku limene mkono wa Ambuye udzaululidwa mu mphamvu mukutsimikizira maiko, maiko achikunja, nyumba ya Yosefe, ndi uthenga wabwino wa chipulumutso chawo.

11 Pakuti zidzachitika mu tsikulo, kuti munthu aliyense adzamva chidzalo cha uthenga wabwino mu lilime lake, ndi mu chiyankhulo chake, kudzera mwa iwo amene adzodzedwa ku mphamvu imeneyi, mwa kutumikira kwa Mtonthozi, wotsanulidwa pa iwo ku mavumbulutso a Yesu Khristu.

12 Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu, ndikupereka kwa inu lamulo kuti mupitirize mu utumiki ndi utsogoleri.

13 Ndipo pamene inu mwamaliza kumasulira kwa aneneri, kuchokera pamenepo mudzatsogolera zochitika za mpingo ndi sukulu;

14 Ndipo ku nthawi ndi nthawi, monga zidzaonetsedwa mwa Mtonthozi, mudzalandira mavumbulutso kuti mutambasule zinsinsi za ufumu;

15 Ndi kukhazikitsa mu dongosolo mipingo, ndi kuwerenga, ndi kuphunzira, ndi kukhala odziwa mabuku onse, ndi ziyankhulo, malilime ndi anthu.

16 Ndipo ichi chidzakhala chochita chanu ndi ntchito mu moyo wanu wonse, kutsogolera mu msonkhano, ndi kukhazikitsa mu dongosolo zochitika zonse za mpingowu ndi ufumu.

17 Musachite manyazi, kapena kusokonezedwa; koma mudzudzulidwe mu kudzikweza ndi kunyada kwanu konse, pakuti zimabweretsa msampha ku miyoyo yanu.

18 Khazikitsani mu dongosolo nyumba zanu; ikani ulesi ndi umve kutali nanu.

19 Tsopano, indetu ndinena kwa inu, lolani malo apezeke, mwachangu, kwa banja la aphungu anga ndi alembi, ngakhale Frederick G. Williams.

20 Ndipo lolani mtumiki wanga wachikulire, Joseph Smith, Sen., apitirize ndi banja lake pa malo amene akukhala tsopano; ndipo asagulitsidwe kufikira zitanenedwa ndi kamwa la Ambuye.

21 Ndipo lolani mlangizi wanga, ngakhale Sidney Ridgon, akhalebe kumene akukhala tsopano kufikira zitanenedwa ndi kamwa la Ambuye.

22 Ndipo lolani bishopu afunefune mwakhama kuti apeze womuthandizira, ndipo mloleni iye akhale munthu amene ali ndi chuma chake—munthu wa Mulungu, ndi wachikhulupiliro cha mphamvu—

23 Kuti potero iye akathe kukwanitsa kupereka ngongole zilizonse; kuti nkhokwe ya Ambuye musakakhale kunyozeka pamaso pa anthu.

24 Funafunani mwakhama, pempherani nthawi zonse, ndipo khalani okhulupilira, ndipo zinthu zonse zidzagwira ntchito pamodzi kwa ubwino wanu, ngati inu muyenda mowongoka ndi kukumbukira pangano limene inu mudapangana wina ndi mzake.

25 Lolani mabanja anu akhale ochepa, makamaka mtumiki wanga wachikulire Joseph Smith Sen., monga zokhudza amene sali abanja lanu;

26 Kuti zinthu zimenezo zimene zaperekedwa kwa inu, kuti zithandize ntchito yanga, zisatengedwe kuchokera kwa inu ndi kupatsidwa kwa iwo amene sali oyenera—

27 Ndipo potero mungathe kulepheretsedwa mu kukwaniritsa zinthu izo zimene ine ndakulamulani inu.

28 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ndi chifuniro changa kuti mdzakazi wanga Viena Jaques alandire ndalama kuti agulire zinthu zake, ndi kupita ku dziko la Ziyoni.

29 Ndipo ndalama zotsalirazo zipatulidwe kwa ine, ndipo iye adzalipidwa mu nthawi yanga yoikika.

30 Indetu ndikunena kwa inu, kuti ndikofunikira m’maso mwanga kuti iye apite ku dziko la Ziyoni, ndi kulandira cholowa kuchokera ku dzanja la bishopu;

31 Kuti iye akathe kukhazikika mu mtendere pamene iye ali wokhulupirika, ndi kusachita ulesi mu masiku ake kuchokera pano.

32 Ndipo taonani, ndikunena kwa inu, kuti mudzalembe lamulo ili, ndi kunena kwa abale mu Ziyoni, mu moni wachikondi, kuti ndaitana inunso kuti mutsogolere pa Ziyoni mu nthawi yanga yoikika.

33 Kotero, lolani iwo asiye kunditopetsa ine zokhudza nkhani iyi.

34 Taonani, ndikunena kwa inu kuti abale anu mu Ziyoni ayamba kulapa, ndipo angelo akukondwera nawo.

35 Komabe, sindili wokondwera ndi zinthu zambiri; ndipo sindikukondwera ndi mtumiki wanga William E. McLellin, ngakhale ndi mtumiki wanga Sidney Gilbert; ndiponso bishopu, ndipo ena ali ndi zinthu zambiri zoti alape.

36 Koma indetu ndinena kwa inu, kuti, ine, Ambuye, ndidzalimbana ndi Ziyoni, ndi kuchondelera ndi anyonga ake, ndi kumudzudzula kufikira iye atagonjetsa ndipo ndi oyera pamaso panga.

37 Pakuti iye sadzachotsedwa pa malo pake. Ine, Ambuye, ndanena ichi. Ameni.