Gawo 2
Zolemba zochokera ku mbiri ya Joseph Smith zokhudza mawu a mngelo Moroni kwa Mneneri Joseph Smith, ali m’nyumba ya mitengo ya a Smith ku Palmyra, New York, madzulo a Seputembala 21, 1823. Moroni adali womaliza pa mndandanda wautali wa olemba mbiri omwe adapanga zolemba zomwe tsopano zili padziko lapansi ngati Buku la Mormoni. (Fananitsani Malaki 4:5–6; ndiponsogawo 27:9;110:13–16; ndi128:18.)
1, Eliya ayenera kuvumbulutsa unsembe; 2–3, Malonjezo a makolo abzalidwa m’mitima ya ana.
1 Taonani, ndidzaulura kwa inu Unsembe, ndi dzanja la Eliya mneneri, lisadadze tsiku lalikulu ndi lowopsya la Ambuye.
2 Ndipo iye adzabzala m’mitima ya ana malonjezano opangidwa kwa makolo, ndipo mitima ya ana idzatembenukira kwa makolo awo.
3 Ngati sikudali choncho, dziko lonse lapansi lidzawonongedwa kotheratu pakudza kwake.