Gawo 40
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Fayette, New York, January 6, 1831. Kutsogola zolemba za vumbulutsoli, mbiri ya Mneneri ikuti, “Monga James [Covel] adakana mawu a Ambuye, ndikubwelera ku mfundo zake zakale ndi anthu, Ambuye adapereka kwa ine ndi Sidney Rigdon vumbulutso lotsatirali” (onani gawo 36).
1–3, Kuopa chizunzo ndi kusamalira za dziko zimayambitsa kukana uthenga wabwino.
1 Taonani, inde ine ndinena kwa inu, kuti ntima wa mtumiki wanga James Covel udali wolungama pamaso panga, pakuti adapanga pangano ndi ine kuti adzamvera mawu anga.
2 Ndipo adalandira mawuwo mokondwera, koma pomwepo adamuyesa Satana; ndipo kuopa mazunzo ndi kusamalira za dziko zidampangitsa kukana mawu.
3 Kotero adaphwanya pangano langa, ndipo zikhala ndi ine kumuchitira iye monga ndikufunira ine. Ameni.