Gawo 89
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Feburuwale 27, 1833. Ngati zotsatira za abale oyambilira kugwiritsa ntchito fodya mu misonkhano yawo, ndi powuzidwa ndi mkazi wake, Emma Smith, Mneneri adafunsa Ambuye zokhudza ichi. Vumbulutso ili, lodziwika kuti Mawu a Nzeru, lidali lotsatira lake.
1–9, Kugwiritsa ntchito vinyo, zokumwa zaukali, fodya, ndi zokumwa zotentha kuletsedwa; 10–17, Zitsamba, zipatso, nyama, ndi mbewu ndizopatulidwa kuti zigwiritsidwe ntchito ndi munthu ndi zinyama; 18–21, Kumvera lamulo la uthenga wabwino, kuphatikizapo Mawu a Nzeru, kumabweretsa madalitso akuthupi ndi ku uzimu.
1 Liwu la Nzeru, lopindulitsa kwa bungwe la ansembe aakulu, okumana ku Kirtland, ndi mpingo, ndiponso oyera mtima mu Ziyoni—
2 Kutumiziridwa moni; osati mwa lamulo kapena chopinga, koma mwa vumbulutso ndi mawu a nzeru, kuonetsa dongosolo ndi chifuniro cha Mulungu mu chipulumutso cha thupi la oyera mtima onse mu masiku omaliza—
3Â Kuperekedwa pa mfundo yokhala ndi lonjezo, kutengera kuthekera kwa ofooka ndi ofooketsetsa mwa oyera mtima onse, amene ali kapena angathe kutchulidwa oyera mtima.
4 Taonani, indetu, akutero Ambuye kwa inu: Mu zotsatira za zoipa ndi madongosolo amene ali ndipo adzakhalabe mu mitima ya anthu achiwembu mu masiku omaliza, ndakuchenjezani inu, ndi kukuchenjezeranitu, popereka kwa inu mawu a nzeruwa mwa vumbulutso—
5Â Kuti pamene munthu aliyense amwa vinyo kapena chakumwa chaukali pakati panu, taonani ichi si chabwino, kapena choyenera pamaso pa Atate anu, koma posonkhana nokha pamodzi kupereka masacramenti pamaso pake basi.
6Â Ndipo, taonani, uyu akuyenera kukhala vinyo, inde, vinyo weniweni wa chipatso cha mpesa, mwa kupanga kwanokha.
7 Ndiponso, chakumwa chaukali sichoyenera m’mimba, koma potsukira matupi anu.
8 Ndiponso, fodya siwoyenera kuthupi, kapena m’mimba, ndipo siwabwino kwa munthu, koma ndi mankhwala a zilonda, ndi ng’ombe zodwala, kukagwiritsidwa ntchito mwanzeru ndi luso.
9 Ndiponso, zokumwa zotentha sizathupi kapena m’mimba.
10 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, zitsamba zabwino zonse Mulungu wazipatula pa chilamulo chakayendetsedwe, chilengedwe ndi kagwiritsidwe ka munthu—
11Â Zitsamba zilizonse mu nyengo yake, ndi chipatso chilichonse mu nyengo yake; zonsezi kuti zigwiritsidwe mwanzeru ndi chiyamiko.
12Â Inde, nyamanso ya zilombo ndi mbalame za mlengalenga, ine, Ambuye, ndazipatula pa kagwiritsidwe ka munthu ndi chiyamiko; komabe zikuyenera kugwiritsidwa ntchito mosamala;
13Â Ndipo ndizokondweretsa kwa ine kuti zisamagwiritsidwe, pokhapokha mu nthawi ya dzinja, kapena yozizira, kapena chilala.
14Â Mbewu zonse zapatulidwa kuti zigwiritsidwe ndi munthu kapena zinyama, kukakhala chakudya ya moyo, osati kwa munthu yekha komanso kwa zinyama za kuthengo ndi mbalame za mlengalenga, ndi zinyama zomwe zimathamanga ndi kukwawa pa dziko lapansi;
15Â Ndipo zinthu izi Mulungu adazipanga kuti zigwiritsidwe ntchito ndi munthu munthawi ya chilala yokha ndi kuchuluka kwa njala.
16 Mbewu zonse ndi zabwino kuchakudya cha munthu; monganso chipatso cha mpesa; chomwe chimabeleka chipatso, kaya pansi pa nthaka kapena pamwamba pa nthaka—
17 Komabe, tiligu kwa munthu, ndi chimanga ku ng’ombe, ndi mapila kwa kavalo, mchewere kwa mbalame ndi nkhumba, ndi zinyama zonse zam’munda, ndi balere kwa zinyama zonse zogwiritsidwa ntchito, ndi kupangira zakumwa zosaledzeretsa, ndiponso mbewu zina.
18 Ndipo oyera mtima onse amene akumbukira kusunga ndi kuchita zonenedwa izi, kuyenda mu kumvera kwa malamulo, adzalandira thanzi mu mchombo mwawo ndi mafuta a m’mafupa mu mafupa awo;
19Â Ndipo adzapeza nzeru ndi chuma chochuluka cha chidziwitso, ngakhale chuma chobisika;
20Â Ndipo adzathamanga koma sadzatopa, ndipo adzayenda koma osafooka.
21Â Ndipo ine, Ambuye, ndikupereka kwa iwo lonjezo, kuti mngelo owononga adzawadutsa, monga ana a Israeli, ndipo sadzawapha iwo. Ameni.