Mutu 53
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Algernon Sidney Gilbert, ku Kirtland, Ohio, Juni 8, 1831. Pa pempho la Sidney Gilbert, Mneneri adafunsa kwa Ambuye za ntchito ndi kusankhidwa kwa m’bale Gilbert mu Mpingo.
1–3, maitanidwe ndi kusankhidwa kwa Sidney Gilbert mu Mpingo ndi kokuti adzodzedwe kukhala mkulu; 4–7, Iye akuyeneranso kutumikira monga nthandizi wa bishopu.
1 Taona, ndikunena kwa iwe, mtumiki wanga Sidney Gilbert, kuti ndamva mapemphero ako; ndipo iwe waitanira pa ine kuti chidziwitsidwe kwa iwe, mwa Ambuye Mulungu wako, zokhudzana ndi maitanidwe ndi kusankhidwa kwako mu mpingo, umene ine, Ambuye, ndaudzutsa m’masiku otsiriza ano.
2 Taona, ine, Ambuye, amene ndidapachikidwa chifukwa cha machimo a dziko lapansi, ndikupereka kwa iwe lamulo kuti usiye za m’dziko lapansi.
3 Udzitengere pa iwe kudzodza kwanga, ngakhale uko kokhala mkulu, kukalalikira chikhulupiliro ndi kulapa ndi chikhulukiro cha machimo, molingana ndi mawu anga, ndi kulandira kwa Mzimu Woyera mwa kusanjia kwa manja;
4 Ndiponso kukhakhala nthumwi ku mpingo uwu mu malo amene adzasankhidwe ndi bishopu, molingana ndi malamulo amene ine ndidzapereke mtsogolo muno.
5 Ndiponso, indetu ndikunena kwa iwe, ukayambe ulendo wako ndi mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon.
6 Taona, iyi ndi miyambo yoyambilira imene iwe udzalandira; ndipo yotsalirayo idzadziwitsidwa mu nthawi ili nkudza, molingana ndi magwiridwe antchito yako mu munda wanga wampesa.
7 Ndiponso, ndikufuna kuti iwe uphunzire kuti iye yekha amene amapulumutsidwa ndi amene amapilira kufikira chimaliziro. Ngakhale choncho. Ameni.