Gawo 88
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri ku Kirtland, Ohio, Disembala 27 ndi 28, 1832, ndi Januwale 3, 1833. Mneneri adalitcha “‘tsamba la azitona’ … lozulidwa mu Mtengo wa Paradiso, uthenga wa Ambuye wamtendere kwa ife.” Vumbulutsolo lidaperekedwa ansembe aakulu pa msonkhano atapemphera “paokha ndi mokweza mawu kwa Ambuye kuti avumbulutse chifuniro chake kwa ife zokhudzana ndi kumangidwa kwa Ziyoni.”
1–5, Oyera mtima okhulupirika amalandira Mtonthozi ameneyo, amene ali lonjezo la moyo wosatha; 6–13, Zinthu zonse zimalamulidwa ndi kulamuliridwa ndi Kuwala kwa Khristu; 14–16, Chiukitso chimadza kudzera mu Chiwombolo; 17–31, Kumvera ku lamulo la selestiyo, la terestriyo, kapena la telestiyo kumakonzekeretsa anthu ku maufumu ndi ulemererowo; 32–35, Awo amene akufuna kukhala mu uchimo akhalabe anyansi; 36–41, Maufumu onse amalamulidwa ndi chilamulo; 42–45, Mulungu adapereka lamulo kwa zinthu zonse; 46–50, Munthu adzazindikira ngakhale Mulungu; 51–61, Fanizo la munthu wotumiza antchito ake kumunda ndi kuwayendera iwo motsatira; 62–73, Yandikirani kwa Ambuye, ndipo mudzaona nkhope Yake; 74–80, Dziyeretseni nokha ndi kuphunzitsana wina ndi mzake ziphunzitso za ufumu; 81–85, Munthu aliyense amene wachenjezedwa akuyenera kuchenjeza mnansi wake; 86–94, Zizindikiro, kugwedezeka kwa chilengedwe, ndi angelo amakonza njira ya kudza kwa Ambuye; 95–102, Malipenga aungelo amaitana akufa mu dongosolo lawo; 103–116, Malipenga a angelo alengeza za chibwenzeretso cha uthenga wabwino, kugwa kwa Babulo, ndi nkhondo ya Mulungu wamkulu; 117–126, Funani maphunziro, khazikitsani nyumba ya Mulungu (kachisi), ndipo mudziveke nokha ndi chomangira cha chikondi; 127–141, Dongosolo la Sukulu ya Aneneri ikhazikitsidwa, kuphatikizapo mwambo wa kusambitsa mapazi.
1 Indetu, akutero Ambuye kwa inu amene mwasonkhana pamodzi kuti mulandire chifuniro chake chokhudzana ndi inu:
2 Taonani, izi ndi zokondweretsa kwa Ambuye wanu, Ndipo angelo akukusangalalirani; zachifundo za mapemphero anu zafika m’makutu a Ambuye wa Makamu, ndipo alembedwa m’buku la maina a opatulidwa, ngakhale iwo a dziko la selestiyo.
3 Kotero, tsopano nditumiza pa inu Mtonthozi wina, ngakhale pa inu abwenzi anga, kuti akhale m’mitima yanu, inde Mzimu Woyera wa malonjezano; amene Mtonthozi wina ndi yemweyo amene ine ndidalonjeza kwa ophunzira anga, monga kwalembedwa mu umboni wa Yohane.
4 Mtonthozi uyu ndi lonjezo limene ndipereka kwa inu la moyo wosatha, ngakhale ulemelero wa ufumu waselestiyo;
5 Ulemelero umene uli wa mpingo wa Woyamba Kubadwa, ngakhale wa Mulungu, woyera wopambana onse, kudzera mwa Yesu Khristu Mwana wake—
6 Iye amene adakwera kumwamba, monganso adatsikira pansi pa zinthu zonse, m’menemo adazindikira zinthu zonse, kuti akathe kukhala mu zonse ndi kudzera m’zinthu zonse, kuunika kwa choonadi;
7 Choonadi chimene chimawala. Uku ndiko kuwala kwa Khristu. Monganso iye ali mu dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa, ndi mphamvu yake imene lidapangidwa.
8 Monganso iye ali mu mwezi, ndi kuwala kwa mwezi, ndi mphamvu yake imene udapangidwa;
9 Monganso kuwala kwa nyenyezi, ndi mphamvu yake imene zidalengedwa;
10 Ndipo dziko lapansiso, ndi mphamvu yake, ngakhale dziko lapansi pamene inu muima.
11 Ndi kuunika komwe kumawala, komwe kukupatsa inu kuunika, kuli mwa iye amene amaunikira maso anu, komwe kuli kuunika komweko komwe kumafulumizitsa kuzindikira kwanu;
12 Kuwala kumene kumatuluka pamaso pa Mulungu kudzadza ukulu wa mlengalenga—
13 Kuwala komwe kuli muzinthu zonse, kumene kumapereka moyo kwa zinthu zonse, amene ali lamulo limene zinthu zonse zimalamuliridwa, ngakhale mphamvu ya Mulungu amene amakhala pa mpando wachifumu wake, amene ali pachifuwa cha muyaya, amene ali pakati pa zinthu zonse.
14 Tsopano, indetu ine ndinena kwa inu, kuti kudzera mu chiwombolo chimene chidapangidwira kwa inu chabweretsedwa kuchitika chiukitso kuchokera kwa akufa.
15 Ndipo mzimu ndi thupi ndizo moyo wa munthu.
16 Ndipo chiukitso cha akufa ndicho kuwomboledwa kwa moyo.
17 Ndipo chiwombolo cha moyo chili kudzera mwa iye amene amapatsa moyo zinthu zonse, amene pachifuwa pake kwalamulidwa kuti anthu osauka ndi ofatsa a padziko lapansi adzalandira.
18 Kotero, uyenera kuyeretsedwa kuchokera ku kusalungama konse, kuti ukathe kukhala okonzekeretsedwa ku ulemelero waselestiyo;
19 Pakuti utatha kudzadza muyeso wa chilengedwe chake, udzavekedwa korona wa ulemelero, ngakhale ndi kupezeka kwa Mulungu Atate;
20 Kuti matupi amene ali a ufumu waselestiyo ukathe kukhala nawo kunthawi za nthawi; pakuti, chifukwa cha cholinga ichi chidapangidwa ndi kulengedwa, ndipo chifukwa cha cholinga ichi iwo amayeretsedwa.
21 Ndipo iwo amene sadayeretsedwe kudzera mwa lamulo limene ndapereka kwa inu, ngakhale lamulo la Khristu, akuyenera kulowa ufumu wina, ngakhale uwo wa ufumu waterestriyo, kapena uwo wa ufumu watelestiyo.
22 Pakuti iye amene samatha kutsata lamulo la ufumu waselestiyo sangakhale mu ulemelero waselestiyo.
23 Ndipo iye amene sangathe kutsatira lamulo la ufumu waterestriyo sangathe kukhala mu ulemelero wa terestriyo.
24 Ndipo iye amene sangatsatire lamulo la ufumu watelestiyo sangathe kukhala mu ulemelero watelestiyo; kotero sali woyenera ufumu wa ulemelero. Kotero, akuyenera kukhala mu ufumu umene suli ufumu wa ulemelero.
25 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, dziko lapansi limakhala muchilamulo cha ufumu waselestiyo, pakuti limadzadza muyeso wa chilengedwe chake, ndipo siliphwanya lamulo—
26 Kotero, ilo lidzapatulidwa; inde, posatengela kuti lidzafa, ilo lidzaukitsidwanso, ndipo lidzakhalabe ndi mphamvu imene ilo lidzapatsidwira kukhala moyo, ndipo olungama adzalilandira ilo.
27 Pakuti ngakhale iwo afa, iwonso adzaukanso, thupi lauzimu.
28 Iwo amene ali a mzimu wa selestiyo adzalandira thupi lomwelo lomwe lidali thupi lachibadwa; ngakhale inu mudzalandira matupi anu, ndipo ulemelero wanu udzakhala ulemelero womwewo umene matupi anu adzaukitsidwire.
29 Inu amene mwaukitsidwa ndi gawo la ulemelero waku selestiyo pamenepo adzalandira chimodzimodzi, ngakhale chidzalo.
30 Ndipo iwo amene aukitsidwa ndi gawo la ulemelero waku terestriyo adzalandira chimodzimodzi, ngakhale chidzalo.
31 Ndipo iwo amene aukitsidwa ndi gawo la ulemelero wa telestiyo pamenepo adzalandira chimodzimodzi, ngakhale chidzalo.
32 Ndipo amene atsala adzaukitsidwanso; komabe, iwo adzabweleranso ku malo awoawo, kuti akasangalale ndi zomwe iwo ali ofunitsitsa kulandira, chifukwa iwo sadafune kusangalala ndi zomwe akadatha kulandira.
33 Pakuti munthu apindulanji ngati mphatso yapatsidwa kwa iye, koma osalandira mphatsoyo? Taonani, iye sakondwera mu icho chimene chapatsidwa kwa iye, kapena kusangalala mwa iye amene ali wopereka wa mphatsoyo.
34 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, chimene chimayendetsedwa ndi lamulo chimasungidwanso ndi lamulo, ndipo chimapangidwa kukhala changwiro ndi choyeretsedwa ndi chomwecho.
35 Chimene chimaphwanya lamulo, ndipo sichitsatira lamulo, koma chimafuna kukhala lamulo kwa icho chokha, ndi kufuna kukhala mu uchimo, ndi kukhaliratu mu uchimo, sichingayeretsedwe ndi lamulo, kapena ndi chifundo, chilungamo, kapena chiweruzo. Choncho, iwo akuyenera kukhalabe azonyansa.
36 Maufumu onse ali ndi lamulo lopatsidwa;
37 Ndipo pali maufumu ambiri; pakuti palibe malo amene ali opanda ufumu; ndipo palibe ufumu umene mulibe malo, kapena waukulu kapena wochepa.
38 Ndipo ku ufumu uliwonse wapatsidwa lamulo; ndipo ku lamulo lililonse palinso malire ndi makhalidwe.
39 Zolengedwa zonse zomwe sizikhala m’makhalidwe amanewo sizingalungamitsidwe.
40 Pakuti luntha limamamatira ku luntha; nzeru imalandira nzeru; choonadi chimakumbatira choonadi; ukoma umakonda ukoma; kuunika kumamatira ku kuunika; chifundo chili nacho chifundo pa chifundo, ndipo chimadzitengera zake; chilungamo chimapitilira njira yake ndikudzitengera zake; chiweruzo chimapita patsogolo pa iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndipo amalamulira ndi kuchita zinthu zonse.
41 Iye amamvetsetsa zinthu zonse, ndipo zinthu zonse zili pamaso pake, ndipo zinthu zonse zili zomuzungulira iye; ndipo iye ali pamwamba pa zinthu zonse, ndi mu zinthu zonse, ndipo ali mwa zinthu zonse, ndipo ali wozungulira zinthu zonse; ndipo zinthu zonse zikhala mwa iye, ndi kwa iye, ngakhale Mulungu, kunthawi za nthawi.
42 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, iye wapereka lamulo kwa zinthu zonse, zimene zimayenda mu nthawi zawo ndi nyengo zawo;
43 Ndipo mayendedwe awo ndi okhazikika, ngakhale mayendedwe akumwamba ndi dziko lapansi, amene amazindikira dziko lapansi ndi mapulaneti onse.
44 Ndipo zimapatsana kuwala kwa wina ndi mzake mu nthawi zawo ndi nyengo zawo, mu mphindi zawo, mu maola awo, mu masiku awo, mu masabata awo, mu miyezi yawo, mu zaka zawo—zonsezi ndi chaka chimodzi ndi Mulungu, koma osati ndi munthu.
45 Dziko lapansi limazungulira pa mapiko ake, ndi dzuwa limapereka kuwala kwake usana, ndi mwezi umapereka kuwala kwake usiku, ndi nyenyezi nazonso zimapereka kuwala kwawo, pamene zizungulira pa mapiko awo mu ulemelero wawo, pakati pa mphamvu ya Mulungu.
46 Ndidzafanizira maufumu awa ndi chiyani, kuti mumvetsetse?
47 Taonani, onsewa ndiwo maufumu, ndipo munthu aliyense amene waona kalikonse kapena kochepa ka izi waona Mulungu akuyenda mu ukulu wake ndi mphamvu zake.
48 Ndikunena kwa inu, iye wamuona iye; komabe, iye amene adadza kwa ake omwe sadazindikiridwe.
49 Kuunikaku kumawala mumdima, ndipo mdimawo sumakuzindikira; komabe, tsiku lidzafika pamene inu mudzazindikira ngakhale Mulungu, kukhala woukitsidwa mwa iye ndi iye.
50 Pamenepo mudzazindikira kuti mudandiona, kuti ine ndine, ndi kuti ine ndine kuunika koona kumene kuli mwa inu, ndi kuti inu muli mwa ine; mwanjira ina simukadachuluka.
51 Taonani, ndidzafanizira maufumu awa ndi munthu wokhala ndi munda, ndipo iye adatumiza akapolo ake kumunda kukakumba m’munda.
52 Ndipo adati kwa woyamba: Pita ndikukagwira ntchito m’munda, ndipo ola loyamba ndidzabwera kwa iwe, ndipo udzaona chisangalalo cha nkhope yanga.
53 Ndipo adati kwa wachiwiri: Pita iwenso kumunda, ndipo ola lachiwiri ndidzakuyendera ndi chisangalalo cha nkhope yanga.
54 Ndiponso kwa wachitatu, nati: Ndidzakuyendera iwe;
55 Ndipo kwa wachinayi, ndipo mpaka wakhumi ndi chiwiri.
56 Ndipo mbuye wa mundawo adapita kwa woyamba pa ola loyamba, ndi kukhala naye nthawi yonseyo, ndipo adakondwera ndi kuwala kwa nkhope ya mbuye wake.
57 Ndipo pamenepo adachoka kwa woyambayo kuti akayendere wachiwirinso, ndi wachitatu, ndi wachinayi, ndipo mpaka wakhumi ndi chiwiri.
58 Ndipo kotero iwo onse adalandira kuwala kwa nkhope ya mbuye wawo, munthu aliyense mu ola lake, ndi mu nthawi yake, ndi mu nyengo yake—
59 Kuyambira pa woyamba, ndi mpaka kufikira wotsiriza, ndi wotsiriza kufikira woyamba, ndi woyamba kufikira wotsiriza;
60 Munthu aliyense mudongosolo lake la iye yekha, kufikira ola yake idatha, ngakhale monga mbuye wake adamulamula iye, kuti mbuye wake akalemekezedwe mwa iye, ndi iye mwa mbuye wake, kuti onse akalemekezedwe.
61 Kotero, kwa fanizo ili ndidzafanizitsa maufumu onse awa, ndi okhalamo ake—ufumu uliwonse mu ola lake, ndi mu nthawi yake, ndi mu nyengo yake, ngakhale molingana ndi lamulo limene Mulungu adapanga.
62 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, anzanga, ndikusiya mawu awa ndi inu kuti mulingalire mu mitima yanu, ndi lamulo ili limene ndikupereka kwa inu, kuti mudzaitanira pa ine pamene ndili pafupi—
63 Senderani pafupi ndi ine ndipo ine ndidzasendera kufupi ndi inu; mundifufuze ine mwakhama ndipo mudzandipeza; pemphani, ndipo mudzalandira; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.
64 Chilichonse chimene mupempha Atate mu dzina langa, chidzapatsidwa kwa inu; chimene chili chabwino kwa inu;
65 Ndipo ngati mupempha chilichonse chimene sichoyenera kwa inu, chidzatembenukira ku chiweruzo chanu.
66 Taonani, icho chimene inu mukumva ndi ngati mawu a iye wofuula m’chipululu—mu chipululu, chifukwa inu simungamuone iye—mawu anga, chifukwa mawu anga ndi Mzimu; Mzimu wanga ndi choonadi; choonadi chimakhala ndipo chilibe malire; ndipo ngati chikhala mwa inu chidzakhalabe.
67 Ndipo ngati diso lanu likhala lolunjika pa ulemelero wanga, matupi anu onse adzadzadzidwa ndi kuwala, ndipo simudzakhala mdima mwa inu; ndipo thupi limene ndilodzadza ndi kuunika limazindikira zinthu zonse.
68 Kotero, dziyeretseni kuti maganizo anu akhale oyera kwa Mulungu, ndipo adzafika masiku amene mudzamuona iye; pakuti adzaonetsera nkhope yake kwa inu, ndipo kudzakhala mu nthawi yake, ndi mu njira ya iye yekha, ndi molingana ndi chifuniro chake.
69 Kumbukirani lonjezo lalikulu ndi lomaliza limene ndakulonjezani; tayani maganizo anu aulesi ndi kuseka kwanu kochuluka kutali ndi inu.
70 Yembekezani inu, yembekezani inu pamalo pano, ndipo itanani msonkhano wapadera, ngakhale wa iwo amene ali antchito oyamba mu ufumu uwu wotsiriza.
71 Ndipo aloleni iwo amene awachenjeza paulendo wawo aitanire pa Ambuye, ndipo alingalire machenjezo m’mitima mwawo amene adawalandira kwa kanthawi kochepa.
72 Taonani, ndipo onani, ndidzasamalira zoweta zanu, ndipo ndidzadzutsa akulu ndi kutumiza kwa iwo.
73 Taonani, ndidzafulumizitsa ntchito yanga m’nyengo yake;
74 Ndipo ndipereka kwa inu, amene muli antchito oyamba mu ufumu uwu wotsiriza, lamulo kuti musonkhane inu nokha, ndi kudzikonza nokha, ndi kudzikonzekeretsa, ndi kudziyeretsa nokha; inde, yeretsani mitima yanu, ndipo sambitsani manja anu ndi mapazi anu pamaso panga, kuti ndikathe kukupangani inu oyera;
75 Kuti ine ndikathe kukuchitirani umboni kwa Atate wanu, ndi Mulungu wanu, ndi Mulungu wanga, kuti inu muli oyera ku mwazi wa m’badwo woipa uwu; kuti ndikathe kukwaniritsa lonjezo ili, lonjezo lalikulu ndi lotsiriza ili, limene ine ndapanga kwa inu, pamene ine ndikufuna.
76 Ndiponso, ndikupatsani inu lamulo kuti mupitilire mu pemphero ndi kusala kudya kuyambira nthawi ino mpaka yamtsogolo.
77 Ndipo ndikupatsani inu lamulo kuti muziphunzitsana wina ndi mzake chiphunzitso cha ufumu.
78 Phunzitsani mwakhama ndipo chisomo changa chidzakhala nanu, kuti mukathe kuphunzitsidwa kokwanira bwino mu malingaliro, mu mfundo, mu chiphunzitso, m’chilamulo cha uthenga wabwino, mu zinthu zonse zokhudza ufumu wa Mulungu, zimene zili zoyenera kwa inu kuzizindikira;
79 Za zinthu zakumwamba ndi zapadziko lapansi, ndi za pansi pa dziko; zinthu zomwe zidakhalapo, zinthu zomwe zilipo, zinthu zomwe zikuyenera kuchitika posachedwa; zinthu zimene zili m’nyumba, zinthu zimene zili kunja kwa dziko; nkhondo ndi zododometsa za maiko, ndi ziweruzo zomwe zili padziko; ndi chidziwitso cha maiko ndi maufumu—
80 Kuti mukathe kukhala okonzeka mu zinthu zonse pamene ndidzakutumizaninso kuti mukakulitse maitanidwe amene ndidakuitanani; ndi ntchito ya utimiki imene ndakulamulirani.
81 Taonani, ine ndakutumizani inu kukachitira umboni ndi kuchenjeza anthu; ndipo zili kwa munthu aliyense amene wachenjezedwa kuchenjeza mnasi wake.
82 Kotero, iwo amasiyidwa opanda chowiringula, ndipo machimo awo ali pa mitu yawo.
83 Iye wondifunafuna msanga adzandipeza, ndipo sadzasiyidwa.
84 Kotero, yembekezani inu, ndipo gwirani ntchito modzipereka, kuti mukathe kukhala angwiro mu utumiki wanu kupita patsogolo pakati pa Amitundu kwa nthawi yotsiriza, onse amene mkamwa mwa Ambuye adzawatchula, kuti amange lamulo ndi kusindikiza umboni, ndi kukonzekeretsa oyera mtima kwa ola la chiweruzo chimene chilinkudza;
85 Kuti miyoyo yawo ipulumuke ku mkwiyo wa Mulungu, chipululutso cha zonyansa chimene chikuyembekezera oipa, monse m’dziko lino ndi m’dziko lilinkudza. Indetu, ndinena kwa inu, lolani iwo amene sali akulu oyamba apitilire m’munda wampesa kufikira m’kamwa mwa Ambuye mudzawaitana iwo, pakuti nthawi yawo siidafike; zovala zawo sizili zoyera ku mwazi wa m’badwo uno.
86 Khalani inu mu ufulu umene mudamasulidwa nawo; musadzikodwe ndi uchimo, koma lolani manja anu akhale oyera, kufikira akadzabwera Ambuye.
87 Pakuti si masiku ochuluka ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera ndi kugwedezeka uku ndi uko ngati munthu woledzera; ndipo dzuwa lidzabisa nkhope yake, ndi kukana kuunika; ndipo mwezi udzasambitsidwa ndi mwazi; ndipo nyenyezi zidzakwiya koopsa, ndipo zidzazigwetsa ngati mkuyu zimene zimagwa pamtengo wa mkuyu.
88 Ndipo utatha umboni wanu ukubwera mkwiyo ndi ukali pa anthu.
89 Pakuti utatha umboni wanu ukudza umboni wa zivomelezi, zimene zidzabuula pakati pake, ndipo anthu adzagwa pansi ndipo sadzatha kudzuka.
90 Ndipo pakudzabweranso umboni wa liwu la mabingu, ndi liwu la mphezi, ndi liwu la namondwe, ndi liwu la mafunde a nyanja akugwedezeka okha kuposa malire awo.
91 Ndipo zinthu zonse zidzakhala muchisokonezo; ndipo ndithudi, mitima ya anthu idzawalephera; pakuti mantha adzafika pa anthu onse.
92 Ndipo angelo adzawuluka pakati pa thambo, akufuula ndi liwu lalikulu, akuwomba lipenga la Mulungu, nati: Konzekani inu, konzekani inu okhala pa dziko lapansi; pakuti chiweruzo cha Mulungu wathu chafika. Taonani, ndipo onani, Mkwati akubwera; tulukani kukakomana naye.
93 Ndipo pomwepo padzaoneka chizindikiro chachikulu kumwamba, ndipo anthu onse adzachiona pamodzi.
94 Ndipo mngelo wina adzawomba lipenga lake, nati: Mpingo waukulu uja, mayi wa zonyansa, umene udapangitsa mafuko onse kumwa vinyo wa mkwiyo wa dama lake, amene amazunza oyera mtima a Mulungu, amene adakhetsa mwazi wawo—iye amene amakhala pa madzi ambiri, ndi pa zisumbu za nyanja—onani, iye ndi nansongole wa dziko lapansi; iye wamangidwa mitolo; zomangira zake zapangidwa zolimba, palibe munthu angathe kuzimasula; kotero, iye ali wokonzeka kuwotchedwa. Ndipo iye adzawomba lipenga lake lalitali ndi lokweza, ndipo mitundu yonse idzalimva.
95 Ndipo kudzakhala bata kumwamba kwa nthawi ya theka la ola; ndipo pomwepo chinsalu chotchinga cha kumwamba chidzafunyukulidwa, monga mpukutu ufutukulidwira ukatha kupindidwa, ndipo nkhope ya Ambuye idzavundukulidwa;
96 Ndipo oyera amene ali padziko lapansi, amene ali ndi moyo, adzasandulitsidwa ndi kukwatulidwa kukakomana naye.
97 Ndipo amene adagona m’manda mwawo adzatuluka, pakuti manda awo adzatsegulidwa; ndipo iwonso adzakwatulidwa kukakumana naye pakati pa chipilala cha kumwamba—
98 Iwo ndi a Khristu, zipatso zoyamba, iwo amene adzatsika ndi iye poyamba, ndi iwo amene ali padziko ndi m’manda awo, amene adayamba kukwatulidwa kukakomana naye; ndipo zonsezi ndi liwu la kulira kwa lipenga la mngelo wa Mulungu.
99 Ndipo zikadzatha izi mngelo wina adzawomba, lomwe lili lipenga lachiwiri; ndipo pamenepo pakudza chiwombolo cha iwo amene ali a Khristu pa kudza kwake; amene alandira gawo lawo m’ndende ija imene idakonzedwera iwo, kuti akathe kulandira uthenga wabwino, ndi kuweruzidwa monga mwa anthu mu thupi.
100 Ndiponso, lipenga lina lidzawomba, limene lili lipenga lachitatu; ndipo kenako idzabwera mizimu ya anthu yomwe ikuyenera kuweruzidwa, ndipo idzapezedwa pansi pa chiweruzo;
101 Ndipo akufa otsalawo ndi awa; ndipo sadzakhalanso ndi moyo kufikira zaka chikwi zidzathe, ngakhalenso, kufikira malekezero a dziko lapansi.
102 Ndipo lipenga lina lidzalira, limene lili lipenga lachinayi, nati: Apezeka mwa iwo amene atsala kufikira tsiku lalikulu ndi lotsirizalo, ngakhale mapeto, amene adzakhala onyansabe.
103 Ndipo lipenga lina lidzalira, limene lili lipenga lachisanu, amene ali mngelo wachisanu amene amachita uthenga wabwino wosatha—akuwuluka pakati pa thambo, kwa maiko onse, mafuko, manenedwe, ndi anthu;
104 Ndipo ili lidzakhala liwu la lipenga lake, kunena kwa anthu onse, konse kumwamba ndi padziko lapansi, ndi amene ali pansi pa dziko lapansi—pakuti makutu onse adzamva, ndipo bondo lililonse lidzagwada, ndipo lilime lililonse lidzavomereza, pamene iwo akumva kulira kwa lipenga, kuti: Opani Mulungu, ndipo perekani ulemelero kwa iye amene akhala pa mpando wachifumu, kunthawi za nthawi; pakuti yafika nthawi ya chiweruzo chake.
105 Ndiponso, mngelo wina adzawomba lipenga lake, amene ali mngelo wachisanu ndi chimodzi, nati: Wagwa amene adamwetsa mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa dama lake; wagwa, wagwa!
106 Ndiponso, mngelo wina adzawomba lipenga lake, amene ali mngelo wachisanu ndi chiwiri, nati: Kwatha; kwatha! Mwana wa Nkhosa wa Mulungu wagonjetsa ndi kupondereza mopondera mpesa yekha, ngakhale moponderamo mpesa wa mkwiyo waukali wa Mulungu Wamphamvu zonse.
107 Ndipo pamenepo angelo adzavekedwa korona wa ulemelero wa mphamvu yake, ndipo oyera mtima adzadzazidwa ndi ulemelero wake, ndi kudzalandira cholowa chawo, nadzalingana naye.
108 Ndipo pamenepo mngelo woyamba adzaombanso lipenga lake m’makutu a amoyo onse, ndipo adzaulula machitachita achinsinsi a anthu, ndi ntchito zamphamvu za Mulungu mu zaka chikwi zoyamba.
109 Ndipo pamenepo mngelo wachiwiri adzawomba lipenga lake, ndipo adzavumbulutsa zochitika zachinsinsi za anthu, ndi maganizo ndi zolinga za mitima yawo, ndi ntchito zazikulu za Mulungu mu zaka chikwi chachiwiri—
110 Ndi zina zotero, mpaka mngelo wachisanu ndi chiwiri adzawomba lipenga lake; ndipo adzaimilira pa dziko ndi pa nyanja, ndipo adzalumbira m’dzina la iye wokhala pa mpando wachifumu, kuti sipadzakhalanso nthawi; ndipo Satana adzamangidwa, njoka yakaleyo, iye wotchedwa mdyerekezi, ndipo sadzamasulidwa kwa nthawi ya zaka chikwi.
111 Ndipo pamenepo adzamasulidwa kwa kanthawi, kuti akathe kusonkhanitsa ankhondo ake.
112 Ndipo Mikaeli, mngelo wachisanu ndi chiwiri, ngakhale mngelo wamkulu, adzasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake, ngakhale makamu a kumwamba.
113 Ndipo mdyerekezi adzasonkhanitsa ankhondo ake; ngakhale makamu a gahena, ndipo adzabwera kudzamenyana ndi Mikaeli ndi ankhondo ake.
114 Ndipo pamenepo pakubwera nkhondo ya Mulungu wamkulu; ndipo mdyerekezi ndi ankhondo ake adzaponyedwa kutali ku malo awo omwe, kuti iwo sadzakhala ndi mphamvu pa oyera mtima konse.
115 Pakuti Mikaeli adzamenya nkhondo zawo, ndipo adzagonjetsa iye amene akufunafuna mpando wachifumu wa iye amene akhala pa mpando wachifumu, ngakhale Mwana wa nkhosa.
116 Uwu ndi ulemelero wa Mulungu, ndi woyeretsedwayo; ndipo iwo sadzaonanso imfa.
117 Kotero, indetu ndinena kwa inu, anzanga, itanani msonkhano wanu wapadera, monga ine ndakulamulirani inu.
118 Ndipo monga onse alibe chikhulupiliro, funafunani inu molimbika ndi kuphunzitsana wina ndi mzake mawu a nzeru; inde, funafunani inu m’mabuku abwino koposa mawu a nzeru; funafunani kuphunzira, ngakhale mwa kuphunzira komanso mwa chikhulupiliro.
119 Dzikonzeni nokha; konzani zinthu zonse zofunika; ndi kukhazikitsa nyumba, ngakhale nyumba ya pemphero, nyumba ya kusala kudya, nyumba ya chikhulupiliro, nyumba ya maphunziro, nyumba ya ulemelero, nyumba ya dongosolo, nyumba ya Mulungu;
120 Kuti kulowa kwanu kukathe kukhala mu dzina la Ambuye; kuti kutuluka kwanu kukathe kukhala mu dzina la Ambuye; kuti malonje anu onse akathe kukhala mu dzina la Ambuye, ndi manja okwezedwa kwa Wam’mwambamwamba.
121 Kotero, lekani zoyankhula zanu zonse zopepuka, ku kuseka konse, ku zilakolako zanu zonse, ku kunyada kwanu konse ndi kuganiza kopelewela, ndi zoipa zanu zonse.
122 Mudziikire mphunzitsi, ndipo musakhale mukuyankhula nonse pamodzi; koma lolani m’modzi ayankhule pa nthawi, ndipo lolani onse amvetsere ku zonena zake, kuti pamene onse ayankhula kuti onse akathe kulimbikitsidwa ndi onse, ndi kuti munthu aliyense akathe kukhala ndi mwayi wofanana.
123 Onani kuti mukukondana wina ndi mzake; lekani kusilira; phunzirani kugawirana wina ndi mzake monga umafunira uthenga wabwino.
124 Lekani kukhala aulesi; lekani kukhala wodetsedwa; lekani kupezerana zifukwa wina ndi nzake; lekani kugona nthawi yayitali kuposa yofunikira; pitani kukagona msanga, kuti mukathe kukhala osatopa; dzukani msanga, kuti matupi anu ndi maganizo anu akhale olimbikitsidwa.
125 Ndipo koposa zonse valani chomangira cha chikondi, monga chovala, chimene chili chomangira cha ungwiro ndi mtendere.
126 Pempherani nthawi zonse, kuti musakathe kufooka, kufikira nditabwera. Taonani, ndipo onani, ndidza msanga, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha. Ameni.
127 Ndiponso, dongosolo la nyumba yokonzedwera atsogoleri a sukulu ya aneneri, yokhazikitsidwa kwa malangizo awo mu zinthu zonse zimene zili zoyenera kwa iwo, ngakhale kwa adindo onse a mpingo, kapena m’mawu ena, iwo amene aitanidwa ku utumiki mu mpingo, kuyambira pa ansembe aakulu, ngakhale mpaka kwa madikoni—
128 Ndipo ili lidzakhala dongosolo la nyumba ya atsogoleri a sukulu: Iye amene asankhidwa kukhala mtsogoleri, kapena mphunzitsi, adzapezeka ataima m’malo mwake, m’nyumba yomwe idzakonzedwera iye.
129 Kotero, iye adzakhala woyamba m’nyumba ya Mulungu, pamalo amene mpingo m’nyumbamo ungathe kumva mawu ake mosamalitsa ndi momveka bwino, osati ndi mawu okuwa.
130 Ndipo pamene iye afika m’nyumba ya Mulungu, pakuti iye akuyenera kukhala woyamba m’nyumba—onani, ichi ndi chokongola, kuti iye akathe kukhala chitsanzo—
131 Adzipereke yekha mu pemphero pa maondo ake pamaso pa Mulungu, mu chizindikiro kapena chikumbukiro cha pangano losatha.
132 Ndipo pamene wina adzalowa pambuyo pake, lolani aimilire mphunzitsi, ndipo, ndi manja ake okwezera kumwamba, inde, ngakhale molunjika, ayankhule m’bale wake kapena abale ndi mawu awa:
133 Kodi ndinu m’bale kapena abale? Ndikukupatsani moni m’dzina la Ambuye Yesu Khristu, m’chizindikiro kapena chikumbukiro cha pangano losatha, m’menemo ndimakulandirani inu ku chiyanjano, m’chitsimikizo chokhazikika, chosasunthika, ndi chosasinthika, kukhala bwenzi lanu ndi m’bale wanu kudzera mu chisomo cha Mulungu mu zomangira za chikondi, kuyenda m’malamulo onse a Mulungu opanda banga, mu chiyamiko kunthawi za nthawi. Ameni.
134 Ndipo iye amene adzapezedwa wosayenera ku malonje amenewa sadzapatsidwa malo mwa inu; pakuti simudzalola kuti nyumba yanga iipitsidwe ndi iye.
135 Ndipo iye amene alowa ndi kukhala wokhulupirika pamaso panga, ndipo ndi m’bale, kapena ngati ali abale, adzapereka moni kwa mtsogoleri kapena mphunzitsi ndi manja okwezera kumwamba, ndi pemphero lomweli ndi pangano, kapena pakunena Amen, mu chizindikiro cha chomwecho.
136 Taonani, indetu, ndinena kwa inu, ichi ndi chitsanzo kwa inu cha moni kwa wina ndi mzake m’nyumba ya Mulungu, mu sukulu ya aneneri.
137 Ndipo mwaitanidwa kuchita ichi ndi pemphero ndi chiyamiko, monga Mzimu adzayankhula mu zochita zanu zonse mu nyumba ya Ambuye, mu sukulu ya aneneri, kuti ikathe kukhala malo opatulika, chihema cha Mzimu Woyera kuchilimbikitso chanu.
138 Ndipo simudzalandira wina wa inu ku sukulu iyi, kupatula ali woyera ku mwazi wa m’badwo uno;
139 Ndipo adzalandiridwa ndi mwambo wa kutsuka mapazi, pakuti kwa ichi mwambo wa kutsuka mapazi udakhazikitsidwa.
140 Ndiponso, mwambo wa kutsuka mapazi ukuyenera kuyendetsedwa ndi mtsogoleri, kapena mkulu wotsogolera wa mpingo.
141 Ukuyenera kuyambika ndi pemphero; ndipo pambuyo pa kudya mkate ndi vinyo, iye akuyenera kudzimanga m’chuuno mogwirizana ndi chitsanzo choperekedwa mu mutu wakhumi ndi chitatu wa umboni wa Yohane chokhudzana ndi ine. Ameni.